Raja B The Poet

Raja B The Poet We Eat Poems

22/05/2025
14/05/2025

With Rajab Mwana Omupeza The Poet โ€“ I'm on a streak! I've been a top fan for 9 months in a row. ๐ŸŽ‰

29/03/2025

With Rajab Mwana Omupeza The Poet โ€“ I'm on a streak! I've been a top fan for 7 months in a row. ๐ŸŽ‰

16/12/2024

With Rajab Mwana Omupeza The Poet โ€“ I'm on a streak! I've been a top fan for 4 months in a row. ๐ŸŽ‰

30/10/2024

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Odetta Andrea, Memori Siwema Weston, Sygles Stars

*๐Ÿ‘ฐM Y  B E S T  G I R L๐Ÿ‘ฐ**Episode 1๏ธโƒฃ6๏ธโƒฃ๐Ÿ‡**By Raja B The Poet ๐ŸŽค๐Ÿ’ฅ*๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธMu episode 15 tidaona Donata...
27/11/2023

*๐Ÿ‘ฐM Y B E S T G I R L๐Ÿ‘ฐ*

*Episode 1๏ธโƒฃ6๏ธโƒฃ๐Ÿ‡*

*By Raja B The Poet ๐ŸŽค๐Ÿ’ฅ*

๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ๐Ÿƒ๐ŸŒช๏ธ

Mu episode 15 tidaona Donata akutsika mu galimoto yake uku Rojas ali pambalipa ndipo adali akuyenda pa chinsalu chofiira antchito akuwayimbira nyimbo.

*๐Ÿ‡๐Ÿ‡๐Ÿ‡Fast Forward ๐Ÿ‡๐Ÿ‡๐Ÿ‡๐Ÿ‡*

Aida adali chakumapeto ndipo adali ndi chidwi chofuna kudziwa boss ndi madam boss a kampaniyo chifukwa adali akunenedwa kuti ndi ovuta komanso amatama plus kulalata.

Madam Donata akuyenda chonchija adatelereka ndipo adadzandira mpaka kukamugwera Aida ndipo Aida adawagwira kuti asafike pansi.

Anthu onse adaweramira pansi ndipo Donata adadzuka kenako adamulavulira malovu Aida nkumuuza zoti akununkha .

Aida adapukuta malovu aja kenako Donata adakalowanso mgalimoto nkukasintha zovala plus kudzithira perfume.

Aida adali okhudzika kwambiri maka kamba kolavulilidwa koma adali asadawayang'anitsitse bosslady wo moti ataona zoti akubweranso adadzutsa mutu kenako adawerama mwachangu uku mtima utatentha plus mkamwa kuotcha atamuzindikira madamuyo kuti ndi Donata.

Aida adacheukira komwe kudayima Jimmy koma sadamuone .

Apa mwana wamkazi sadaimve koma kuchokapo wautali kunyumba kwake kumene adakamupeza Jimmy akupakira ndipo adafikira kufunsa.

Aida:::::"Kodi nawenso waona zomwe ndaona ine?"

Jimmy::::"Malodza enieni,,,, nditangowaona basi chiganizo chomwe chidabwera m'mutu mwangamu ndi chosamuka."

Aida::::" Zoona,,,, koma nanga kusamukako tipite kuti? "

Jimmy::::" Dzulo ndinapezana ndi nzanga dzina lake Chikayiko Maliseni amene amagwira ntchito ku Chankhungu estate 73 yomwe tayandikana nayoyi ndipo adandiuza kuti akufuna kulemba ntchito ma labour okwana 20 mawa lino. "

Aida:::::" Nkhani yabwino,,,,, basi tiyeni ,,, bola akatilembe kumeneko osati malodza akunowa. "

Jimmy::::" Komanso chosangalatsa nchoti akuti mwini kampani imeneyo ndi munthu wabwino kwambiri,,, antchito ake amawasamalira plus kuwamvetsetsa osati akanyimbi awa achina Donata ndi Rojas. "

Apa atakambiranakambirana adayamba kuthandizana kupakira katundu ndipo atamaliza adadikilira kude kaye kuti asamuke usiku koma Jimmy adapita ku 73 kukamuona Chikayi uja komanso kukamudziwitsa zoti amufunire nyumba.

Atafika ku 73 kuja adakumana naye Chikayi amene adamutengera kwa manager wa pa kampanipo Mr Bashir.
Manager Bashir adamuuza Jimmy kuti asadandaule ntchito amulemba koma adamuuza kuti malamulo apa kampanipo ndi oti amafuna munthu okwatira kapena okwatiwa osati mabatchala.

Jimmy adawauza zoti iyeyo akubwera ndi mkazi wake ndipo manager Bashir adamuuza Chikayi kuti awapelekeze kwa a polisi compound (mfumu ya pa estate) kuti awapatse nyumba.

Atafika kwa a polisi compound adawalandira ndipo adawaperekeza ku domitale kapena kuti mdadada *(chinyumba chachikulu chokhala ndi zipinda zambiri ndipo chimakhalidwa ndi mabanja oposa 20 )*.

Jimmy adapatsidwa chipinda chimodzi chimene chidali pakati penipeni pa domitale ija.

Atachezacheza Jimmy adabwelera ku Chimwemwe estate kumene amadikilira kusamuka usiku .

*๐ŸŒช๏ธ๐ŸŒช๏ธRaja ndi Junior๐Ÿƒ๐Ÿƒ*

Raja pa tsikuli adali akulowera ku airport kukamuchingamira Junior amene adali kamnyamata kokongola plus kukhala kwa azungu ndiyetu kudali kuyera plus kukula mwachangu.

Atamuchingamira adafika naye kunyumba kumene kudali mlongo wake wa Raja dzina lake Jessica.

Jessica adamulandira Junior ndipo Junior adafunsa.

Junior::::"Dad,, who is she?"

Raja::::"She is my sister."

Junior::::"Ok,,, thanks aunt Jessica. "

Jessica:::::" I am she brother Raja one blood. "

Junior:::::" What๐Ÿ˜ณ?"

Raja:::::" Kkkkkk nawe Jessy kagwere uko ndi chizungu chakocho kkkkk. "

Jessica::::::" Bwanji osangoyamika zoti ndayamba kuyankhula chingerezi,,, odi nkamuphikire Juu apa,,,, Juuu,,, let's went I cook super soseji mix mix english ๐Ÿš rice. "

Junior::::" Dad,, what is English rice? "

Raja:::::" Kkkkkk it's spaghetti ,,, Don't mind ,,, go and take a ๐Ÿšฟ shower. "

Jessica:::::" Kodi Juu amakonda shawa ? Mukanandiuza kaya bwezi nditamukazingira."

Raja:::::"Kkkkk iwe tamangopita ukaphike kkkkk. "

*๐Ÿƒ๐ŸƒRojas ndi Donata ๐Ÿƒ๐Ÿƒ*

Rojas ndi Donata adabwelera ulendo wawo ndipo atafika pa mtsinje wa Namitete akuti azioloka bridge Donata adamuyimitsa driver mokuwa amevekere.

