04/09/2023
*๐ฅMKAZI WA MLONDA๐ฅ*
*EPISODE 1๏ธโฃ๐ *
*By Raja B The Poet ๐ค๐ฅ๐ฅ๐ฅ*
๐ญ๐ฅ๐ฅฌ๐ง
๐๐ฅ๐ฅ๐ฅ๐ฅ๐ฅ๐ฅฌ๐ฅฌ๐ฅฌ๐ฅ๐ฅ๐ฅ๐ฅ๐
*๐ฅฌ๐ฅฌGarden๐ฅ๐ฅ*
Boss::::::"Tsekula gate!!!".
Linda::::::"Gate lake litinso? "
Boss:::::"Nawenso usakhale ngati mwana ,,, tatsekula."
Linda:::::"Abwana,,, kuno ndi ku garden tu si pa gate apa,,,, koma muli bwinobwino? "
Boss:::::"Zopusa ,,, taona mpaka akubwera akazi anga,,,,tamathyola masambawo usangoyima pamenepo. "
Apa Linda adawerama nkumapitiliza kuthyola masamba ndipo Madam adalowa mu garden muja momwe adawapeza amuna awo akuthyola ๐ฅญ mango ndipo sadalimbane ndi zambiri koma kumuitana Linda amene adayankha mwachibwibwi.
Madam:::::"Linda,,,, bwanji ukuoneka wa mantha?"
Linda:::::"Palibeee ma ma damu ,,, koma mwaswera iiii sorry mwadzuka bwanji? "
Madam:::::"Ndadzuka bwino kaya iwe,,,,? "
Linda::::::"Ndadzuka bwino. "
Madam::::::" Tasiya kaye kuthyola masambawo ,, tiye kuno uzinditsatira,, changu. "
Linda::::::" Ndalakwa chaninso ine? "
Madam:::::" Linda ,, koma zikuyenda? Nthawi zonse ndimakutenga koma siumafunsa,,, why lero ukuoneka mosinthika? "
Linda::::::" Pepani adona,,, tiyeni. "
Linda adayamba kuwalondola madam aja uku ali cheucheu kumawayang'ana abwana ake amenenso adangogwira bango uku akunjenjemera poganiza zoti mwina akazi awo adabwa chinachake.
*๐ฅ Dinning Room๐ฅ๐๐๐๐*
Madam adalowa naye Linda mchipinda chodyera ndipo adamuonetsa zonse za mnyumbamo pomuuza zoti akhonza kumadya chakudya chomwe wachikonda plus kumaonetsetsa zoti wapukuta bwino pamatebulo onse ,,, kukolopa ndi plus kuchapa zovala.
Abwana adali akumvetsera pa window ndipo mtima wawo udatsika atamva zomwe amayankhulana.
*๐งRaja๐ง*
Raja adali ali mu mkanyumba kake uku akumvera Bluetooth speaker yake kenako adangomva kuodira ,,, uyu adali nzake dzina lake Shemu amene adalowa nkukhala nawo pa bench yomwe idakhomedwa mkanyumba kaja.
Shemu:::::"Anzathu mwadekhatu,,,, uku mukumvelera tinyimbo ,,, komatu nyimbo imeneyi mukumaikondatu almost week yatha tsopano mumangoyiyika pa repeat and repeat again and again twice for the next second time. "
Raja:::::" Paja nawenso kkkkkk wachilakatulatu,,,,. "
Shemu;::::::" Paja ifetu ndi makina na pachingende pokhapo usaiwale,,,, ndiye ndiuze the reason behind this wachenjera darling song. "
Raja::::::"Aise Shemu,,,, nkhani yake ndi yaitali,,,, ungandisungile chinsisi? "
Shemu:::::::" Za ine umadziwanso,,,, unless utandiuza wekha kuti ndiulule . "
Raja:::::::"Ok aise,,,, choyamba ndikufunse,,,, Kodi utapita kumudzi kukamutenga mkazi wako kumubweretsa mtown muno,,, ndiye after kusukusula wayamba kukutaya mwinanso nkumafika pomahoperana ndi abwana ako ,,, ungatani? "
Shemu:::::::" Eeish ndi mbola man,,, ameneyotu angandimve,,, by the way,,, ukundifunsiranji choncho kumachita zoti iweyo ulibe mkazi? "
Raja;::::::" Aise Shemu,,, sorry pomakubisila zonsezi,,,, koma zoona zake ndi zakuti Liii. "
Raja adayimikira kaye kuyankhula atamva horn pa gate ndipo adatuluka mwansangansanga,,,, ataona zoti ndi galimoto ya abwana ake sadachedwe koma kutsekula gate uku atamenya sailuti ,,,, galimoto idayenda ndipo atafika pamene padayima Raja,,, boss adatulutsa ndalama kumupatsa Raja uku akumuuza zoti ndalama imeneyo ndi mphatso chifukwa adamubweretsera mtsikana okongola ,,,,,.
