08/01/2022
*Zidze Pano Nzatonse!!*
_Tsiku lina khoswe_ _Anaona Mwini_ _Nyumba_
_Ak*tchera_
_Msampha Oti Iyeyo Akodwapo_
_Ndipo_
_Anachita mantha,_
_Napita Kukaiuza Nkhuku za Chiwembucho._
_Nkhuku Itamva Inati:_ _'Kaya Zako Izo, Ine Zisandikhudze.'_
_Kenaka Khoswe uja Adakadandaulira Mbuzi za_
_Msampha Omwe Udatcheredwa Uja._ _Nayonso Mbuzi Idati;_ _'Zisandikhudze, Msamphawo Ndi Wako Uisova Ase!_
_Wakula Watha,_
_Khoswe Adasweka mtima_
_Adapitanso Kwa Ng'ombe_
_Naifotokozera Iyo_ _Zimene Iye_ _Adakambirana ndi Nkhuku ndi Mbuzi_
_Za Chiwembu Chija_
_Koma Ng'ombe Idamulanda Mawu Mkamwa_
_Niti;_
_'Iwe Khoswe Ndiwe Wakuba, Msampha Umenewo Ndi Wako_
_Ukuphe Kumene Ndi kuba kwakoko'_
_Khoswe Adakhumudwa _Ndipo adati;_ _Dziwani ichi anzanga;_ *Ziti zidze pano nzatonse*
_Poona Kuti_
_Palibe_
_Akumuthandiza_
_Adangoyamba Kuyenda_
_Mosamala._
_Usiku Wina_
_Padamveka Phokoso Pamsampha paja._
_Amayi Am'nyumbamo Adadzuka_
_Poyesa Kuti Khoswe Uja Wagwidwa_
_Mwatsoka Idali Njoka Ya Ululu_
_Yomwe Idali Itangogwidwa Ku Mchira_
_Itawaona Idawaluma Ndipo Posakhalitsa Anafa_
_Mwini Nyumba Uja Adapha Ng'ombe, Mbuzi Ndi Nkhuku_
_Kuti Anthu Adye_
_Pa Maliro_
_Khoswe ataona izi adati_
_'Ha!!Zidze pano nzatonse'_
*Phunziro:*
_TIYENI ABALE NDI ALONGO TIDZIKHUZIKA NDI VUTO LA WENA. CHIFUKWA TIKHOZA KUMAONA NGATI VUTOLO SILATHU KOMA PAMAPETO PAKE IFEYO NKUDZAVUTIKANSO KUPOSA OMWE AMAONEKA NGATI VUTOLO NDI LAWO LOKHA_
_taonani zomwe_
_Ng'ombe_
_Mbuzi_
_ndi Nkhuku anati zisawakhudze, Zinawakhudza Mpaka Imfa..._
*AMBUYE AKUSUNGENI MCHIKONDI CHAKE*
_*AMEN*_ππ»