*"Iwe driver tayimitsa apa ungandigundire mayi anga!!!! ๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธ!!"*

Rojas adali odabwa mpaka adamufunsa .

Rojas::::" Dia ,, koma uli bwinobwino? "

Donata:::::" Eyaaa koma muuze uyu asawagunde amayi ,,,. "

Rojas:::::" Kulibe amayitu uku ,, usaiwale zoti adatisiya. "

Donata:::::" Ayinso ,,, taona ,, ndi awo ali kutsogoloko ,,, amayiii๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธamaaaa๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธ!" Donata adaitana mokuwa kwambiri.

Rojas ataona zoti Donata walimbikira adamuyimitsa driver uja ndipo adatsekula chitseko nkumufunsa kuti ali kuti mayi akewo.

Donata adaunguzaunguza ndipo adati.

*"Komatu ndinawaona amayi ine,,, adayima apapa atanyamula baibulo uku atavala nsalu ya mvano!!! "*

Rojas:::::" Ndiye kuti umalota ,,, yako ija yomagona masana,, tiye tizipita. "

Atatero onse adakweranso ulendo nkumapitilira.

*๐Ÿ‡๐Ÿ‡Aida ndi Jimmy๐Ÿ‡๐Ÿ‡*

Aida ndi Jimmy adasamuka usiku ndipo adafikira mu mdadada muja ndipo apolisi compound adamuuza Aida nati.

*"Mayi mwalandiridwa ndipo abwana athu amasangalala ndi banja la mtendere osati lomangokangana kapena kumenyana ,,,,,, muli ma families ambiri mchinyumba chino ndiye asasowe mtendere kamba ka kubwera kwanu ,,, ndikhulupilira kuti mukhala banja lachitsanzo.! "*

Aida adali odabwa ndi kuyankhula kumeneku koma asadayankhe Jimmy adamudula nati.

*" Zikomo kwambiri amfumu,,,, ine ndi akazi angawa chikwatiliraneni sitidakanganepo choncho tipitiliza kukondana kwathu ndithu. "*

Aida adali odabwa ndi kuyankhula koteroko komabe adangomezera malovu nati.

*" Chabwino amfumu ,,,,, tathokonza kamba kakutilandira ndipo tikulonjeza kuti sitidzabweretsa mavuto pa line pano. "*

Amfumu aja adanyadira ndipo adatsanzika nkumapita kuwasiya achina Jimmy akufunsana koma Jimmy adangomuuza zoti awanamiza kamba koti pa kampanipo salola mabatchala.

*๐Ÿ‡๐Ÿ‡Raja ndi Junior๐Ÿ‡๐Ÿ‡*

Raja usiku umenewo adamuuza Junior kuti mawa akupita ku estate yake ku Mchinji kukayendera choncho adzapite limodzi komanso Jessica.
Mamawa kutacha after kusamba ndi kudya breakfast onse adanyamuka pa BMW yawo wautali ku Mchinji.

*๐Ÿƒ๐ŸƒAida ndi Jimmy ๐Ÿƒ๐Ÿƒ*

Aida ndi Jimmy adalembedwa ntchito ndipo ogwira ntchito onse adauzidwa kuti kukubwera mwini kampani koma asatekeseke ,, azingogwira ntchito yawo monga mwa nthawi zonse,,,,, poti boss man ndi munthu wabwino ndipo safuna kulemekezedwa kopitilira malire.

Pamene nthawi imati 10 am Raja adatulukira ku Chankhungu estate 73 kumene adapeza antchito akugwira moupeza mtima ndipo adayamba kuyendera malo osiyanasiyana.

Raja adamuuza Jessica kuti akhonza kumutenga Junior nkulowera mbali ina ya ku office ko kumakaona m'mene anthu amagwilira ntchito koma osamakayenda mwa matama,,,,.

Raja::::"Iwe Juu,,, umatha chichewa choncho osamangokayankhula chizungu wamva? "

Junior ::::" Ndamva adad ndipo ndikulonjeza kuti sindikaonetsa khalidwe lonyasa. "

Raja::::" Ndiye Juu wanga okondedwa ameneyo,,, goo. "

Jessica::::"Mwanena nokha kuti chizungu ayi koma mukuyambitsanso nokha,,,, go , go ndiye chani,,,,,, chabwino,,, *"she and we go travel out the office."*

Raja adangomwetulira nkuwauza zoti akhonza kutuluka mu office mo nkukalowa mu shed momwe anthu akusankhira fodya.

Junior ndi Jessica atalowa adapeza azimayi ali mbuuu ndi fumbi la fodya ndipo Junior adayamba kuwamvera chisoni anthuwo.

Amati akafika pa munthu amene watuwa amamupatsa moni uku akupereka ulemu ndipo anthu amakapatsa ulemu powona zoti ndi mwana osangalatsa plus waulemu.

Akuyendabe chonchija Junior adafika pa tebulo lomwe Aida ndi azimayi ena amasankhirapo fodya ndipo Junior adayima nkuyamba kuwafunsa azimayi aja.

Junior::::"Kodi ndiye kuti simumaweruka ?"

Azimayi;::::"Timaweruka bwana."

Junior:::::"Ine si bwana,,,,, bwana ndi bambo anga,,,, ngati mumaweruka ndiye werukani."

Azimayi:::::" Tiweruka nthawi ikakwana. "

Junior::::" Mumaweruka nthawi yanji? "

Azimayi;::::" Timaweruka aliyense akamaliza mgwazo wake."

Jessica:::::"Mgwazo ndiye chani? "

Aida::::" Mgwazo ndi mulingo umene wina aliyense amapatsidwa pa tsiku kuti amalize,,, monga ine,,,, iyi ndi mbokoma yanga kapena kuti mulu wanga wa fodya amene ndisankhe nkumanga ndindi ndipo ndikamaliza mbokoma imeneyi basi ndiweruka. "

Jessica:::::" Wow!!! Lero tiphunzira zambiri,,,,, amayi inu mukhale apongo anga bwaaa!!!!! Mwandisangalatsa."

Aida:::::" Zikomo,,,,, nanenso ndalemekezedwa ndi khumbo lanu madam,,,,, ndavomera. "

Jessica:::::" Thanks,,,,, dikirani ndikupatsani mphatso plus phone yangayi ndikupatsani kuti tiziyimbirana ndipo tsiku lina mudzabwereko kwathu ku Lilongwe,,,, kodi Juu,,, bwanji ukungowayang'anitsitsa apongo angawa? "

Junior:::::" Amayi inu,,,,, bwanji mukhale mayi anga? "

Jessica:::::",Kkkkkkk koma Juu,,,, amayi sitichita kugulatu,,,,. "

Aida:::::"Kamnyamata kokongola iwe,,,,, ndikhala mayi ako wamva? "

Junior:::::" Zikomo,,,, eni aka ndipo mukasunge ,,, adad anga adandipatsa akuti idali mphatso ya ...... "

Asadamalize kuyankhula adangomva kuitana kwa bambo ake ndipo Juu adamuhaga Aida nkumutsanzika koma Aida mtima wake udagunda kwambiri mpaka adakanika kuyankha kenako Jessica adamuuza Juu kuti .