Raja atasunzumira mkati mwa galimoto seat ya kumbuyo adamuona Linda atakwera ,,,, apa Raja adawafunsa abwana ake .
Raja:::::"Boss,,, mukupita kuti ndi Lindayo?"
Boss:::::"Ndikupita naye mtown kukamuonetsa ma shop ndi malo ena omwe timagula zinthu kuti akamapita asadzavutike,,,, ok ,,, tionana. "
Boss adaiponda galimoto ndipo mtima wa Raja udagunda kwambiri mpaka adaiwala zotseka gate ndipo adalowa mkanyumba kaja ndikuyamba kulira mosisima mpaka Shemu adafunsa.
Shemu:::::"Raja,,, what's wrong,,, mpaka zafika pogwetsa misonzi ? "
Raja:::::" Aise ,,, ndithandize plz nzakone zandivuta . "
Shemu:::::"Bwanji ,,, kapena akukuchotsa ntchito? "
Raja:::::" Mayazi,,, ikanakhala ntchitoyo sibwenzi ndikudandaula. "
Shemu:::::" Nanga ndi chani? "
Raja:::::" Usaiwale paja ndimakuuza nkhani . "
Shemu::::::" Yes ,,, ndiye umatanthauza chani pondifunsa chonchija? "
Raja:::::"Aise,,,, ineyo ndili ndi mkazi ndipo ndi..... "
Shemu:::::" Amfana Raja,,, moti ndi inu okwatira? Bwanji osatiuza? Ali kuti mkazi wakoyo timudziwe kapena udamusiya kumudzi? Kamutengeni man zikuoneka kuti zayamba kukuthekeranitu mtown muno. "
Raja:::::"Shemu,,, umakumbukira day inayake ndinkakuuza zoti abwana anga akufuna wa ntchito mtsikana? "
Shemu:::::" Ndipo udamupeza ,, si uyo wakwera galimoto ndi abwana akowo? By the way,, umadziwa zoti mkazi ameneyo ndimamufila? Kubwerakutu ndimafuna ndizikuuza nkhani ya beib imeneyo,,, Raja,, asadalowe abwana akowo pakufunika ndimulowe kaye eeeish ndi akatundu abomatu tithandizeni man. "
Raja:::::" Aise Shemu khala serious,,, dikira ndimalizetu kufotokonza. "
Shemu::::::" Kkkkkk ok apa tsopano ndakutolera,,, nawenso umamufira mkaziyo eti ?Tiye tipikisane tione yemwe awine. "
Raja:::::" Shem tadekha,,, ndimayesa ndati undithandize.? "
Shemu::::::" Sorry man,, it's fine,, ndiye wati bvuto ndi chani?"
Raja;:::::"Abwana atandiuza zoti ndiwapezere wantchito koma akhale wachitsikana komanso wa ma looks abwino,,, ndinaganiza maganizo awiri,,, ganizo loyamba linali loti ndizingoyimitsa mtsikana aliyense bola akhale owoneka bhooo nkumamufunsa ngati angafune ntchito ya mnyumba,,,, ganizo lina lidali loti ndiyitane mkazi wanga kumudzi kuti adzagwire ntchitoyo. "
Shemu::::::" Ganizo loyitana mkazi wakolo ndi ganizo lopusa,,, unless ngati ali manyaka koma bvuto ndi loti bwana wako amafuna duwa ,,, ndiye tsopano Lindayu udamupeza bwanji? Kapena amafunanso ntchito mtown mu? "
Raja::::::" Ayi,,, ganizo longomayimitsa aliyense ndinaliona zoti ndi loipa,,, ukhonza kuyimitsa wakuba bola kupeza mtsikana oti ndikumudziwa,,, ndiye ndinamuyitana Lindayu. "
Shemu'::::::"Over my dead body,,, meaning to say,, Lindayu ndi mkazi wako?"
