Ndakatulo za luntha

Ndakatulo za luntha To promote the African identity and culture through poems and promoting poets

Congratulations to you beans Raphael SitimaToday you are responsible man sangalani kuti mwalowa m'banjaLangizo banja ndi...
06/07/2025

Congratulations to you beans Raphael Sitima
Today you are responsible man sangalani kuti mwalowa m'banja
Langizo banja ndi ulendo ndipo mukumana ndizambiri.Zabwino,zowawa, myozo,kusanvana,kusphana zichewa.
Ndilipo mwana padali nkuluwina aniakonda nyimbo izi polanga ukwati
1.ukugugu ukugugu wadya nsima ya mwana osasamba mmanja
2.kapilire kunkaiweko kapilire kunkaiweko
Kumeneko kuli ana eee kumeneko kuli ana eee osasamba eee amanthongo eeeee kapilire kunkaiweko
Mmagsnizo mwanga ndinkaona ngati anawo ndi
eni eni amoyo koma ayi ndithu adali mavuto am'banja
3.nankholowa watamba tamba kusaukira utundu nyimbo zomwe inenso ndikufuna kuti munvemo malangizowo sanakusankhireni
Kamukondeni moyo wanuonse nyimbo ikhale ya Lucioas Banda ft.san b Kennedy

01/07/2025

Tinagokhuta chabe
Mwina udalikhuto
Tikuewa koohwetsera
Mmanja phuu mfiti tidaombera
Tikadadziwa sitikadaoanga

Tidaledzera ndi ufulu
Popusitsika ndi atsogoleri
Zikopa zankhosa atavala
Mumbulu idalidi eti
Alikuti lero biyeni aja
Nyamata wadzithu jetu wathu
Adakatisiya kuti Kodi sindende iyi

Popita kunsewu titakhuta
Lero anthu atopa ndi goli
Tikadadziwa tikadaphika therere
Mimba nchipala izi nde zanyanya
Kuk**ayonda kwati itulutse chani?
Talowadi ntchala ndithu haaaa!
Ndikunsabwera tilikuno izi nde zoona
Atatitulutse mmasanomuno ndindani?
Tagwera m'buna kunga fisi lero haaa!

Otiuza analipo koma kusanva konweku
Lero ndiuyu tikunong'oneza bondo
Adatilaniza ndithu koma kusadekha
Nkanda oyera sitidavale eti
Ndakhilupirira lero lino ndithu
Poti akulu mawu sapita pachabe
Akona akagoneradi ndadziwa lero
Chikuni chachikulu kusunga Moto
Mlera khungwa sakhala nyamata
Chomwe mudachiona mutakhala chija
Ife tinkadupha osachiona
Ena akalionera lero tikuohetsa nyani

Ndaonera momwemo ndithu
Ngwagulugufe mwambi ntheradi
Adali ndiolotse ndikakutafune?
Chisoni chidamphetsadi Biyeni
Poti mphunosalota sakadadziwa
Sufuka utsi Moto palibe
Muntimamu mwagwidwa ukapolo
Ukadakhala nthenda iweyo
Bwezi uli yooatsirana pogonana
Takutopera wanjira nsana tikuonetsa
Watsala madzi amodzi tikukuonera pakhosi
Amoyo salekana koma sudzakhalamgumunso

22/06/2025

Kuyitana mafumu ndikuwadyetsa tsikulimodzi sizokwanira pomwe
Mafumuwo akukanoka kukhala ndimoyo okondwera .
Munthu zoona akabetse voti chifukwa cha chakudya chamasana chokha chokudya kamodzi mmmmmmmh,Dzukani aphunzitsi ,Dzukani mafumu ,Dzukani achinyamata ndi amayi yambani kuona kavuto amoyowanu wa tsiku ndi nyltsiku panopo 50 sauzande kwacha sikunukha kathu olo ndi dontho nde musapuse ndi chanje chomwe iwo akukubwezerani no dalama atatenga musagulitse ukulu want ngati esau kwa jakobo ndi nsuzi omwe akupereka ku chikoko bay

20/06/2025

Welcome me back pa line after long time nkalasi munavuta

Ndadziwiranji?Ngati kutulo eti ndakwanitsadiNdikutsekulani mmimba ndithuMuvutikanane simunati mbambaMesa munadanei bonit...
06/02/2025

Ndadziwiranji?

