22/09/2022
THE DENIED RING
• CHAPTER 09•
Like the pages.
Umiasi Book Series and Kingman Stories.
Kwa omwe akufuna kukhala sponsor wa nkhaniyi m***a kutipeza pa ma number awa;
Ka Bird 0883236863
Kingman 0993701546
By Ka Bird
Jonez atamaliza kufotokoza zonse, anamumva Haryana akulankhula modekha koma mwaukali nkuti panthawiyi misozi itazaziratu ku nkhope yake
“ Jonez ndiwe oyipa kwambiri! Jonez ndiwe mfiti! Ndiwe otani koma kundipha moteromo ineee!”
“aaah Komano kungoti.....”
“ hey shiiiii.....! ndisekere chimbuzi chakocho ukuziwa I think umasangalala ukamaona misozi yanga, and zikuonesa kuti sunamve bwino pamiyezi ndakhalayi osakudandaulapo koma ndamvesesa , Mesa wati sindizaberekanso let it be like that ! ndachilandira ndeno chomwe ungandipangire ndikunditurukira mnyumba mwanga muno pompanoo!!”
Jonez adayesera kuti ayankhureko adangozindikira walandira mbama
“ tuluka muno ndisakuganizire zoyipa mfiti iwee”
Jonez adaziwa akuti munthuyi wakwiya mwachoncho sadakakamire koma kutuluka munyumba’mo. Haryana sanazitengere nthawi kuti akhale pansi nkuziganizira Zomwe adayankhura Jonez zija koma malo mwake adakasintha zovala ndikutenga galimoto ulendo waku Restaurant yomwe Jazzy amagwira ntchito.
“ hey takulandira wabwera kuzadya dinner kodi?” Anafutsa Jazzy.
“ ayi ndikufuna ndikumane ndi abwana ako”
“ abwana anga !? okay anyway ali ku office kwawo tiye ndikakuonese”
Jazzy adamutenga Haryana kuti akamuonese ku office ya abwana akewo.
“ hey ndi Miss Haryana kodi, ndakukandirani mukhoza kukhala pampandopo “
Eni ake a restaurant'yi adamulandira Haryana ndi nsangala poti ankamuziwa ndikale.
“ Hey mwaswera bwanji koma?”
“Ndaswera bwino!Kaya inuyo sir”
“Ndaswera bwino, eyetu nde mwangotiyendera kodi?”
“ Mr Dan ndimafuna ndimutengeko Jazzy ndikufuna andiperekeze kwa mchimwene wake”
“ oooh okay Komano pali vuto pang’ono , Jazzy wakhala ndi tima holiday tolumikizana sabata ino ma excuse ambirimbiri, nde eeh antchito ena kumuwelusanso mwachangu lerori akhoza kukaganiza zambiri”
“Mr Dan imeneyo ndi 5000 mungomwera madzi”
“ aah oooh ookay vuto pa-palibe Miss Haryana ndizoti apapa zatheka kkkk”
Mr Dan atangomva kandalama kaja adavomera kumuwerusa Jazzy nthawi yolakwika. Kenako Jazzy ndi Haryana adakakwera galimoto ya Haryana koma mnyamatayu sankaziwa komwe akupita.
“ hey kodi ukuyendeseranji galimoto mwaliwiro choncho chifukwa chani?”
Jazzy adamufunsa mtsikanayu ataona mayendesedwe akewo akhoza kuchita nawo ngozi koma Haryana sankayima malo mwake ndipomwe ankaonjezera speed.
Haryana adayendesa galimoto ija mpaka kumalunjika msewu waukulu ochokera muzimdawu kupita kumzinda wina. Jazzy mantha anayamaba kumugwira chifukwa njira yomwe amatengayo kopita kwake kumayemera kukhala kumudzi kwachina Haryana’yo.
Haryana atafika pakatikati pa msewu wamizinda iwiriyi panali club ndipo adayimisa galimoto pomwepa
“ hey tiye tafika malo omwe timapita nde ukhoza kusika”
“ oh iwe mtunda onsewu timabwera ku middle point club?”
Jazzy adafunsa momudabwa kwambiri mtsikanayu
“ yesss ndisatire.....”
Haryana adamuuza Jazzy kuti amusatire ndipo onse adalowa mkati mwa ka club muja. Atafika mkati, Haryana adayitanisa mowa mabotle awiri
“ hey kodi nzoonadi ndekuti zoti unasanduka chilezerere ?”
“ yess ndi chilungamo ndithu, ndetenga mabottle awiriwa lina langa lina lako”
“ sindikufuna mowa ine!!!”
“ okay nde undidikira”
Ogulisa mowa adatenga matambula ndikumupasira Haryana
“ hey ayise sunga ma tambula akowo !”
Haryana adamulesa matambula aja chifukwa choti amamwera direct ku bottle Jazzy ankangomuyang’ana mtsikanayu.