*"Tiye tizipita,,, ndawapatsa phone tiziyankhulana wamva? Ona adad akubwera."*

Junior adanyamuka uku akuwakuwila adad ake amvekere.

*" Adaaaaaaaad!!! ๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธNdapeeeee!!!"*

Next,,,,,,, kkkkkkkkk komadi azungu paja adati blood is thicker than water !!! Kaya amatero kaya.

Kodi mwati zitha bwanji mu shed m'menemu?

Aunt Jessica abweranso ndi yawoyawotu.

Donata ndiye akuti akuwaona amayi ake atayima kutsogolo kkkkkkkk kayaaaa.๐Ÿค”๐Ÿค”

Kalikonse tikaona mu episode 17.

Join my WhatsApp group today through this number,,,, *0884849947*.

Or follow my page RAJAB MWANA OMUPEZA THE POET kuti nkhanizi zisamakuphonyeni.

Raja B loves you all good people with beautiful names ๐Ÿ™.

*๐Ÿ’ฅMKAZI WA MLONDA ๐Ÿ’ฅ**Episode 2๏ธโƒฃ2๏ธโƒฃ๐Ÿฆš**By Raja B The Poet ๐ŸŽค๐Ÿ’ฅ.*Sponsored by.๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐Ÿฉธ๐ŸฉธMu episode 21 tidaleke...
23/11/2023

*๐Ÿ’ฅMKAZI WA MLONDA ๐Ÿ’ฅ*

*Episode 2๏ธโƒฃ2๏ธโƒฃ๐Ÿฆš*

*By Raja B The Poet ๐ŸŽค๐Ÿ’ฅ.*

Sponsored by.

๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐ŸŽˆ๐Ÿฉธ๐Ÿฉธ๐Ÿฉธ

Mu episode 21 tidalekeza pamene Linda ndi Alick adasowa chochita atathamangitsidwa pa gate ndi ma guard ndipo Linda adayamba kulira maka ndi momwe situation idaliri.

*๐ŸฉธFast Forward ๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€*

Mr Alick amati kuyima apa kuchoka ,,, nkudzayima pena nkuchokanso kenako adazitolera mphamvu ndipo adayamba kuyenda pamodzi ndi Linda koma komwe amalowera samakudziwa mpaka adafika pa Mulunguzi bridge pamene Linda adakhala pansi kamba kotopa.

Naye Alick adakhala nawo kenako patatha 2 minutes adayamba kuyankhula.

Alick::::::"Waonatu phuma lako,,,, ndinkakuuza ine kuti tiye basi tivomereze koma kakaka dyera ndi chuma."

Linda:::::" Galu iwe ukuti chani? Zoti ndinakuda kuyambira kale siudziwa? Kupanda iweyo bwezi ine ndili mkazi wa Raja mpaka kale. "

Alick::::::" Zopusa,,, zoti ndi iwe amene udachita kundiyamba dala waiwala? Kupanda iweyo ine bwezi banja ndi Naomi lilipo."

Linda:::::::" Koma iwe Alick,,, usandinyase apa wamva ? Mwamuna wanji opanda ma plan ,,, bwezi pano chuma chija chili chathu koma kugona uli fwiiiii. "

Mr Alick adakhala kwa kanthawi kenako adati.

Alick:::::"Tiye tisiye zokangana,,, uno ndi usiku mwinanso yakwana 10 pm ndiye akatipeza apolisi tikukangana angotitengapo. "

Linda:::::::"Ine ndimaganiza ngati tikasume zoti Raja watithawira."

Alick::::::"Tizikayambira pati? Ukukudziwa komwe Raja wapita?"

Linda'::::::"Ndimayesa a judge wo ndi amene akamuyang'ane Raja? "

Alick:::::" Kkkkkk koma umbuli winawu,,, taona ma lawyer aja adatinyanyalira ,,, ndiye ndalama inanso tikaitenga kuti yoti tiwalipile?"

Linda::::::" Alick ganiza ngati mwamuna ,,,, ndiye tikapanda kutero tizitani mtown muno? "

Alick;::::::"Zomwe tichite apapa ndi choti tipeze malo oti tikagone ,, zinazo tikakambirana konko. "

Linda':::::::" Ndiye tikagona kuti ? Tilibe ndalama iliyonse plus ine ndiye ndili ndi njala ndisaname. "

Alick::::::" It's ok,,,, apapa ndikuganiza ma plan,,, Eyaaa wamuona wanjinga yamoto akubwerayo? "

Linda:::::" Eya,,,, bwanji? "

Alick:::::" Iweyo chita ngati wasenza katundu ndipo umupemphe lift ,,, sangakane chifukwa ndi iwe olumala,,,,. "

Linda:::::" Ok,,, kenako ndipange bwanji? "

Alick::::::"Akakukweza umubaye ndi mpeni uwu ,,, upange changu asadafike pa fueling station po. "

Linda:::::" Ndipanga zimenezo,,, ndiye iweyo utani pamapeto pake.?"

Alick::::::"Ukamubayamo mugwetsana ,,, ine ndidzabwera ndi chimwala ichi nkumumenya nacho m'mutu kenako timulande njingayo plus ndalama. "

Linda:::::" Deal done,,,, focus. "

Linda adayamba kuyenda ndi ndodo yake ija uku atanyamula chikwama ndipo wanjinga yamoto uja atafika adamufunsa komwe akupita ndipo Linda adati.

Linda:::::::"Chonde ndithandizeni ,,, ndikupita kwa Chimsewu ndiye ndimati mukanditsitsire pa msewu opita ku Namitembo. "

Wanjinga:::::" Ok,,, kwerani ndipo simulipila ,,, nkakusiyani ,,,,, chitani changu poti kwada komanso pa bridge pano pamamveka ndi mbiri zonyasa. "

Linda adakwera ndipo wanjinga pamene amati ayambe kuyenda mwansangansanga Linda adatulutsa mpeni nkumubaya nawo pa khosi mpaka kutulukira mbali ina pompo wanjingayo adagwa ndipo Alick adatulukira nkumumenya mutu ndi chimwala mpaka ubongo udafwamphuka kenako mnyamata wanjinga adamwalira pompo.

Alick ndi Linda adamusecha m'matumba nkupezamo zindalama plus ma ID awanthu ndi ma simcards zomwe adadziwiratu kuti mnyamatayo adali agent .

Atakwezana njinga ija adayenda ndipo amati akafika pa roadblock amazembapo nkukatulukira kutsogolo mpaka adakafika ku Nserema pamenepo nkuti nthawi ikuthamangira 4 am .

Atafika pa trading ya Nserema adaganiza zobwelera nkupita ku Nayuchi kuti kukacha bwinobwino akwere sitima azipita ku Mchinji.

Pamene kumacha adapezeka zoti afika ku Nayuchi kumene adasintha maganizo okwera sitima aja ndipo adaganiza zongolowa m' Mozambique .

Linda ndi Alick adalowadi m' Mozambique ndipo adakafika pa ka trading kamene kali mkatikati mwa Mozambique dzina lake Mitumbi komwe adapeza nyumba ya rent.
Linda ndi Alick atawerenga ndalama zija zidali zokwana 300 thousand kwacha ndipo adayambira geni ya zovala imene Alick amapita ku Nayuchi nkumaoda pa njinga yakuba ija imene adaisintha paint.

