27/09/2026
THE DAY I MET MY FIRST LOVE
PART 8
STORY DONE BY ASODZI COMEDY
Bambo ake a Lunah anamuyang’ana mwana wawo, kenako n’kuyang’ana akazi awo.
“Mwamva zomwe akuyankhula mwana wanu?” Anafunsa bambo aja akazi awo.
Mayi: “Iii, iwenso Lunah, takhala chete apa. Tseka kukamwa kwakoko.”
Lunah: “Palibe zimenezo. Ndine wamkulu pano, ndikudziwa pakati pa chabwino ndi choipa. Ndaphunzira school, ndamaliza. Kunatsara ndi kukwatira, ndipo uyu ndiye mamuna wanga. Zili ndi inu kuvomera kapena ayi, koma chisankho ndapanga kale.”
Bambo: “Hey Lunah, please tuluka panja ndi munthu nzako amene ukuti ndi mamuna wako. Koma chomwe ungadziwe ndikuti ukatuluka panja ukafunefune kuli makolo ako. Hope, tuluka panja.”
Ndinadziwilatu kuti nkhani ija yakula tsopano. Panalibe munthu amene amawonetsa mano pa malo paja. Mwakachetechete ndinatuluka panja osayankhula chilichonse. Mosakhalitsa ndinangoona Lunah akundithamangira, ndipo tinatuluka pa gate limodzi.
“Hey Lunah, walimba mtima mpaka kutuluka panja?” ndinafunsa.
Anandiyang’ana modabwa Lunah.
“Yaa, ndalimba mtima. Kapena sunakonzeke kukhala ndi munthu ngati ine?”
“Aaa ayi dear, ndine wokonzeka ndithu. Kungoti ndili ndi mantha kuti makolo ako angapeze njira yoti ndisowe mtendere, ndi cholinga choti ndikulephere basi.”
Anamwetulira Lunah.
“Aaa honey, osadandaula zimenezo. Amenewo sangapange china chilichonse, bola adziwa kuti ndili ndi iwe kusiyana ndi kungothawa. Usadandaule china chilichonse. Kuyambira lero tidzipangira zinthu limodzi ngati banja. Ntchito ikapezeka, ndinkhonza kuyamba kugwira kuti tidzithandizana kupanga zinthu.”
“Oky chabwino dear. Pamenepo wayankhula mawu olimbitsa mtima. Osadandaula, ntchito ipezeka ndithu. Ndiyesa kuwafotokozera nzanga.”
“Oky chabwino honey,” anayankha Lunah.
Tinayenda njira yonse, nkhani zathu zili pakamwa, kwinaku ndikulingalira za malo omwe ndimakhala ngati Lunah angawakonde.
Mu mtima mwanga ndinali ndi manyazi poti room yomwe ndimakhala munalibe katundu wokwanira. Monga ine munthu wongofika kumene ku Joweni, ndinali ndisanazitolele bwino zinthu zanga.
Titafika ku malo omwe ndimakhala aja, ndinatsegula mu room mwanga ndikuyankhula:
“Sorry dear, pa nkhomo ndi pano. Nyumba yanga ndi imeneyi, yamalata okhaokha.”
Anamwetulira Lunah akuyankhula:
“Mmh dear, osayiwala kuti chara chimakanda pomwe chikufikira. Usakhale moyo wopanikizika chifukwa cha ine. Ndinakulora chibwenzi ukugulitsa mango, pano ukugwira ntchito pa filling station. Cha bwino ndi chiti? Moyo wako wasintha than before. Tawona, m’nyumba mwako muli TV yomwe kumudzi kuja unalibe. Pang’ono ndi pang’ono Mulungu azatidalitsa.”
Ndi mawu omwe anayankhula Lunah, mtima wanga unali zii.
Tinalowa mu room muja tonse ndikukhala pa bed kumacheza. Tili pakati pa kucheza, Lunah anandiyang’ana modabwa kwambiri, kenaka anafunsa funso:
“Hey dear, tsono ndi chifukwa chani unasintha dzina, kukhala Yusuf? Kapena umawopa Adad?”
