07/04/2023
MWANA WA A LANDLORD
Ester mwana wanga waitenge kuti mamba, ndipo iye anayankhula nati ineyo ndikukhuzidwa pa mimbayi, Laptop yanga inatsala pang’ono kugwa kuchokela pa tchafu zanga.ndipo ndinayankha sindikunvesesa!!
Ester anandiloza ine ndikuzayankhula kuti ndikukhuzidwa pa mimbayi.ndinabalalika kwambiri. “Ndi inuyo Mr Emz” anayankhura. Yesu!! Komatu tinangogognana kamodzi, mwina nkutheka chishango chinaphulika kapena akufuna angondikakamiza kuti mimbayi ndi yanga……. Mulungu, ndabalalika ine. Amenewa ana maganizo amene ankayenda mmalingalilo anga.
Ndinakumbukila tsiiku loyamba nditangofika pa mudzi umenewu ndinakopeka chifukwa cha ukhondo komaso bata. Malo achilengedwe cha bwino kwa mlembi ngati ine.
Ndinasamukila mu numba yanga monga bachelor ( munthu osakwatila) ndinalibe zinthu zambiri, ndinalongeza katundu wanga mmene ndinkafunila, nditamaliza kulongeza katundu wanga ndinaphika ka chakudya kanga ndikudya kenako ndinapuma.
Kutacha tsiku lostatila ndinayenda yenda mmudzi , ndinapeza kuti anthu ambiri ndiosakwatila ndi ochepa okha amene anali m’mabanja komaso omwe anali ndi mabanja awo.
Chifukwa sindinali pa ntchito kupatula kulembemba nkhani zomwe ndimapanga tsikundi tsiku, kusakhala pa ntchito kwanga kunabweretsa vuto pa mudzi anthu anayamba kundinena kuti ndine lova chonsecho ndimigwilitsa ntchito an Iphone komas ndnali ndi an appel laptop.
Koyambiria sankandinkafusa za nkhaniyi Chifukwa choti ndine muthu ofasa komasa owoneka monyozeka mumawonekedwe, kufikila tsiku lina ndikufika pakhomo ndinapeza Anthu a ku boma ali pa bwalo la nyumba yanga. Tachokela ku boma tanvesedwa kangapo kuti ndiwe Munthu okuba kudzela pa internet ( internet fraudster) anatelo munthu wachikulile.
Ndipo izi ndi zotiyeneleza (Identification card) za ku ntchito kwathu, anatelo akundionetsa mapepala omwe angadzagwirile ntchito kunyumba kwangaku yofufuza myumba, muphone, mu laptop komaso chilichonse chomwe ndinali nacho.
Pompo pompo anthu a mmudzi anatulukila ndikudzaona zomwe zikuchitika moti ena ankajambula ndi ma lamia awo a pamwamba. Ndinamwetulila ndikuyankhula m***a kuyang’ana paliponse mnyumba mwangamu.
Panali munthu winawake wachilendo amene amandiyang’na kwambiri ngati tinakumanapo penapake, Atamaliza kufufuza paliponse kuphatikizapo mu laptop ndi mu lamia. Munthu amene amandiyang’ana kwambiri uja anabwera ndikuzandifusa ngati ndimaopa ndipo ndinamuyankha kuti eya ndimawodi.
Ndipoo anamwetulila ndikundilimbikisa kuti ineyo siokuba komano ndine mlembi, Anawafotokozela ndine bambo amwana amene amafuna nyamatuyu, chifukwa mwanayangayo ndi amene anandipangisa kuti ndiziwelenga nkhani za nyamatayu zambiri.
Anawafusa ngati akukumbukila nthawi yomwe ankaseka mo office muja, za nkhani yake yomwe imakamba za nyamata yemwe ankafuna kuphedwa ndi tsıkana wa kuphalombe chifukwa cha chigogolol ndipo anayankha eya takumbukila.
Anawawuzaso kuti nkhani ija ndiyowona ndipo inandichitikila ineyo. Ndipo kufotokoza kwakwe kunandipulumutsa kenako anandipasa numbala ya phone ndikundiwuza kuti ndipite ndikawachezele komaso kukadya chakudya cha madzuro ndipo ndikatelo mwana wawo adzakhala osangalala, ndinalandila nambala ija.
Anthu ammudzi anandipepesa ndikundiwuza kuti iwowo amangopenekela(vigilant) ndinawayankha, panalibe kuchitila mwina komano kuwawuza akubomawo ndipo sindinakwiye, ndinatelo.
Madzuro amenewo ndinayima pakhomo panya ndikuwawuza Anthu amene anali pamenepo kuti alowe nyumba komaso ester mwana wa a landrod analowa nyumba mwanga
To bee continued…………..