Moto Salumpha

Moto Salumpha Nkhani Zochita ndi Amalawi komanso m'madera wena Ozungulira. Entertainment | Politics | Business | History I

07/09/2026

JB . . . .

23/08/2026

Nsambiii. Ufiti . Utchisi . Nkhanza . Nsanje ati kuonesa m'kwiyo kuti sakufuna ma foreigner dziko lako . Aii zikomo

Rest in Peace Sir
08/08/2026

Rest in Peace Sir

Ndiye Munthu ukalimbe mtima osaopa chitedze kuti chikuyabwa m'malo mwake nkumachikolola nkumakadya .Dzikoli ndilokondera...
21/07/2026

Ndiye Munthu ukalimbe mtima osaopa chitedze kuti chikuyabwa m'malo mwake nkumachikolola nkumakadya .

Dzikoli ndilokondera ndithu .

21/07/2026

M'malawi akapita ku-Joni amaiwala chomwe anapitira , nchifukwa chake apita pama bus aulele aja ayambiranso kubwera kenolako akomedwanso .

Chifukwa kukhala kuti zili bwino ku malawiko there's no way kuti uzibwelerakonso kumenene wathamangitsidwa .

Mwina tuganizo udyo enafe , mulomoyu utipalamulisa ๐Ÿ˜…๐Ÿ˜…

19/07/2026

Tamverani ndipo mumveleso mpaka mumvesese , mukatero share or SAVE post .

Mulungu amapanga njira popanda njira , kumalimbikira ntchito chifukwa sabwera khomo ndi khomo kuzagawa ndalama ndi ntchi...
19/07/2026

Mulungu amapanga njira popanda njira , kumalimbikira ntchito chifukwa sabwera khomo ndi khomo kuzagawa ndalama ndi ntchito .

Pempherani kosalekeza , khulupilirani ndipo pemphani muzapasidwa .

Mavuto , Umphawi ndi kuthodwa ndizosakhalisa ndipo kucha .

"you cannot unlock a new door if your hands are full of old keys."
18/07/2026

"you cannot unlock a new door if your hands are full of old keys."

18/07/2026

Happy 86th Birthday ๐Ÿฅณ Mr President of the Republic of Malawi , Professor Arthur Peter Mutharika .

"MUKAWAUZE KUMUDZIKO KUTI NDIKUPULUMUKIRA MANGOWA KUDIMBA KUNO NDIYE MUSAMALIZEMO..."Amenewa anali mawu afupi, koma olem...
18/07/2026

"MUKAWAUZE KUMUDZIKO KUTI NDIKUPULUMUKIRA MANGOWA KUDIMBA KUNO NDIYE MUSAMALIZEMO..."
Amenewa anali mawu afupi, koma olemera ndi ululu. Atangowanena, maso ake anayamba kutseka pang'onopang'ono, mpweya wake unayamba kuchepa, ndipo patangopita mphindi zochepa anapuma komaliza.
Anthu onse amene anali pafupi anangoyamba kulira chifukwa sanamvetse tanthauzo la mawu ake.

Patapita masiku ochepa, anthu a m'banja anayamba kukumbukira kuti nthawi zambiri ankadandaula kuti usiku akamalota amangoona anthu akumuthamangitsa kupita kumunda wina, ndipo ankadzuka ali ndi mantha kwambiri. Koma palibe amene anaganiza kuti zimene ankafotokozazo zinali zomuvutitsa kwambiri m'maganizo mwake.

Tsiku la maliro linafika. Misozi inali yosatha. Mayi ake ankangolira mokweza, "Mwana wanga, unandisiya chifukwa chiyani? Kodi unafuna kundiuza chiyani pa mawu ako omaliza?"

Abambo ake anangokhala chete, maso awo odzaza ndi misonzi. Ana aang'ono a m'banjamo sankamvetsa chifukwa chake munthu amene ankasewera nawo tsiku lililonse sanadzukenso.

Mpando wake unatsala wopanda munthu. Chipinda chake chinangokhala chete. Zovala zake zinali pomwepo, koma mwini wake sanabwerenso.

Panatha miyezi ingapo anthu akupeza zolemba kudimba "MUKAWAUZE KUMUDZIKO KUTI NDIKUPULUMUKIRA MANGOWA KUDIMBA KUNO NDIYE MUSAMALIZEMO..." ndipo anthu am'mudzi anasiya kudya mango amtengo uliwonse mpaka tsiku ndi tsiku mango amachepa mpaka nkufika pokutha onse . Ndipo tsiku lina mango onse atatha anaitanisa nsima yamazira ndipo anthu akubanja anaphikadi ndikupitisa kudimba atavindikira bwino ndipo pobwera m'mawa lake anapeza zakudya zonse zadyedwa mbalenso zavindikiridwa . Ulendo omaliza unali omweyo mpaka pano kuli ziiii kungoti chete ngati bodza.

Nthawi zina imfa imasiya mafunso ambiri kuposa mayankho. Mawu omaliza a munthu amatha kukhala chinsinsi chimene chimakhala m'mitima ya achibale moyo wawo wonse.
Choncho tisamachedwetse kusonyeza chikondi kwa anthu athu.

Tiyeni tizikondana, tizikhululukirana, ndi kupemphererana chifukwa sitikudziwa tsiku kapena nthawi imene tidzanene mawu athu omaliza.

"Pakuti munthu aliyense ali ngati nthunzi; amaoneka kanthawi, kenako n'kusowa."
Moyo ndi waufupi. Konda banja lako, lemekeza anzako, ndipo khala wokonzeka nthawi zonse, chifukwa mawa silinalonjezedwe kwa aliyense. ๐Ÿ’”๐Ÿ˜ญ

Based on true story ! Moto Salumpha

Address

Marble Towers
Johannesburg

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Moto Salumpha posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share