Haryana adayamba kumwa mowa uja almost ma bottle anayi , naye Jazzy anangotenga botolo limodzi ndikumamwa
Patadusa maola angapo awiriwa akucheza pa phone ya Jazzy padafika message kuchokera kwa Aria
““hey jazzy uli kuti? ndinapita kuntchito kwako ndiye Mr Dan andiuza kuti waweruka kale, aah ndikufuna ndikumane nawe chifukwa pali zoti tikambirane’”’
Jazzy sadayilabadire message ija atangoyiwerenga adayika phone mthumba sadaganizenso zomubwezera
“ hey ndindani ameneyo haaa Nanga bwanji sukumuyankha”
“ aaah zitaye ndizopanda ntchito ndi chibwezi changa”
“ hey mxieew ndiwe otani kumandiuza zopusazo. Hey taodi ndipase phone’yo”
Mawu omwe Jazzy adayankhura adamuguguda pachifuwa Haryana kamba ka mowa adamufunsa Jazzy mpaka kulanda phone kuyamba kuwona message ija.
“oh ndekuti chibwezi chako ndi Aria eti ? ooh iwe Jazzy ndekuti umandizembera sichoncho? koma umadziwa mmene ndimamvera za iwe koma?”
“ hey iwe ukuyankhurazo ndi zichani sopano”
Jazzy anadabwa ndizomwe Haryana’zo adayamba kuyankhura mokhala ngati akunyasidwa adamufunsa funsori
“ hey ndekuti sukumvetsesa ? just imagine; ndikamalira misozi imasiya, maso anga akangoona iwe, ndikayamba kumva ululu wamumaganizo ndimapeza mtendere ukandifungatira , do you remember ndinkafuna kuzipha koma ndinazabweza maganizo chifukwa cha iwe, ndili kutali kuno koma sindikanakwisa kubwera ndekha kopanda iwe ndeno zonsezi zikuthandauza chani!!!”
Haryana adakuwa moti anthu onse anali muclub muja ankamva. Ntsikanayu adapita ndikukayima komwe kunali a Dj amu bar’yi nkulanda micphone. Anapitiriza kuyankhura.
“ hey Jazzy sindikuziwa kuti uyankhura zichani komano , ma feelings anga akundipanga force kuti ndizikukonda , ndipo zikuonesa kuti ndalephera ku wapanga control , sindinganene zambiri Komano the thing is ndili mukusausika muchigwa cha chikondi...,,Dj ndiyikire nyimbo Kerr Albert thousands reasons to love you”
Dj uja adamuyikira mtsikanayu nyimbo yachikondi ija, Mtsikanayu ankayiyimba ndi mtima osweka moti anthu omwe anali mu club muja nyimboyi inkawakhuza .. Haryana akungomalizisa kuyimba kuja adagwa pansi, kamba koti anali atalezera kwambiri.
Jazzy adakamutenga Haryana nkukamuyika mugalimoto kuti azipita koma nthawi inali itatha. Mtsikanayu anamuuza Jazzy kuti akuyenera kugona konko.
“ hey man kodi kuno kuli ma room ngati?
Jazzy adafunsa kwa barman.
“ yaah alipo ndithu komano ndi a bed limodzilimodzi”
“ aaa it’s okay”
Jazzy adapasidwa room kenako ndikulowa ndikumugoneka Haryana
“ hey ndikupita kukagona mu galimoto”
“ ko-koma undisiya ndekha muno morning?”
“ aah ndibwera kuzakuonanso nthawi ina”
Jazzy atangoyankhura mawuwa adaganiza zotuluka koma akuti azituruka adangopeza Haryana wamugwira mkono
“ hey Har.....”
Mtsikanayu sindikuziwa kuti inali mphamvu yamowa kapena chani😂, Jazzy asanamalizise kuyankhura anali atamuvungira kale kiss , kwinako akumugwira malo osakhala bwino. Jazzy anatheratu mpaka kuchita zosakhala bwinozo...................
Malive Street
Jonez atangochoka kunyumba kwa Haryana kuja adayenda straight kupita kuntchito kwawo ndikukapereka chidandaulo chofuna kusiya ntchito. Bwana ake anavomela moti anapanga zonse monga mwakufuna kwake. Anamupasa ma pepala aumboni kupangira pa mawa.
Atamaliza kupanga zakezo adayendera straight kubar komwe adalezera mpaka kufika pamlingu ogonana ndi akazi oyendayenda.
Jonez anachoka kuja atatheratu ndipo adafika pa nyumba usiku nthawi ikuthamangira chama 7.
“ hey Ibrah watan brother wangayo”
“ madam a zanga ena ake akuti awatenga kubar anali atangogona pansi nde anaganiza zozawasiya kunyumba kuno”
Kuchoka ku bar kuja Jonez adachita kutengedwa ndi anyamata ena ake omwe ankaziwana ndi guard wake
“ hey kodi ndichifukwa chani ukupanga izizi”
“ chifukwa this is what I have chose! ! ! komanso ndikuuze ine sindingapepese kumuthu okay , umuuze Jazzy wakoyo sindikusamala za iye am living my own life ... nde-nde iwe Ibrah nditengere kuchipinda kwanga”
Jonez analezereratu kufika pasize yoti amakanika or kuyenda . Ellen adamudandaura kwambiri brother wakeyo
Ikupitirira..........
Chonde macoment’wo pliz