*โ™ฅ๏ธโ™ฅ๏ธRaja ndi Naomi โ™ฅ๏ธโ™ฅ๏ธ*

Raja adali atapita ku Tanzania ku chilumba cha Zanzibar kumene adapita pamodzi ndi makolo ndi azibale onse a Naomi ,,,,.

Raja sadathere pompo koma adawafufuzanso azibale amalemu bambo ndi mayi ake amene kamba ka thandizo la Dr Junaid Faziri adawapeza kuti ndi aku Balaka.

Ku Zanzibar kudali company imodzi komanso plot ya Raja and ndi kumene adakafikira kenako patatha 2 days Naomi adafuna kumudziwitsa Raja zoti ali ndi mimba.

Naomi adawauza abale ndi alongo ake plus akwawo kwa Raja kuti akuwafuna pa sitting room.

Onse adafika ndipo Raja adali odabwa ndi kuitanidwa kwadzidzidzi kumeneko kenako onse atakhala Naomi adayamba kuyankhula.

Naomi::::::"Adad,,, Amayi,,,,, mwamuna wanga okondedwa Raja,,,, azibale nonse amene tili muno ,,, lero ndabwera ndi nkhani yabwino yoti nonsenu mukondwera nayo,,,, mwamuna wanga Raja ndi amene akuuzeni,,, Raja ,,, talota ,,, ndi nkhani yanji yomwe ndikuinenayi? "

Raj:::::" Dear,,,, inetu sindikudziwa kkkkkkk ndiuze. "

Febe:::::"Asisi Naomi Ife tikuidziwa nkhani yake,,, ndimayesa ndi yokhudza ukwati wanu mukufuna uchitikire kuno?? "

Raja:::::" Ayini apo ndiye mwalasa,,,,, amama ,,, adad komanso azibale nonse,,,, ndiloreni ndilengeze zoti ine ndikufuna ukwati wathu uchitikire kuno !!!!!! ๐Ÿฉธ"

Apa achibale onse adalulutira ndipo adayamikira ganizo limeneli.

Naomi:::::"Ayinso,,,, nkhani siyokhudza ukwati!!!"

Apa makolo onse adamucheukira modabwa muja ndipo Raja adati.

Raja::::::" Nao,,,, koma ukuzidziwa zomwe wayankhula pamenepo?"

Naomi::::::" Kwambiri,,,, ndipo ndikubwerezanso zoti nkhani yake si yaukwati. "

Raja:::::" Ndiye palinso nkhani yabwino kunoku yoposa ya ukwati?"

Naomi::::::;" Eyaaaa,,, ndi imene ndikufuna ndikuuzeni. "

Apa onse adachita kukhala chete uku akumuyang'ana Naomi mwachidwi kenako Nao adati.

Naomi:::::::"Ndikufuna nonse muone miracle ,,,,, ndipo miracle imeneyi ikundipangitsa ine kukhala mkazi osangalala koposa aliyense pa dziko pano. "

Febe:::::" Asisi inu tangonenanitu ife mitima yathu ili phamuphamu apapa,,, ndi chani? "

Naomi::::::" Raja tabwera ,,, tiye kuno . "

Naomi adamutenga Raja nkulowa naye kuchipinda kenako adatulutsa ka PT ndipo Raja adafunsa.

Raja:::::"Nkachani kameneka,,,,? Kapena ndi koyezera magazi ?"

Naomi;:::::"Kkkkkkkkk ayinso,,,, ndikufuna ndikodzere mu ka kontena aka ndipo ukaviyike ka PT ka mu kontena mu then udikire pang'ono kwa 3 minutes chabe kenako ubweretse pa sitting room ndipo umupatsire Febe kuti alengeze zomwe azione pamenepo,,, imeneyi ndi suprise kwa iwe ndi makolo onse. "

Raja:::::" Nao,,, sindikukumvetsatu ine,,,, kodi ukufuna kuyeza chani? Kapena uli ndi chindoko? "

Naomi::::::" Kkkkkk dia wanga,,, ukufuna mpaka ndikuuze? Dikilira ,,, nkhani iyiyi ndinkafuna kukuuza tsiku lija ndinagundidwa ndi minibus lija ,,, just wait,,,. "

Naomi atamaliza zakezo Raja adaviyika ka PT kaja ndipo pamene amakaviyika adawerenga tanthauzo la PT lomwe ndi *~Pregnancy Test~*,,,, apa Raja mtima wake udalumpha ndi chimwemwe ndipo kukhosi kudali dyokodyoko chifukwa samayembekezera .

Patadutsa 5 minutes Raja adakavuula ndipo sadakaone ,,,, adangoyenda straight nkufika pa sitting room nkumupatsa mlamu wake ndipo adamuuza zoti alengeze mokuwa atayima pakati zomwe waonazo.

Febe adalandira ka PT kaja ndipo adafika pakati pa sitting room po kenako adati.

Febe:::::: *"Mphatso iyi yachokera kwa sister wanga okondedwa Naomi ndipo akuti ndiyitsekule nkulengeza zotsatira zomwe zili m'menemu,,,,. "*

Febe adakatembenuza kuti aone zotsatira ndipo amayi ake a Naomi ataona zoti ndi ka PT adachita kulumpha ndi chisangalalo ngakhale adali asadamve zotsatira ,,, adapita pamene padali Naomi nkumukumbatira uku akuti.

*"Congratulations" my daughter!!,,,, Ambuye ndi wabwino nthawi zonse ๐Ÿ™. "".*

Amake Naomi adagwada uku mzimayi akutsitsa misonzi ya chisangalalo ndipo adamuuza Febe kuti alengeze mwachangu.

Febe adatembenuza ndipo Naomi adali atamupanilira Raja uku misonzi ya chimwemwe ikutsika ndipo naye Raja mtima wake udali uli thi,thi,thi kuona kuchedwa.

Febe atangoona zotsatira nthawi yomweyo adagwa pansi uku akuyankhula.

*"Ambuye mwaloleranji zimenezi kwa mng'ono wanga!!!๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ"*

Onse::::::๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ!

Next,,,,,,,,Kodi mwati zikukhala bwanji?"

Ndi chani chomwe waona Febe choti mpaka kuyankhula choncho?"

Tiziti mimba ilipobe kapena eeeish๐Ÿ™†?"

Linda ndi Alick ndiye asanduka ma vampire uko kkkkkkk.

Kalikonse tikaona mu episode 23 yomwe izitchedwa.

*โ™ฅ๏ธMKAZI WA ABWANA โ™ฅ๏ธ*

Join my WhatsApp group today through this number,,, *0884849947*.๐Ÿฉธ

Or follow my page RAJAB MWANA OMUPEZA THE POET kuti nkhanizi zisamakuphonyeni.

Raja B loves you all good people with beautiful names ๐Ÿ™.

