12/06/2026
RONWEN WILLIAMS goalkeeper wa South Africa wadandawula kuti maiko aku Africa sanawapatse sapoti.
Tankhetsa misozi kuwona abale athu aku Africa akuspota Mexico.
Kugonjetsedwa kwathu lero sikunali chifukwa choti sitinayesetse kwambiri. Ndikukhulupirira kuti kusowa kwa thandizo kuchokera kwa anthu ena aku Africa kunathandizanso.
Africa ndi kontinenti yomwe nthawi zonse ndakhala ndikudziwa kuti imathandiza ndi kuyimirira limodzi ndi matimu ake pa World Cup kapena mipikisano yapadziko lonse, koma kwa ife zinamveka ngati zinthu zinali zosiyana.
Mβmalo mokhala ogwirizana, kugonjetsedwa kwathu kukuoneka ngati kwasangalatsa anthu ena, ngakhale ena omwe ali mu Africa. Zimenezi zinatikhumudwitsa, chifukwa tinkayembekezera kuti kontinenti yathu idzakhala nafe nthawi ngati izi.β
Maiko ambiri aku Africa sakuyisapota South Africa chifukwa Cha nkhaza zomwe akuchitila anthu amayiko ena ku South Africa.
South Africa yagonja 2-0 ndi Mexico usiku wapitawu.