Raja:::::"100 percent,,, Linda ndi mkazi wanga!! ".
Shemu:::::"Man Raja munabetsa,,, mkazi ngati Linda si ofunika kumamuyika pa auction choncho,, aise,, Lindayu uli naye mwana? Chifukwa akuonetsa ngati ndi namwali sadaberekepo. "
Raja:::::"Tilibe mwana,,, takwatira a miyezi 6 yapitayo. "
Shemu::::::" Meaning even kuombera siudaombere? "
Raja:::::" Yes. "
Shemu::::::" Chibwana,,, ndiye umati titani? "
Raja:::::" Iwenso ukundifunsa ine? Ndati ndithandize maganizo plz. "
Shemu::::::" It's ok,,, pakufunika ukhale naye pansi umukumbutse udindo wake,,,. "
Raja::::::" Ndakhala naye kambirimbiri koma pano wayamba kumandipewa ndipo ndikamuyitana nthawi zambiri sakumabwera. "
Shemu:::::" Ok,, abwana ako amadziwa zoti Lindayo ndi mkazi wako? "
Raja:::::" Ayi,,, eeee aise kuti adziwe si basi ife ntchito njeeee!! ".
Shemu::::::" Upa..... Eeee kukubwera adona uku,,, akukuitana. "
Raja adatuluka mkanyumba ndipo adathamangira komwe madam amaitanako ndipo adanyonyomala.
Madam::::::"Raja ,, koma waona pa gate po?"
Raja:::::"Eeeish madam sorry ,, kungoti ndinangobalalika,,, odi ndikatseke. "
Madam::::::" Ndikudziwa zoti ukumabalalika masiku ano ,,, Raja ndi iwe mnyamata okongolatu choncho usafere mchenga oyera poti tirigu wakoyo wakolanakolana ndi nansongole,,,. "
Raja::::::" Adona,,, mwandikuluwikatu pamenepo,,, ndimasuleni chonde. "
Madam::::::" Raja,, dekha,, siya tirigu ndi nansongole zikulire pamodzi,,,, takatseka gate lo kenako undipeze mnyumbamo. "
Madam adangotero iwo nkumakalowa mnyumba kumusiya Raja atangoyima uku akudya mutu kenako adapita nkukatseka gate lija ,,, atatero adalo mkanyumba kaja kuti atsanzikane ndi nzake koma adamufunsa kaye nzeru.
Raja:::::"Aise Shemu,,, ukamamva zoti munthu amalowa mchala,,, dzuwa zoti ine ndalowa mchala. "
Shemu::::::" Nice,,, ndiye walowa chala chake chiti? Chakuphanzi kapena chamkombaphala? "
Raja:':::::" Choka nawenso,,, aise ndikuona ngati madam ayitulukira zoti boss akuvayilira mwa mkazi wanga,,, komanso zoti Linda ndi mkazi wanga. "
Shemu:::::" Zili bwino,,, kodi madam wa ali ndi ana angati?"
Raja:::::"Akuti alibe,,, kuchipatala adawauza zoti sangabereke."
Shemu:::::"That's why akuoneka chitsikana choncho eti? Koma ameneyu si mwanamwana wangokula zima hip zo? "
Raja::::::" Ndi mwana moti even ndi Linda uja, wamkulu ndi Linda,,,. "
Shemu:::::" Tavayani man,,, ukakapezana nawo ukakumbukire mau awa,,,, *"nzako akati konzu,, nawenso konzuu,,, kachipande ka therere kamanzuna nkuyenderana,, "* ndapita."
Raja::::::"Kkkkkkk koma iweyo ndi more ,,, koma usamaiwaletu zoti " *mbuto ya kalulu imakula ntadzaoneni."*
Shemu:::::::" Ndiye zikugwirizana pati? Kkkkk a Raja B paja za miyambizi nkumanzere,,, mwambo wakowo siukugwirizana ndi nkhaniyi,,, kkkkkk tavayani mwachangu uko paja *kayitana kavula ukachedwa ukapeza kali mu leggings. "*
Apa Raja ndi Shemu adasiyana wina kumatuluka mu mpanda pomwe Raja amakalowa mnyumba.