“Aaa ayi dear. Malo aja ndimagwira ntchito aja, eni ake ndi Amwenye. Nde amakonda kulemba ntchito ma Muslim, moti dzina limene lija anandipatsa ndi nzanga ogwira naye ntchito.”
“Oooh, chee Yusuf, komatu lakukhala dzinalo,” anayankhula akuseka Lunah.
Ndinamumenya mbama mwa chikondi.
“Ukhalike dear. Komanso nthawi yatha apa, ndiphike kuti udye kuti ukhale ndi mphamvu,” ndinayankhula ndikudzuka pa bed paja kupita pomwe panali hot plate stove pa mbali pa bed pomwe paja.
Ndiyamba kuphika, Lunah atangogona pa bed paja akuseweletsa foni yake kwinaku tikucheza.
Ndinatenga foni yanga kulowa WhatsApp kuti ndiwone ma messages, koma ndinali odabwa kuona Lunah atayika status chithunzi chomwe anandijambula ndikuphika, ndipo sindinkadziwa.
M’munsi mwake atalemba mawu oti:
“Amalume anu akuphika kuti ndidye, kenaka nawo adye.”
Ndinamuyang’ana Lunah. Anayang’ana kumbali akumwetulira.
Kunena zoona, pa nthawi imeneyo chikondi chinali chitakula pakati pathu.
Anadzuka pa bed Lunah kubwera kudzandithandiza kuphika. Titamaliza kuphika tonse, tinayamba kudya tikupitiliza ndi macheza athu.
Tinacheza kwa nthawi ndithu, kenaka tonse tinagona monga banja.
Kutacha m'mawa, ndinalawilira kusamba kukonzekera ulendo waku ntchito.
Pa nthawi imeneyo Lunah anali atadzuka kale, koma anangokhala chogona pa bed.
Nkhawa yomwe inali mu mtima mwanga inali yoti Lunah analibe chovala china chilichonse kupatula zomwe anavala zija, poti china chilichonse anachisiya kwa sister wake uja.
Ndinalongedza chakudya changa chokadyera ku ntchito m’chikwama changa, kenaka ndinatulutsa card la ku bank ndikumupatsa Lunah.
“Hey honey, card la ku bank ili. Upita pamusipo pali pep store, ukagule zovala, ma dress awiri, malaya awiri ndi ma skirt. Zina ukawona wekha. Ukachotsemo 700 rand, PIN ndakutumizira pa WhatsApp,” ndinayankhula.
Anamwetulira Lunah.
“Ooh zikomo kwambiri dear. Tsono pamenepa ubwera nthawi yanji?”
“Aaa, tikumana 4 koloko madzulo. Ukhale ndi tsiku lopambana. I love you, byeee,” ndinayankhula ndikutuluka panja.
Lunah anadzuka pa bed kundigwira malaya.
“I love you too,” anayankha Lunah akundipatsa kiss, kenaka anandisiya kuti ndituluke panja.
Ndinanyamuka ulendo waku ntchito ndili ndi chimwemwe kwambiri. Ndinkangonva kuti chikondi ndi chinthu cha bwino, koma pa nthawi iyi ndinatsimikiza ndithu.
Ndinafika ku ntchito ndi nkhope ya chimwemwe kwambiri kuposa masiku onse.
Nditangofika ku ntchito kuja, ndinayenda straight kupita mu office kuti ndikasayine nthawi yomwe ndafika ku ntchito kuja monga mwa nthawi zonse.
Koma ndili pakati posayina, bwana wamkulu analowa mu office muja.
“Aaaa, kodi ndi Hope? Sorry, usasayine. Lero sukugwira ntchito. Kalata yako iyi,” anayankhula bwana.
Mtima wanga unagunda.
“Aaa bwana, ndalakwitsa chani kuti lero ndisagwire ntchito?” ndinafunsa, mtima wanga ukugunda.