04/11/2023

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Ruth Chiyesa, Dan K Kacheche, Sara Sanyiwa, Ahmad Kamundi, Aidah Maganga, Mustapher Shukran, Gift Fusa, Yassin F White

*๐ŸฆšMKAZI WA MLONDA๐Ÿฆš**Episode 2๏ธโƒฃ1๏ธโƒฃ**By Raja B The Poet ๐ŸŽค.*Sponsored by.John Chimatiro.Emmanuel Mlenga.Khalid Sabiti.๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ...
18/09/2023

*๐ŸฆšMKAZI WA MLONDA๐Ÿฆš*

*Episode 2๏ธโƒฃ1๏ธโƒฃ*

*By Raja B The Poet ๐ŸŽค.*

Sponsored by.

John Chimatiro.
Emmanuel Mlenga.
Khalid Sabiti.

๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ

Mu episode 20 tidalekeza pamene Raja amalota ali ku khothi ndipo mlandu umaoneka zoti ukumukomera Linda choncho Raja adayamba kukuwa kutulo kuja.

*๐ŸฆšFast Forward ๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€*

Raja adayamba kukuwa kutulo kuja amvekere.

*"Ayi zisatero plz,,,,,,,, a judge sichilungamo chimenechi ๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธ๐Ÿ—ฃ๏ธ!!!"*

Naomi adachita kudzidzimutsidwa maka atamva kukuwa kwa mwamuna wake ndipo adayamba kumudzutsa.

Naomi:::::"Heyiiii Raja,,,, Rajaaa๐Ÿ—ฃ๏ธtadzukaa,!!! Kodi bvuto ndi chani?"

Raja adadzidzimuka uku akuyankhula kuti ayi zisakhale choncho.

Naomi adatsika pa bed nkumutungira madzi ndipo Raja atamwa madzi aja Naomi adayamba kumufunsa.

Nao:::::"Dear ,,, Kodi umalota chani?"

Raja::::"Swt,,,,, ndimalota zoipa,,, eti kulota tili ku khothi ndipo milandu yathu yonse itawakomera achina Linda ndi Alick. "

Naomi:::::" Chani??? Ambuye sangalole zimenezo,,,,. "

Raja::::::" Amen ๐Ÿ™ndipo kwa ife palibenso mtetezi wina koma Mulungu yekha basi."

Naomi::::::"Dia,,,, tadzuka ,,,, tiye tipemphere !!!! "

Apa onse adadzuka nkugwada pansi kuyamba kupemphera kumupempha Mulungu kuti awachotse mu msinga zimenezi.

*๐Ÿ™†Linda ndi Alick๐Ÿ™†*

Usiku umenewo Linda ndi Alick adakagona kumanda atauzidwa ndi msing'anga wina waku Mozambique ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ฟ amene adawauza zoti akagone kumanda ndipo akakaona mzukwa asakathawe mpaka mzukwawo ukachite zomwe ukufuna ,,,, iwo azikangouvomereza ndipo ukakamaliza zakezo mkuwasiya osawamenya ndiye kuti milandu yonse akawina,,,, koma ukakangowamenya,,,, amene ukamumenyeyo ndiye kuti sakawina mlanduwo.

Nthawi idali ikuthamangira 1 am ndipo kunali mdima wadzaoneni kumandako.

Linda adali atagona pa mtumbira moyang'anizana ndi Alick ,,, adawauza zoti akakafika kumandako palibe akamuyankhulitse nzake mpaka kukache.

Ngakhale Linda ankachita mantha komabe kamba ka mtima ofuna chuma adadzilimbitsa mtima mpaka pamene nthawi imathamangira 1: 30 am adangomva kuphotchola kosonyeza kuti chinachake chikubwera.

Linda adachita kutembenukira konko ndipo mtima wake unkagunda koposa ,,,, ali mkati mwa mantha chonchija adangoona chinthu choti mbeeee ,,,, chimene chimayenda kulunjika komwe adagona Alick.

Alick atachiona zoti chayandikira adatsinzina uku akuchita mantha ,,, chinthu chija chidayamba kumugwiragwira Alick kenako chinamukhudza pa lisani ndipo chidalowetsa dzanja mkati ,,,,, chitaona zoti ndi mwamuna chidachokapo nkupita pamene padagona Linda.

Chitafika chidamugwira pa chest ndipo chidayamba kuseweretsa mawere a Linda kenako chidamutsamira ndi kuyamba kupanga naye zina ndi zina mpaka chidachinya zigoli 6 koma osatopabe.

Linda adali akumva ululu wadzaoneni koma amalephera kuti achiletsa bwanji,,,,, mpaka chimamaliza cham'ma 4 kenako chidasowa .

Nthawi pamene imati 5 koloko mamawa ndi pamene achina Linda amatuluka m'manda muja koma Linda akumva ululu kwambiri moti amachita kukanika kuyenda ndipo Alick ndi amene adamuthandizira kuti ayendeko mpaka adafika mu msewu kenako adamugoneka pansi Mr Alick nkukatenga njinga yamoto nkumukweza.

*๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ฟ Mozambique ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ฟ*

Msing'anga uja atafika kunyumba kwawo adachita kulumpha ndi chisangalalo maka kamba koti amamufuna Linda kotheratu atangomuona ndiye adapanga dala ma plan oterowo ndi cholinga choti akagone naye mosavuta ,,,, apa msing'anga adachita kuyamika mkwapukwapu wake kuti wamuthandizira mpaka zigoli 6 .

*"Ubwino wake ku mlandu wawoko sindikakhalako ndipo akadzabweranso kuno ndidzawasowetsa iyaaaa.!! "*

Adadziyankhulira yekhayekha msing'anga uja uku akugona chifukwa cha kutopa.

*๐Ÿ”น๐ŸŽˆ Blantyre ๐Ÿ”น๐ŸŽˆ*

Naomi ndi Raja adali atamaliza kudya plus kusamba ndipo adakwera galimoto pamodzi ndi apongozi ake komanso azimulamu ake wautali ku Zomba.

*๐ŸŽˆ๐ŸŽˆZomba High Court๐Ÿฉธ๐Ÿฉธ๐Ÿฉธ*

Udali mlandu opatsa chidwi ndipo achina Linda ndi Alick adatulukira pa Benz ya lawyer wawo .
Linda adadzilimbitsa ngakhale adali akumvabe ululu koma adadziguza mpaka mkati m'mene adakakhala pa mpando moyang'anizana ndi a judge.

Mlandu udayambika ndipo lawyer wa Linda adayimilira ndikupempha kwa a judge zoti Mr Raja adathetsa banja lake kwa Linda chonsecho amusiyira chilema choncho bwalo la milandu liganizirepo pa ichi.

Judge amamvetsera mwachidwi nkhani ija kenako adapempha zoti lawyer wa Raja ayimilire kuti amudzutse Raja nkuyamba kufotokonza mbali yake koma Raja adati iyeyo alibe lawyer.
Khothi lonse litamva izi lidaseka maka poganiza zoti mlandu omwe ukukambidwawo ndi waukulu ndiye munthu nkubwera dala opanda lawyer.

Judge adaletsa phokoso ndipo adamuuza Raja kuti alowe mkachipinda alumbire kenako ayambe kufotokonza mbali yake.