*๐ฅฌ๐ฅKu Msika๐ฅ๐๐ฅ๐ฅ๐ฅฌ*
Linda ndi abwana ake adayenda mu ma shop angapo kenako adakathera ku Lodge kufupi ndi msika wa Limbe,,,.
Atafika kumpanda adayimika galimoto yawo ndipo boss adabhuka room ,,, onse adakalowa mu room ndipo adayamba kukambirana.
Boss::::::"Linda,,, ukudziwa zoti ndi iwe mkazi wabwino?"
Linda::::" Kkkkkkkk kaya sindikudziwa ine. "
Boss::::::"Yaaah,,, ndiye ndakutengera kuno pa zifukwa,,,,, Kodi udakwatiwapo? "
Linda::::::" Mwafunsiranji choncho? "
Boss::::::"Chifukwa choti umandisangalatsa ,,,, ndi iwe mkazi wakumaloto kwanga,,,,, ndiye ngati udakwatiwapo undiuze ,,, ngatinso uli pa banja undiuze. "
Linda::::::"Ndikakakhala zoti ndili pa banja mutani? "
Boss::::::"Ndithetsa,,,, just magine chilengedwe ngati iwe nkumachilola kukagwira ntchito ya mnyumba,,,, sali serious mwamunayo. "
Linda::::::" Kkkkkk ine sindili pa banja,,, feel free. "
Boss:::::" Wow!!! Ndiye dziwa zoti ndili ndi nkhani yabwino kwa iwe,,, talota!!! "
Linda::::::" Kkkkkk ine sindikuidziwa plz ndiuzeni! ".
Boss:::::::" Ukudziwa vuto lomwe lili mnyumba mwathu muja?"
Linda::::::"Lokhudza kusabereka kwa madamu?"
Boss:::::"Eyaaa,,."
Linda:::::"Ndikudziwa,,, nanensotu ndimangodabwa ,,, ndiye ndimangoti basi paja chimanga chimalola opanda mano kkkk,,, anthu ndi inu olimba,,, mpaka kumakhala ndi zinkhupule? "
Boss:::::" Kkkkk zikuoneka kuti wayamba kale kuona patali,,, ndiye ukangodekha nkundilola kuti thupi lakolo ndiligwiritse ntchito mpaka kunyamula chipatso changa,,,, udzakhala mwini filimu ndipo madamu ako aja basi. "
Linda:::::" Ndilonjezeni kaye zoti mudzawasiya nkundikwatira ine. "
Boss::::" Ndidzatero ,, kapena ukufuna ndichite chowinda? "
Linda:::::"Ndipatseni imodzi mwa nyumba zanu ikhale mu dzina langa . "
Boss:::::" Tikamachoka muno tikapanga zonse,,,, ndiye tisachedwe ndikuona kuchedwa,,, tagona."
Linda:::::"Dikirani,,,,, ndimafuna mundilonjeze chimodzinso!! "
Boss:::::" Say it ndipo ndipanga . "
Linda:::::" Gate man uja akalandira mwezi uno mumuchotse ntchito. "
Boss:::::" Ngati akumakuvutitsa ndimuchotsa even lero. "
Apa Linda adachita kunyamuka nkudziponya pamwamba pa abwana ake omwe sadachedwe koma kuyamba kazukuta.
*๐งRaja๐ง*
Raja atalowa mnyumba muja adafikira pa sitting room ndipo madam atamuona zoti wabwera adapita pa sitting room pompo ndipo adatenga phone yawo nkuyatsa kenako adamuuza Raja kuti .
*"Tapenyaaa๐ณ*"
Next,,,,,,,, guys,,,,, ka nkhani akaka mukatsatire ndi chidwi chifukwatu muli zinthu ,,,, apapa zangoyambika kumene,,,,,,.
Kodi Linda atengadi pakati?
Nanga Raja waona chani pa phone ya madam boss? ๐ณ
Join my WhatsApp group today through this number,,,, *0884849947*.
Raja B loves you all good people with beautiful names ๐.
Nkhanizi mukazipeza pa page yanga ,,, just search,,, RAJAB MWANA OMUPEZA THE POET kenako pangani follow page imeneyo basi.