“Aaa, china chilichonse chalembedwa mkatimo. Ukawerenga ukakafika ku nyumba,” anayankha bwana aja.
Ndinatuluka mu office muja, mtima wanga ukuyaka moto.
Nditafika panja, ndinangoti gululu ndi Ahamadu, mnyamata anandipezera ntchito uja.
Anandikokera pa mbali Ahamadu kupita kuseri kwa filling station ija.
M’maso mwanga munali misozi itayamba kutsika.
“Aaa man Hope, kodi chachitika ndi chani? Dzulo madzulo kunabwera abambo ena ake owoneka achikaladi choncho. Ndinawamva akuyankhulana ndi bwana, koma amatchula dzina lako ndi police. Kungoti ndinali busy, kunali kovuta kumva bwino bwino. Koma amawoneka kuti anali olusa kwambiri,” anayankhula Ahamadu.
Ndinadziwilatu kuti omwe amanena aja angakhale bambo ake a Lunah.
Ndinalibe mphamvu ina iliyonse yoti ndikanatha kumuyankha.
Ndinamuyankha Ahamadu:
“Esh, sorry bro. Ndilore ndipite ku nyumba. Ndikufotokozera china chilichonse mtima wanga ukakhala m’malo.”
“Oky chabwino bro, uyende bwino. Ticheza pa foni. Koma osadandaula china chilichonse, chikhala bwino bwino,” anayankhula Ahamadu mondilimbitsa mtima.
Ndinasiyana ndi Ahamadu kubwerera ku nyumba.
Nditafika ku nyumba, ndinapeza Lunah kulibe.
Ndinadziwilatu kuti wapita kukagula zovala zija.
Ndinakhala panja kumudikirira poti m’nyumba munali mokhoma.
Ndinakhala nthawi ndithu panja paja, kenaka ndinangomuwona Lunah akubwera, ndipo jumbo yake ili ku manja.
“Aaaa Honey, nthawi yomweyo wabwera ku ntchito kuja? Mesa umatiuma weluka 4 koloko madzulo?” anafunsa modabwa Lunah akundiyang’ana, maso anga poti anali atafiyira kwambiri.
Ndinapusa mutu osayankhula china chilichonse. Ndinatenga kalata ija kumupatsa, yomwe inali itapinidwa bwino bwino.
Analanda kalata ija Lunah. Anatsegula chitseko, tonse tinalowa m’nyumba, koma nkuti naye akuwoneka okhumudwa kwambiri.
Anaitsegula kalata ija ndikuyamba kuwerenga mokweza mawu, ndipo inalembedwa motere:
“Hello Yusuf,
Ntchito yako yatha pazifukwa zingapo. Choyamba, unanama dzina lako kwa ine. Ndadziwa dzulo kuti ndiwe Hope. Chachiwiri, ulibe mapepala olongosoka ogwirira ntchito pa malo ano. Of course, ndimalemba anthu ntchito opanda passports, koma iwe uli ndi mulandu womwe ungapangitse police kufika pa malo ano. Mapeto ake ndi kulipira ndalama zambiri komanso kuwononga mbiri chifukwa cha iwe.
Zikomo kwambiri. Ndiwe mnyamata wa bwino. Tidzakuyitana nthawi ina tikadzafuna anthu.”
Anapumira m'mwamba Lunah.
“Aaa, ntchito imatha chonchi abale? Ndikuwona ngati wina wake samakufunira zabwino ndi amene wakunenera ma bodza,” anayankhula Lunah.
Ndisanayankhe, anayiwerenganso kalata ija.
Anapitiliza kuyankhula Lunah:
“Aaa ayi, nkutheka makolo anga anapita ku ntchito kwako. Akuyesera kupeza njira yoti iwe ndi ine tizunzike, ndi cholinga choti ndibwerere ku nyumba.”
Ndinamuyankha Lunah:
“Yaa, ndi makolo ako omwe apanga zimenezo. Koma andilakwira ntchito ina ndiipeza kuti pano?”