Ngati kutulo eti ndakwanitsadi
Ndikutsekulani mmimba ndithu
Muvutikanane simunati mbamba
Mesa munadanei bonitsa kunga kamwa ndilije
Lero zathekatu suyu ndakodola kadona
Kani kutsitsa mfundo nkophweka zedi?
Kundiopseza kuja adali mantha ?
Munkaopa kuti ndikulandani kkkkk
Ndikuyabwani lero poti ndakwanitsadi
Mbendu ziwiri zagwa kale mu ukonde wanga
Samalani nane chenjezani anamwali anu
Mbendu zonse ndi myatitsa mukapusa
Nyenyezi titha yanuyo ndilandadi

Ndadziwiranji ?
Kuti maluso alipo mpweche kutapa kutaaya
Sinkadakangalika nkungo tcha mbalame
Ku sema mipini kukhoma k**a ndichitadi
Kuluka malichero mipando ndi mphasa
Ndakwanitsa samalani luso lanulo mogwiritsa
Ndi ngaku tsomphoreni ogula
Ndichanga chikoka mu malonda

Ndadziwiranji?
Mesa ndinkachedwa sizamaonekedwe
Kapena kuyhekera kungolumikizana
Kuchenjera pakamwa ndi mbalume
Aphungu anymba yamalamulo nduna
Samalani inde inu makhansala chenjezo
Landirani ndipo nsilomweri moando wanuwo
Muzindikira nditausunga mosamala
Wandale samalitsa ndikukgaulitsa
Chake chaka ndichino mukhauladi
Ndadziwiranji kuti ndale ndimasewera

04/02/2025

Mmaganizo ndinachita kale

Zochotsa ndalama nthumba
Zovala nkupatsa naliyera achape
Mmaganizo ndalama ndinachotsa
Chododometsa Naliyera sadanene
Ndangoonera ndiwo zakhuli
Ndigwire nthumba lathalauza ndalama nulibe
Ndangodziwa mmaganizo ndinachita kale

Eti kuchoka pa malonda nkusiya chanje
Muntima nkumati andipatsa kale
Osadziwa kuti ndinayiwala
Nditangogwira nthumba ndipomwe ndazindikira
Mmaganizo chanje ndinatengakale

Kumampangira nsanje namwaliyo
Akayima ndi ena nsunanamo ndinvekere
akutani naye
Ntima kutupa kufuna kuphulika
Nsanje yatambala iri muntimamu
Aliyense okamba za nambingeyu
Udani timapalana ati poti akulimbana ndi wanga
Pomwe ndimadzakubukira
Chinkhoswe atapanga ndi wina
Ine manja alinkhosi
Mmaganizo nkaziyu ndinamufunsira
Ine aravomera
Mmaganizo ndinachita kale

🎉 Facebook recognized me for starting engaging conversations and producing inspiring content among my audience and peers...
01/01/2025

🎉 Facebook recognized me for starting engaging conversations and producing inspiring content among my audience and peers!

30/12/2024
28/12/2024

Tikupanga zoti titulutse buku landakatulo ili likhala buku loyamba kusindikizidwa mu mbiri yanthu ngati alembi a ndakatulo nonse akufuna kwabwino tiyeni tipangeni support

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Gloria Kaliati, Gift Malinga
21/12/2024

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Gloria Kaliati, Gift Malinga

20/12/2024

Likadza tsiku latsoka

Mumayamba ndinkutu kufadi
Ugonthi umakulira kulira
Makani umachita kunga ofula agalu
Kuposa yayikazi nfiti ntheradi
Litalimba tsoka nkute umakutethadi
Vuto munakwera pansana panjovu
Mame singawawone olo titanyowa nawo
Tidakusandutsani andya nyemba
Mwatiiwara adya makokofe

Likadza tsiku latsoka
Umayakha mafunso mosaganiza
Nkumaona ngati nzabeino
Aliyense umantenga ofanana nawe
Machitidwe kaoezedwe ndi kithekera
Mukuyiwala kuti ukatamba tamba
Yang'na kummawa kungakuchere
Bondo ndilinongoza ndidalakwitsa
Zoonadi chosadzi mfiti mmanja ndinayimbira
Nkadadziwa therere nkadaphika
Masiku sakoma onse koma izi zanuanya
Kati delu kaopsa mlenjedi ananu
Ndakulapa nkulinga utayendanaye
Wationetsa zowawa nthawi nkachiysiru

Likadza tsiku latsoka
Umasowa kothawira
Omwe ankakukonda atakuthawa
Wopanda nyangawu umapukusidwa
Poti udasankha unkhutukunve
Limodzitsi chidzatera olo chiyauluka bwanji
Dzenje mwadzikumbiraro simudzalidumpha
Misonzi ya anthu ochulika idzagwa
Inde idzagwera chikondwerero cha kutha kwanu
Zonse mudzszisiya adzatenga anzanu
Pokuperekezani ngati ankakukonda
Ufumu mufzsvekedwa mukutsikira kulichete
Kokadzala nkhadze kwanu kapande
Angoni pothokoza amati zimatha wawa
Nzosiyilana palibe wamuyaya dziwani
Lanu tsiku latsoka lidzakwanadi
Simudzalidumpha mudzakumanzndi nkwiyo

Likadza tsiku latsoka
Mudzalira ndikukutamano
Anakudyerani aja sadzakusamalani
Mudzaona ngati kutolo
Mawanga adzasitha anasi anuwo
Mudzaona ngati chisumphi wakondera
Mudzalaka laka mutangolowa pansi
Okutothozani adzachepa
Bwezilenireni lidzadziwika
Makutu anu auzimu adzatsekuka

Address

Zomba
91313

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ndakatulo za luntha posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share