18/10/2026
Mpikisano wa FDH Bank Premiership wayaka moto pomwe timu iliyonse ikuyesetsa kudzimenyera nkhondo pofuna kupeza mapointi atatu mu gawo lachiwiri la mpikisanowu.
Tikunena pano, timu ya FCB Nyasa Big Bullets yabwereranso pamwamba pa mpikisano wa FDH Bank Premiership pomwe yachotsa Mighty Wanderers yomwe yangokhalapo kwa maola 24 chabe kutsatira kugonjetsa timu ya Mafco FC ndi zigoli zotatu kwa chilowere masana a lero la Mulungu pa bwalo la Civo mu mzinda wa Lilongwe.
Bullets inapeza zigoli kudzera mwa Clever Kalambo yemwe anagoletsa pa mphindi ya 13 m'chigawo choyamba asamwetse Tsimba Tiyaye pa mphindi za 87 ndi 90+3 za m'chigawo chachiwiri kuti masewerowa athere mokomera Mapale ndi zigoli zitatu kwa duuu!!
M'masewero ena, Silver Strikers yagonjetsa Moyale Baracks 1-0 pa bwalo la Silver ndi chigoli chomwe anagoletsa Innocent Shema, Ekhaya yalepherana ndi Red Lions posagoletsa chigoli chilichonse pa bwalo la Zomba, pomwe zigoli ya Tonic Viyuyi komanso Webster Mzunga zapambanitsa Blue Eagles ndi zigoli zitatu kwa chilowere yomwe imasewera ndi Chitipa United pa bwalo la Nankhaka.
Zateremu, Bullets yatolera mapointsi 36 pa masewero 17 kusiyana ndi pointi imodzi ndi Mighty Wanderers, ndipo Blue Eagles yakhazikikabe pa nambala yachitatu ndi mapointi 34.
Masewero omaliza mtsiku la lero a sabata ya nambala 17, aliko madzulo ano nthawi ya 6 koloko pakati pa timu ya Masters Security FC yomwe ithambitsane ndi timu ya Karonga United pa bwalo la Bingu.
Wolemba: Rashid Mtumbati-Mwanza