Anapukusa mutu Lunah akuyankhula:
“Osadandaula sweetheart. Mulungu ndi amene amadziwa tsogolo la munthu. Ndine wokonzeka kukhala nawe mu nyengo zonse. Usaiwale kuti golide samakhala golide asanadutse mu ng’anjo ya moto.”
Anayankhula Lunah akupukuta misozi yanga ndi malaya ake.
---
MIYEZI IWIRI INADUTSA CHONTHERO TCHITO IJA.
Moyo unasintha kwambiri.
Masiku onsewa ndinali ndikuyesetsa kusaka ntchito koma osaipeza.
Ndimayima m'mbali mwa msewu nditanyamula chikatoni nditalemba mawu oti:
“I'M LOOKING FOR A JOB — ANY KIND OF JOB.”
Koma masiku onsewa palibe amene amanditenga ngakhale kukagwira garden boy kwa tsiku limodzi lokha.
Pang’ono ndi pang’ono ndalama zomwe zinali ku account kwanga zinali zikutha.
Pa nthawi imeneyo, Lunah akumagwira maganyu ochapa zovala m’nyumba mwa anthu, ambiri anali a Malawi amene amakhala okha komanso omwe zinthu zimawayendera.
Kunali zovuta kumuletsa Lunah kuti asamagwire maganyu malingana ndi moyo umene unaliri pa nyumba.
Anali madzulo.
Ndinanyamuka ulendo waku nyumba kuchokera kosaka ntchito. Mutu wanga sunali kugwira ntchito bwino malingana ndi mavuto azachuma omwe anali pakati panga.
Ndinafika ku nyumba ndi nkhope yokhumudwa ngati mulenje wobwera chabe ku uzimba.
Ndinalowa m’nyumba ndinamupeza Lunah atagwada pansi kupemphera.
Mkati mwa pemphero lake munali kumveka dzina langa.
Ndinadzimvera chisoni, poti naye Lunah nkuti usiwa utamusawutsa. Tsitsi lake anali atameta chifukwa chosowa chisamaliro.
Ndinakhala pansi osayankhula china chilichonse powopa kumusokoneza mapemphero aja.
Kenaka ndinangomva:
“Amen.”
Kusonyeza kuti wamaliza kupemphera kuja.
Anandiyang’ana Lunah ndi nkhope yokhudzika.
“Mwaswera bwanji? Kaya wayenda bwanji lero kosaka ntchito?” anafunsa Lunah.
“Aaa ndaswera bwino dear. Kosaka ntchito ndayenda bwino ndithu poti ndabwera ndi moyo, koma ntchito, ngakhale ganyu, sindinaipeze.”
“Oky sweetheart, koma uti ukawona tikhala moyo umenewu mpaka liti? Ndikudutsa m'mayeso akulu dear. Ndimawona ngati kuli bwino tidzipita kumudzi. Bola kumazunzika kwathu kusiyana ndi kuno. Ganiza mofatsa chonde, ndalama zisanathe.”
“Honey, tidzikatani kumudzi? Nanga ukuganiza kuti anthu adzati chani ndikapita opanda kathu?” ndinafunsa Lunah.
Andiyang’ana, nkono wake akundisisita ku nsana, kenaka anayamba kuyankhula:
“Dear, ukakhala m'moyo uno, ukamapanga ziganizo zako usamati anthu adziganiza kuti chani. Panga zinthu zolingana ndi nyengo yako.
Pakati paja ndimagwira ntchito yochapa kwa anyamata aja, koma pano asiya kundipatsa ganyu chifukwa choti ndawakana chibwenzi.
Sorry, sindinkafuna kukuudza izi, koma ndikungofuna udziwe nyengo zomwe ndikudutsamo monga mkazi wako.
Tiyeko tidzipita kumudzi. Sunatsanzike munthu kuti ukagule galimoto.”
TIKUMANENSO MU PART 9.
MWAKOMA NONSE ❤️
STORY DONE BY ASODZI COMEDY