Raja atalumbira judge adamuuza kuti afotokonze mbali yake ndipo Raja adati alibenso nkhani yoti angafotokonze.

Khothi lija lidasekanso ndipo judge adamufunsa Raja.

Judge:::::"Mnyamata,,,kuno sitidabwere kudzacheza,,,kodi zoti ukuthetsa banja ndi zoona?"

Raja::::" Ndi zabodza."

Judge::::::" Komatu mayi Linda afotokonza zoti ukuthetsa banja,,,tinene kuti akunama."?

Raja:::::"Zimenezo afunseni iwowo."

Judge:::::" Madam Linda,,,,Mr Raja akuti sakuthetsatu banja ,,,kodi muli ndi umboni oti akufuna kukusiyani?"

Linda:::::" Ayi koma iwowo bwanji amakandisiya kuno ku Zomba m'malo momakhala nane ku Blantyre konko?"

Judge:::::" Mr Raja,,,,nchifukwa chani munthu oti ndi mkazi wanu munakamusiya ku Zomba m'malo momakhala limodzi ku Blantyre?"

Raja:::::" Kodi nzoletsedwa mwamuna kumugulira mkazi wake malo nkumuuza zoti azikhala kumeneko?"

Judge::::::"Nkhaniyi ikuoneka zoti kwakula ndi kusamvetsetsana m'banja mwanu ndiye mlandu umenewu siupitiliranso ,,,watha,,,ulowe mlandu wina."

Judge adathetsa mlandu wa Linda ndipo udalowa mlandu wa Alick ndi Naomi.

Judge,:::::" Mr Alick ,, lawyer wanu akuti inuyo mukufuna kubwelerananso ndi mkazi wanu Naomi,,,ndi zoona?"

Mr Alick:::::" Eya ."

Judge ::::::" Madam Nao,,,amuna anu akuti akufuna mubwelerane,,,inu muliuzanji bwalo lino?"

Naomi:::::"Your majesty,,,kodi ine ndi Mr Alick banja lidatha?"

Judge::::::" Mr Alick yankhani,,,akufunsatu ,,,kodi banja lidatha?"

Mr Alick::::::"Ayi."

Naomi::::" Nanga nchifukwa chani akuti tibwelerane anthu oti banja silinathe?"

Judge::::" Yankhani Mr Alick."

Mr Alick::::::" Basi ,,kungoti ineyo ndimaona ngati lidatha."

Apa khothi lonse lidakuwa kuli kuipidwa nazo mbwelera zomwe amakamba Mr Alick ndipo judge adangoti.

Judge:::::"Zikuoneka kuti nkhani zanuzi ndi zachibwanabwana ,,,Mr Alick komanso madam Linda khothi lino likulamula kuti mulipile 100,000 kwacha aliyense mwa inu awiri chifukwa chobweretsa nkhani zopanda pake ,,,mwatitayitsa nthawi,,,,mlandu watha."

Apa Mr Alick komanso Linda adangoyang'anizana ndipo atafika kunja lawyer wawo adawauza zoti amulipile chifukwa choti amuputsitsa.

Mr Alick ndi Linda adagulitsa njinga yamoto yomwe adali nayo nkulipila milandu yonse.

*๐Ÿ”นBlantyre*๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น

Naomi ndi Raja atafika ku Blantyre adagwirizana zoti awamvetse kuwawa achina Linda chifukwa atasa kokwanira.

Raja:::::",Nao,,,apa ndiye tawagadabula ku khothi kujatu kkkkk."

Naomi:::::" Ndipo ndiye zoona,,,anthu amene aja tikanangowavomereza mlandu umene uja ukanatigwera chifukwa even judge uja adali mbali yawo."

Raja:::::" Sure,,,ndiye pokana zoti tizilimbanalimbana that's why ndawakhapila kosathwa."

Naomi:::::;" Ndiye tipange bwanji chifukwa mwina tikuyankhula pano ali mnjira akubwera paja alibe manyazitu."

Raja::::::" Ndisiyire ine zimenezo,,,,kodi zomwe ndinakuuza usiku zija wakonza?"

Naomi::::::"Kwambiri,,,,,."

Raja:::::" Nice one,,,,let's do it."

*๐Ÿ”น4 hours later๐Ÿ”น*

Linda ndi Alick adafika kunyumba kwa Raja ndipo adatsitsa zikwama zawo pa gate kenako wa minibus adapitilira.

Linda adayesera kugogoda pa gate koma palibe ankayankha.

Atagogoda kwa nthawi yaitali kudatulukira guard wapamalopo ndipo Linda adafikira kumulandira ndi maphunzo.

Linda:::::"Kanyimbi wa munthu iwe,,,,kabuwaza kaligondo wachabechabe ,,,tachioneni vimaso,,,,zooona ukatidikilitse ife mabwana ako panja pa gate zoona?"

Guard::::::" Heyiiii,,,amayi Inu dzipatseni ulemu ,,,ine si wantchito wanu,,,,nyumba ino adagulitsa ndipo bwana Raja anyamuka lero mwinanso pano akwera kale ndege."

Linda:::::" Chani??? Apita kuti?"

Guard;:::::" Sindikudziwa ,,eyiii tathawani apa akubwera eni kumpanda kuno."

Linda adasuntha zikwama ndipo boss wanyumbayo atafika adafunsa za alendowo koma guard uja adangoyankha mwamwano nati.

*"Bwana musadandaule ndi awa ndi amasikini onka napempha."*

Linda atamva adafuna ampatse mbama guard uja koma adamuuziratu kuti akangoyerekeza amuponda ,,,kuli bwino achoke mwansangansanga.

Linda ndi Alick adachoka ndipo amati kupita ku Lodge ya Raja ogwira ntchito kumaloko amangomuyankha mwano kumuuza zoti bwana Raja adagulitsa chilichonse ndipo apita kunja.

Linda ndi Alick ataona zoti nthawi ikupita ndipo dzuwa likulowa adangoganiza zobwelera ku Zomba ndipo adayimika galimoto back ku Zomba.

Atafika pa Depot adatsika ndipo adayenda koma atatopa chifukwa adalibiretu ndalama iliyonse.

Atafika pa gate la nyumba yawo adangoona ma guard a G4s atatu ali pa gate po uku agalu awo ali pambalipa.

Linda adawafunsa kuti nchifukwa chani akupezeka ku nyumba yawo koma ma guard aja adati.

Guard:::::"Amayi inu,,,nyumba zonse zili mu mpandamu zidali za Mr Raja ndipo adali atazigulitsa kwa wamkulu wa asilikali ku Changalume Barracks choncho ndi awo akutsitsa katundu kumpanda ko,,,chifukwa mr Raja adawayimbira kuti akhonza kudzalowa lero,,,tichokereni apa tili ndi zambiri zochita."

Linda adangoti kakasi ndipo Mr Alick adangoti..........

Guard;:::::: *"Heyiiiiii mzimayi iwe ,,,pitani muzikakomokera uko ife tilibe chifundotu tingokumasulirani agalu apa,,,,pope tiye lumaaa.๐Ÿถ๐Ÿถ!!!"*

Linda:::::: Thiiiii๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ.

