Rumors - mphekesera mw

Rumors - mphekesera mw to inform about recent events

kokawona mzawo yemwe anakana kukhwima
04/22/2026

kokawona mzawo yemwe anakana kukhwima

mtembo wa President wakale wa Zambia, omwe ukuthamangila pafupifupi chaka usanalowe mmanda chifukwa cha kusanvana kwa bo...
04/22/2026

mtembo wa President wakale wa Zambia, omwe ukuthamangila pafupifupi chaka usanalowe mmanda chifukwa cha kusanvana kwa boma ndi akubanja zikunveka kuti wasowa ku motchale 🥲😭

11/09/2025

Tengani ka ngongole ka emergency ku KwachaHelper
Imalowa ku mpamba kapena Airtel money
Ilibe chikole
Zofunika ndi ma number awili a mboni ndi ID yako
pangani apply http://kwachahelper.com/vip/?s=2b2d.1b144

10/06/2025

08/18/2025

Mayeso a standard 8 komaso jce atuluka congratulations kwa okhoza

08/12/2025



Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi amenenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Odya Zake alibe mlandu wati sangapepese pa zimene akunena kuti m'boma muli atsogoleri amene akuchita katangale.
Wofalitsa nkhani za chipani cha MCP a Jessie Kabwila kummawaku anati a Usi akapereke umboni ku bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la ACB kuti m'boma muli anthu ochita katangale ndi ziphuphu kapena apo atule pansi udindo wawo kaamba konyozetsa boma limene akupindula nalo.

Koma poyankha izi pa msonkhano woimaima ku Ulongwe m'boma la Balaka, a Usi ati iwo akudziwa anthu omwe akuchita za katangalezi koma sangawatchule pagulu kuopa kuwasumira ku khothi.

Iwo afunsa kuti ndi chifukwa chani omanga komanso ozenga anthu milandu sakuwapeza kuti awauze anthu amene akuchita mchitidwewu.

"Apolisi ndi a ACB sakundifunsa bwanji kuti ndiwatchule kuti mukawamange? Amene amamanga anthu andipeze ndiwauze omwe apanga za katangale. Ine sindingabwere pano kumangotchuoa maina a anthu pachabe," atero a Usi.

Woyankhulapo pa nkhani za ndale a George Chaima wati ndikofunika kuti Amalawi athandizire kupereka umboni ku ACB kuti onse ochita katangale awamange ngakhale anafulumira kunena kuti bungwe la ACB pakadali pano liribe mphamvu kwenikweni zomanga anthu kaamba ka momwe akuluakulu ake akuliyendetsera.

08/12/2025



Uthenga kwa Okhulupilila amipingo Ku Malawi
Mtendere ukhale nanu

Nyanja ya Galileya ija anayendapo Ambuye wathu Yesu madzi Ake asanduka ofila ngati mwazi monga munthawi ya mose pa Ekisodo 7

Izi zachitika kuyambila pa 7 Mwezi Uno wa August chaka cha 2025

Tikumbukile kuti Mau amatiuza kuti mwana wamunthu akakhala pafupi kubwera ma warning ngati awa amene anachitikanso nthawi ya mose azapelekedwa.

A science anena kuti ndi climate change koma Kwa Tonse Okhulupilila tikumbukile mau mu Bukhu la Chibvumbulunso makamaka kuyambila 16 kumapita mumunsi komanso Chipangano chatsopano chimene chimakamba motsindika za masiku osilza monga

Nkhondo, zivomerezi, Mtundu kuukilana, Aneneri onyenga kuchuluka komanso zizindikilo pa nyanja .

Anthu achikunja uthengau ulibe ntchito kwa Iwo , aseka ndikunyogodola koma Iwe ndi ine zitipangise kulapa nsanga .

08/12/2025



Apolisi m'boma la Phalombe amanga mnyamata wa zaka 18 pomuganizira kuti wagwilira ndikupha nsuwani wake wa zaka zisanu.

Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi m'bomali, a Marco Mvukuta, wati mnyamatayu ndi Vincent Tawombe wa m'mudzi wa Nanyalo mfumu yayikulu Nkhulambe m'bomalo.

A Mvukuta ati malemuyu wakhala akupita ku nyumba ya mnyamatayu yomwe iri pafupi ndi ya makolo ake kukacheza koma atapita pa tsikuli sanabwelerenso.

Iwo ati mayi a mwanayu anapita kunyumba ya mnyamatayo koma atatsegula anapeza msungwanayu ali mbulanda komanso atafa.

Malinga ndi wachiwiri kwa mkulu wa apolisiyu, zotsatira za chipatala zaonetsa kuti mwanayu anagwiliridwa kenako ndikumupha pomukanyanga pakhosi.

😭

Malawi Elections Updates Mwadzuka bwanji AmalawiRegistrar olembesa zipani mumalawi walamula President Chakwera ndi MCP k...
08/07/2025

Malawi Elections Updates
Mwadzuka bwanji Amalawi

Registrar olembesa zipani mumalawi walamula President Chakwera ndi MCP kuti asiye kugawa ndalama pa campaign

Malamulo amalesa kugawa ndalama kapena zinthu zokopa anthu pa campaign. Akapitiliza Registrar kuzera Ku court atha kupanga disqualify candidate ndi Chipani kuti asapikisane nao

Tikhoza kusimikiza kuti Maheu Aja basi samwedwanso

MALAWI ELECTIONS UPDATES MEC yatulusa  official confirmed list ya ma President apikisane Zisankho pa 16 September. Awa n...
08/06/2025

MALAWI ELECTIONS UPDATES

MEC yatulusa official confirmed list ya ma President apikisane Zisankho pa 16 September. Awa ndi ovomelezeka.

Address

New York City
New York, NY
00000

Telephone

+265896068702

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Rumors - mphekesera mw posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Establishment

Send a message to Rumors - mphekesera mw:

Shortcuts

Share