James Mkantho poems

James Mkantho poems Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from James Mkantho poems, Poet, Lilongwe.

07/09/2023

"MOYO UMASINTHA" a collection of fifteen (15) poems is completed. order for your copy now. Ndakatulo zokoma, za mchinyanja chothyakuka bwino. Watsapp me on 0993 234 580 for soft copy. Ka mtengo pang'ono!

31/08/2023

CHIMWEMWE CHENI CHENI

Hehede! azimayi anakondwera
Mai anga atafuula ndi ululu wa ku leba
Mbali inayi akukondwera ndi chiyembekezo
Tsiku limene dziko lidaonjezera chiwerengero cha anthu
Tsiku la kubadwa kwanga
Tsiku limene kunali chimwemwe cheni cheni

Waimilira! mawa ayenda! x2
Adandiyimbila mayi pakutha chilumika
Kuchokera pa tsiku la kubadwa kwanga
M'manja mododometsa mukumveka
Akuti ndaimilira ineyo eti!
Apa panali chimwemwe cheni cheni

Ndalora bola osauza anthu!
Linali tsiku limene ndinapeza bwenzi
Tsiku limene usiku wake tulo tinali tondivuta kwabasi
Kumangoganiza za zimene ndamva pa tsiku lopeza bwenzi
Chimwemwe chosefukira chitadzadza mtsaya mwanga
Chimwemwe cheni cheni

Lulululu azimayi analulutira
Kweee! abambo anayimba malikhweru
Kunali phwando tsiku la ukwati wanga
Magule alunso ndinaonera inee!
Ndikulowa moyo wa m'banja tsopano
Tsiku la chimwemwe chosasimbika

Nyumba yakumtima kwanga ndamanga
Galimoto ka kumaloto kwanga ndagula
Ana anga sukulu zodula aphunzira
Zofuna m'moyo ngakhale sizikwana koma ndatolelabe
Ndimayesa ngati zonse ndanenazi nkudzetsa chimwemwe m'moyo mwanga
Koma ayi antaa!

Chimwemwe chikupezeka mwa mwanawankhosa
Chimwemwe chosasimbika
Chimwemwe chokhazikika
Chimwemwe chosatha
Pangani zoti mudzakalowe dziko la malonjezano
Mudzapeza chimwemwe cheni cheni

15/08/2023

Mukawerenga mupange like pagelo kuti zambili zisamakuphonyeni

15/08/2023

NDITAKAFIKA POTSIKILA

Ndikulinda potsikila
Pamene za manja anga ntchito
Umboni zidzandichitila
Ndikuimba amamva nati wachita bwino
Nditakafika potsikila

Paja mukuti moyowu ndi ulendo
Paja mumati aliyense ali ndi kofikila
Si tili pa mpikisano wayekha wayekha paja?
Amene wafika amalandira yake mphotho?
Inenso ndikulinda yanga kukaituta
Nditakafika potsikila

Nditakafika pagombe
Oyera adzandilandira
Mphete kuchala changa adzamveka
Adzati wamalizatu iwe ulendowu
Nditakafika potsikila

Kundiona mukundiwona
Kupemphera ndi kuopa Chauta
Pokhala ndili ndi chidziwitso chakuya
Wanga kolona ndidzatchena mbamba
Nditakafika pagombe

Nazo ntchito zanga zatsiku ndi tsiku
Kaya kulima kaya kugulitsa zitumbuwa
Yake siteji zili nayo
Ndikasimba lokoma mtsogolo mwake
Nditakafika potsikila

Tinali ambili amene tinayamba ntchitoyi
Ntchito yolima mbatata ya kholowa
Ambili asiya ati ndi yowawa
Koma ine sindisiya ndigwilabe
Ndikasimba lokoma potsikila

Potsikilatu ena akafika ndi zambili
Pomwe ena akafika opanda olo
Zikutengera momwe wachitila mkati mwa ulendowu
Poti zotsatira zidzadziwika
Ukadzafika potsikila

M'bale kodi wakonzekera?
Kukakumana naye wopangitsa mpikisanowu
Kuti ukalandire malingana ndi tchito zako
Chifukwa ndiye ukakumana naye ndithu
Tikakafika potsikila

Like my page

11/08/2023

MLENDO

Mudati amabweretsa kalumo kakuthwa
Mudati ndi mame amakamuka msanga
Ife phee! kumvetsera
Popeza adati inu ndi m'dambo
Moto sungadutse ungakalipe

Pa mlendopa muunikenso koma
Chifukwa umm' kuli alendo kuno
Alendo ena abwino ena oipa ndithu
Kuipa ndi kochokera komwe
Eyatu, kuli alendo kuno eeh!

