07/02/2025
Kodi Nohaata Seven yemwe adabeledwa ndalama ndi Tamia Ja (allegedly) ndi ndani?
Nohaata Seven yemwe amadziwikaso kuti Hatsa ndi Mpondamatiki yemwe adatola chikwama ali wachichepere ndi maluso ake opanga ma website.
Hatsa adatutumutsa anthu pomwe adapanga website ya Nde'feyo Entertainment pomwe adali ndi zaka 13 zokha zakubadwa.
Pomwe akukwanitsa zaka 23 chaka chino, Katswiriyu wapanga zikuluzikulu zomwe mwazina ndima website amakampani odziwika bwino ku Malawi kuno kuphatikizapo ya Mikozi Network.
Tochonga tomwe timaoneka pa tsamba la mchezo (blue badge) kwathu kuno adapanga ndi mkulu yemweyu. Ndipo zidawulurika kuti page ya Phyzix, Piksy, Tsa Leo, Dr Namadingo ndi Dr Lazarus McCarthy Chakwera adapangitsa ndi yemweyu kuti akhale ndi blue badge.
Pakadali pano, Hatsa adakhazikitsa kampani yake yaikulu yotchedwa PayChangu yomwe anthu amagula ndikugulitsa katundu mosavuta.
Kampani imeneyi siyamasewela chifukwa idavomeledwa ndi banki yaikulu ya Reserve Bank of Malawi. Woyimba wa Hip-hop, Episodes wagwiraposo ntchito ku kampaniyi ngati wamkulu woyang'anira zamalonda (sales and marketing officer)
Mpondamatikiyu Ali ndi chuma chochuluka ndipo oyimba onse akuwonetsa timagalimoto tawo pamowa Ali naye kutali kwambiri.
Mwazina, mkuluyu Ali ndi choyendera chapamwamba chotchedwa Ford Ranger komaso amakhala ku chi mansion chapamwamba kwambiri.
Inu ma baddie ndi akazi onse olusa ndi chuma cha mwana wamzanu musavutike ndikufufuze nambala yake ya phone poti ndiwokwatila kale. Ndipo mkazi wake si mkazi wamba, ndi woyimba wotchedwa Bongie Melon yemwe adamubelekera mwana m'modzi.
Side note:
Komabe anthu akuti Ali ndi kathupi kosamva makobidi