08/04/2026
Thank you Nation Publications Limited for the feature
Get your tickets now 🔥💯💯 Asanthe octhipawa 🔥💯💯💯
Mmodzi mwa okonza mapwando a maimbidwe ku Mulanje, Michael Kwapata, wati apitiriza kuitana akatswiri oimba kuti azisangalatsa anthu m'bomali ndi madera ozungulira.
Kwapata wauza izi pomwe katswiri woimba wa chamba cha Amapiano m'dziko muno Joe Ikon akuyembekezera kudzangalatsa anthu ku malo a Cork & Bottle m'bomali pa 25 April 2026.
"Tiwabweretsera oimba aluso ndi onse akuyakitsa moto msangulutso m'dziko muno. Pa 25 kukubwera Joe Ikon ndipo anthu adzakondwa ndi kuvina mothetsa mankhalu chifukwa mkuluyu amayakitsa moto," watero Kwapata.
Iye waonjezera kuti zokonzekera zili mkati kuti phwandoli lidzakhale lopambana monga nthawi zonse.
Anthu adzavina nyimbo za Joe Ikon, yemwe ndi woimba wa Madness Entertainment, monga Pang'ono, Ndafika, Agulu, Oneni ndi Mpaka M'manda.
Mmodzi mwa okonda mapwando m'bomali, Tina Makawa, wati umoyo uli bwino chifukwa akupatsidwa mwayi wotula nkhawa ndi zilinganizozi.
Zina zochitika ku malowa pa tsikulo omwe ali kuseli kwa bwalo la za masewero la Mulanje Park ndi monga mayere, kudzipenta nkhope, kuonera masewero a mpira, ndi kumwa zakumwa zaukali.
Wolemba: Temwa Mhone