Next...... Kkkkkkk koma zili kuno bwerani mudzaone .

Linda ndiye wadyetsa ulere kwa msing'anga kuno ๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ.

Achina Linda alibiretu kokhala koma Raja ndi Naomi inuyo mudzangosowa kkkkkk.

Kalikonse tikaona mu episode 22 mawa lino.

Join my WhatsApp group today through this number,,, *0884849947*.

Or follow my page RAJAB MWANA OMUPEZA THE POET kuti nkhanizi zisamakuphonyeni.

Raja B loves you all good people with beautiful names ๐Ÿ™.

*๐Ÿ’ฅ MKAZI WA MLONDA ๐Ÿ’ฅ**โ™ฆ๏ธ Episode 14๐ŸŒ**By Raja B The Poet ๐Ÿ”น*๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”นโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธMu episode 13 tidaona Dr ...
13/09/2023

*๐Ÿ’ฅ MKAZI WA MLONDA ๐Ÿ’ฅ*

*โ™ฆ๏ธ Episode 14๐ŸŒ*

*By Raja B The Poet ๐Ÿ”น*

๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”น๐Ÿ”นโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธโ™ฆ๏ธ

Mu episode 13 tidaona Dr Abel ali busy ndi Naomi mpaka kumubaya jekeseni ogonetsa ndipo atamubaya adakhoma mu chipinda chomwe amapangiramo operation kenako ada....

*๐Ÿ”นFast Forward ๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€๐Ÿฅ€*

Doctor Abel adali busy maka ndi kuoneka bwino kwa Naomi ndipo adabalalika mpaka adaganiza zoipa ,,, adavula trouser lawo kenako adamugwira mwendo umodzi nkuwutanula ,,,, apa mtima wa Dr Abel udali ukukankha mwazi maka powona miyendo ndi ntchafu zili psuuu .

Dr Abel adakolopola boxer wawo ndipo akuti azimutsamila Nao kudamveka kugogoda pa chitseko.

Mwansangansanga adavala ndipo adatsika pa bed nkutola trouser lija and adalivala mwa fast kenako adavomera .

Dr Abel adatsekula ndipo adawaona azungu amene adabwera kudzayendera chipatalacho ndi kumathandiza anthu pa mavuto osiyansiyana.

Azungu aja adali odabwa ndi momwe amaonekera Dr Abel amene adali ndi phuma kwambiri komanso amatuluka thukuta.

Mzungu wa chizimayi m'modzi adapita pafupi ndi Nao ndipo adawafunsa Dr Abel za bvuto lomwe wagonekedwa nalo Naomi ndipo Dr Abel adati Naomi ali ndi bvuto la uchembere.

Mzungu uja mpaka adawafunsa Dr Abel kuti ndiye bvuto limenelo mpaka kumubaya jekeseni ogonetsa?

Dr Abel adangoti mutu zyoli ndipo mzungu uja sadalimbane nawo koma kuvala ma groves nkuyamba ntchito yawo ,,,, kenako atamaliza adamudzutsa Nao amene adali atafooka.

Dr Abel adamupelekeza Naomi mpaka pamene padakhala Raja kenako onse adatengana nkukafika pamene padali Linda.

Raja adamuuza Alick kuti iwo akupita and ngati akufuna thandizo ndiye kuti Alick yo awasiye azimayiwo iyeyo azikagwira ntchito ya ulonda wake.

Linda ankafuna kuyankhula koma Mr Alick adamuletsa ndipo Raja adangomuuza Nao kuti tiyeko.

Raja atafika ku Lodge ya Jazeera sadachedwe koma kubwelera ku Blantyre kumene adali akukalongosola zina ndi zina maka zokhudza ma truck amene adali paulendo opita ku Botswana ndi katundu ,,,, business imene kwa iyeyo idali yovuta chifukwa samazidziwa kuti zimayenda bwanji choncho adamuuza Naomi kuti ndi amene aziyendetsa zonse zokhudza ma transport.
Naomi sizinamuvute si nanga ankaona zomwe amachita Mr Alick pamene adali mwini wa zinthuzo.

*โ™ฆ๏ธKAMUZU CENTRAL HOSPITAL ๐Ÿ”น*

Amake Linda ataona zoti zinthu sizili mbali yawo adawakodolera pambali Mr Alick ndipo adati.

Amake Linda::::"Kodi bambo,,, ndiye kuti mungozisiyasiya basi?"

Mr Alick:::::"Sindingangozisiya mophweka chonchi amayi."

Amake Linda:::::"Eyaaa bola pamenepo,,, chuma chimenechi chibweleranso m'manja mwathu,,, ndili ndi ganizo ngati mungagwirizane nalo. "

Mr Alick:::::" Ndiuzeni ndipo ndipanga chilichonse. "

Amake Linda:::::" Kwathuku kuli msing'anga osangoti msing'anga koma uyoyo ndi katundu,,, musachedwe ,,, tapitani ndipo mukafotokonze zonse ,,, mudzandiyamika kutsogolo. "

Mr Alick:::::" Eya,,, amayi zikomo,, odi ndimutsanzike kaye Linda. "

Apa Mr Alick adapita pa bed la Linda ndipo adamuuza zonse ndipo Linda adati.

Linda:::::" Pita ,, koma choti udziwe ndi choti ine sindikufuna kukafikira kumudzi plus nyumba ya rent. "

Mr Alick:::::" Ndiye ukafikira kuti? Taona ndi m'mene zinthu ziliri Linda. "

Linda::::" Basi pita,,, ndiye ifeyo ukuganiza kuti tikafikira kuti tikatulutsidwa? "

Mr Alick:::::" Ndikamba naye Raja,,, ndi chitsiru chivomera kutipatsa nyumba yabwino,,, then ndikuuza. "

Linda::::;;" Chabwino,,, komatu m'mutumu ndiye mwanyasa ,, ulibe ya ku saloon?"

Mr Alick:::::"Ndiye ndikaitenganso kuti? Apapa yomwe ndili nayo ndi ya transport,,, osadanda,,, zinthu ziyenda wamva? "

Linda adagwedeza mutu ndipo Mr Alick adanyamuka.

Pambuyo pake Linda adayamba kuyankhula ndi mayi ake.

Linda:::::"Amaa,,, apapa ndikufuna tituluke tipite kwa Raja ndikamupepese,,,, iye uja ndikumudziwa ine ,,, sangandikane ,,, Raja ndi opusatu. "

Amake Linda::::::",Yes ,,, upange zomwezo,,, ena asadatole,,,, ubwino wake ka chithumwa ndinakupatsa kaja umakasungabe ,,, popita ukavale mchiuonomo wamva? "

Linda:::::" Eyaaaa amaaa,,, tawauzeni adotolo kuti tikufuna tizipita,,, kodi achina Grace aja ali kuti?"

Amake Linda:::::::" Ndinawaonatu panjapo akuimitsa galimoto,,, kodi sadakutsanzike? "

Linda:::::" Ayitu,,,, moti andithawadi poti zinthu zabvuta? Asiyeni,,, zoti Raja ndi wanga sakudziwa? Ndidzawaonetsa kuti ndi ine Lix mtsikana ovuta. "

Apa amake Linda adawapempha adokotala ndipo adawalola kutuluka .