Alendo ena amabweretsa macheza
Kudzacheza kwa masiku indee!
Mame anji a milungu itatu
Popita amafuna tiwapatsenso mphatso
Kalumo kaja adzatenganso kathu

Mwana akabadwa pakhomo mukuti mlendo
Chimwemwe chimachulukadi zoona
Mlendo odzakhala nanu zilumika
Mlendo wanji uyu
Mutiuze zoona za mlendo apa

Alendo ena timawakonzekera ena ayi
Ena timadziwa kuti abwera ena ayi
Komatu onsewa ndi alendo
Amabwera ndi kalumo kakuthwa eti,
Ndi mame sachedwa kukamuka eti,

Alendo ena amasangalatsa
Nyumba yatsopano imadzetsa chimwemwe
Galimoto latsopano ndi zabwino ndithu
Mphatsa ya mwana m'banja bwaa!
Alendo

Alendo ena ndi olilitsa
Imfa ya okondedwa ndi mlendonso
Mlendo obwera kudzatsitsa msozi m'maso mwathu
Uyu mlendo saleletseka kudza pakhomo
Usadzabwerenso simungakambe naye

Pamene munkati ndi mame paja umm'
Mudali mutatopa eti
Pomati amabwera ndi kalumo kakuthwa
Mudali ndi njala kapena
Konzekelani kukubwera mlendo

Like my page

11/08/2023

MDIMA M'MASO MWANGA

Ndikuona mdima amayi
Mdima ukundikulira m'maso mwanga
Mdima wandiweyani
Mdima wosasimbika
Mdima wodza ndi ululu
Mdima m'maso mwanga

Kunja kumacha ndi kuda
Kukada kumachanso
Mdima ndimauwona kukada
Mdima ndikuudziwa ine amayi
Kulimbika mtima ndimalimbika kuti kucha
Ndikuona mdima m'maso mwanga

Zochuluka zimachitika mdima ukadza
Zabwino komanso zoipa
Zosangalatsa komanso zowawa inde!
Lero lokha ndiye ndi la zowawa
Zowawa ngati ndulu ya ng'ona
Umm' mdima wachuluka m'masomu

Mdima umabwera ndithu zoona
Mdima wa lero ukundidabwitsa koma
Mwezi ndi nyenyezi zimawalako nthawi ya mdima
Kuwala kwa magetsi inde
Ndimaonako zina zingachepe mu mdima
Wa lero mdima sindikuona kalikonse

Mwina nditha kusochera osabweranso
Mwina nditha kugweranso mu dzenje
Dzenje lakuya losatheka kutuluka
Anamakwilira oyenda usiku adzanditsekera
Chifukwa ndiye umm'
Ndikuwona mdima m'maso mwanga

Mdimawu ukapitilira abale
Langa pempho ndi limodzi
Mkazi ndi mwana mundithandizile
Muwapatseko mayendedwe kumudzi apite
Popeza panu pakhomo sangakhale
Mdima waukulu m'maso mwanga

Abale ndi abwenzi ndikutsanzikilatu
Mwina mawa sitionana kukacha
Ine mdima ukundichititsa khungu
Ndikuona ngati lakhala diso limodzi kuti mundithile
Pamene oyera adzati kwathu sipadziko
Ndikuona mdima m'maso mwanga

Mdima wamtundu wanji kalanga ine!
Mdima wokakamila
Chifundo wosachita mdima!
Mwana wanga ochepayu asamala ndani
Popeza mdima sukundichokera
Mdima wokhalitsa m'masomu

Zafika pa mwana wakana phala tsopano
Mtima walimba zoona
Wanga katundu pa ulendowu ndamanga kale
Sindibwelera! sindibwelera!
Mdima m'maso mwanga amayi
Kalanga! mdima uja! mdima!

Like my page

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when James Mkantho poems posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category