24/08/2026
STOP BEING SENSITIVE, IT'S JUST A SONG!!! ๐ซ
Mukudziwa chifukwa chake anthu akukwiya ndi nyimbo yatsopano ya S Khrizy yokhudza Temwa Chawinga?
Chifukwa S wanena zoona zowawa zomwe aliyense amazidziwa mumtima koma osalankhula mokweza chifukwa cha ulemu.
Yes, Temwa sanasankhe kubadwa momwe alili ndipo ndi God's Plan, koma tonse tikuona kuti iye ndi tomboy ndipo mwini wake anavomereza kale, cholinga chake ndi mpira osati kukhala baddie. Koma izi sizipatsa ufulu kwa S Khrizy ndi bwenzi lake kumunyoza mu nyimbo.
TEMWA CHAWINGA ndi National Treasure, akusewera football ya elite padziko lonse, amafunika kutetezedwa pa mtengo uliwonse ndipo amayenera ulemu wonse.
Koma muyeneranso kumvetsetsa kuti S akadali mwana. Kutchuka kwake sikunamulowe m'mutu. Akuyendabe ngati upcoming wopanda Direction, No Future, No Manager, No Plans. Nde amangokhalira ku diss, kutulutsa nyimbo tsiku lililonse komanso obsessed ndi Spe chifukwa sadziwa kuti wamuposa kale ndipo pano ndi HOTTEST NEW ARTIST mu 265 yonse.
Mawu ake tsopano ali ndi mphamvu ndipo with great power comes great responsibility. Nyimbo zake zikumvedwa ndi anthu zikwi mazana ambiri, nde tsopano afunika kusamala amene aku diss mu nyimbo zake.
Nyimbo imeneyi ikanatulutsidwa ndi upcoming wamba ngati Em EL kapena Ace Dirty or Ca$ino, palibe akanadandaula, koma chifukwa ndi S, nde nkhani yayikulu.
Ndipo vuto lina ndi lakuti wazunguliridwa ndi ma dummies omwe ali pafupi naye chifukwa cha fame yake yaying'ono & clout koma samasamala za career yake ndi future yake.
Tsopano A'bale fans ndi OBG Haters akuganiza kuti ndi nthawi yawo yokondwerera GoGo Downfall? Like n***a WHAT? ๐ซ
Simungathe kuwononga chinthu chomwe simunapange.
S adatchuka yekha, No Mikozi, No Joy NaThu, No A'bale, No Landlord Academy, No Big Homies, No Big Kizzy, ndi iye yekha ndi nyimbo zake zoyaka moto,