Linda ndi amayi ake atatuluka adayimba phone kumuyimbira Raja ndipo adamupempha zoti amulole kuti afikire kaye kwawoko pomadikilira Mr Alick.

Raja adawalola onse ndipo adawatumizira ma transport mpaka adakafika ku Blantyre.

*๐Ÿ’ฅMalombe,,,,, Mangochi ๐Ÿ’ฅ*

Mr Alick atafika kwa msing'anga uja nkumufotokonzera zonse msing'angayo adati zimenezo nzotheka kwa iye,,, adawauza Mr Alick kuti pa 2 days chuma chonse chibwelera kwa iwo ndipo adawauza kuti asankhe ma options awiri.

Ng'anga Imran:::::"Baba,,, zangani chindu chimosi mwa sindu siwirisi. "

Mr Alick::::::" Yes,,, ndiuzeni ndipo ndisankha."

Msing'anga Imran:::::"Pakati poti mundu ameneyu ape ndi kuwutuka mizala muzanga chani?"

Mr Alick::::::"Mwati ape ndiye kuti chani? "

Ng'anga Imran::::::" Ndikutandausa kumwalira. "

Mr Alick::::::"Ameneyu angofa ,, kapena ayi,,, akayambe misala kenako ine ndikawadinditsanso plus kusintha mapepala aja kuwayika mdzina langa kenako adzafe. "

Ng'anga Imran::::::"Fenkesi,,, Inu baba mumaganisa,,,, eni mtera uyu ,,, mukakavika mukatape panzi lake ndipo mukakutulire umu momwe muli doti lakumanda,,, ndiye poti mukuvuna apengezo ndiye popita kubulantayako mukaime kaye ku somba ku mentolo kwa andu amizala kuja,,,, mukapese mpata kapena mtauni momwemo mukapese wamizala amene ali ndi mamina pambuno,,,, mukatenge mamina amenewo ndiye mukazakanyize ndi awa kenako mukawatilire mu sakudya,,, mwamfa? "

Mr Alick:::::" Eya ndamva baba,,, ndikapanga. "

Apa msing'anga Imran adawapatsa mankhwala Mr Alick amene adafika mu Zomba ndipo adakhotera ku mental komwe kudali azinzawo amene ankapangana nawo madhilu ,,, atawapempha adawalola ndipo adalowa mwa amisala muja nkuyamba kuyang'anayang'ana amene ali ndi mamina pa mphuno ,,, kenako adamupeza nkumupukuta nkuwaponya mu msupa basi wautali ku Blantyre.

*๐Ÿ’ฅBlantyre๐Ÿ’ฅ๐Ÿ’ฅ*

Naomi adayamba kumupempha Raja kuti apite limodzi kwawo ,, Raja sadakane ndipo adamuuza zoti mawa adzakhalira limodzi koma Raja adamufunsa kaye.

Raja:::::"Madam Naomi,,, kuchipatala kuja akuti muchite changu pasathe mwezi musadakhale pamodzi ndi mwamuna ndi cholinga choti malo apangidwa operation wo akufunika asadapole akhudzidwe kaye ndi mbewu ya abambo,,, ndiye plan yanu ndi yotani? "

Naomi:::::" Ndilibe plan iliyonse. "

Raja:::::" Kapena mubweleranso kwa Mr Alick? "

Naomi:::::" Komano Raja,,, bwanji ukufuna ndikhumudwenso ,, zoona ukandifanizirenso ndi zobwelera kwa Mr Alick? "

Raja:::::" Sorry,,, ndiye kapena mawalo tikukapanga za mwamuna kwanuko? "

Naomi:::::" Kodi paja usaiwaletu zoti sindinapemphe lonjezo lomwe tinagwirizana lija,, ndiye mawa ndikufuna ndidzakuuze. "

Raja:::::" Chabwino madam. "

Naomi adatuluka koma sadapite patali adamyata pafupi kuti amve zomwe aziyankhulana ndi KB.

KB:::::"Aise Raja,, Kodi umamukonda Naomi?"

Raja:::::"Kwambiri,,, ndipo kwa over."

KB::::::"Ndiye siukuona kuti nthawi yake ndi ino? Muuze usachite kudikilira. "

Raja:::::" Aise KB,,, mwina Naomi sangandikonde ndiye ndikuopa kumukhumudwitsa,,, akhonza kumaona ngati ndikufuna kutengerapo advantage pa chuma changachi. "

KB:::::" Ayinso,, koma ukudziwa zoti Naomi amakukonda ndipo amangodikilira kumva mau achikondi kuchokera kwa iwe? "

Raja:::::" Zoona? ๐Ÿ˜ณ"

KB asadayankhe nthawi yomweyo kudatulukira Linda amene adafikira kugwada pafupi ndi Raja ndipo adayamba kupepesa uku atamugwira mwendo Raja ,,,.

Linda adalira mpaka misonzi idanyowetsa trouser la Raja ndipo adati.

Linda::::::"Raja,, ndikudziwa zoti ndinakulakwira,,, koma sikufuna kwanga ayi,,, kungoti Alick uja ndi amene adandipangira mankhwala kuti ndizerezeke naye chonde ndikhululukire mwamuna wanga. "๐Ÿ˜ญ

Raja::::::"Ukufuna ndipange chani? "

Linda:::::" Tibweleranenso chonde mwamuna wanga,,, ndi iwe wekha basi. "

Raja::::" Udadziwa bwanji zoti Mr Alick adakupangira mankhwala ndipo wadziwa liti? "

Linda:::::" Dzulo ,,,, ndinamumva akuyimba phone kumuuza msing'anga wakeyo zoti amukonzerenso mankhwala oti abwelerane ndi Naomi. "

Naomi atamva zimenezi mtima wake udakwera mpaka mkamwa kutentha ndipo adafuna kupita pompo koma akuti azinyamuka adawaona mr Alick akumulandira mtsikana wantchito mbale ya zakudya kenako adawaona akutulutsa zinthu mu thumba la jekete lawo ndipo adathira zinthu mu mbale muja kenako adayamba kupititsa mbale ina kwa Raja .

Atafika adalowa ndipo adamupeza Linda ali chigwadirebe kenako adapereka ulemu nkupereka mbale ya chakudya ija kwa Raja amene adangofikira kuvundukula ndipo ataona zoti ndi ๐Ÿฐ cake adanyema nkamwa ndipo Naomi ada.......

Next,,,,,, kkkkkkkk guys uku kuli ntchito ndipo mu episode 15 muli maferano.

Kodi Raja amuvomere Linda?

Nanga tinene kuti mission ya Mr Alick yatheka poti Raja wafikira kudya cake uja? "

Anthu aphana umu.

Kodi Raja wachita mistake powalola onse kumakhala mu mpanda umodzi?

Join my WhatsApp group today through this number,,, *0884849947*.

Raja B loves you all good people with beautiful names ๐Ÿ™.

Address

Katuli
Mangochi

Telephone

+265999334636

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Raja B The Poet posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Establishment

Send a message to Raja B The Poet:

Share