19/12/2025
Mkulu wina Ku Ireland dzina lake DJ Carey ananamiza azibale ake ndi amzake kuti akudwala ndipo wagonekedwa ku chipatala kotelo akufunika ndalama kuti alipile ma Bill chonsecho zili zaboza ndipo amatumiza chintchuzi ngati Ali mchipatala chomwe pamapeto pake anazindikila kuti ndi boza
Ankagwiritsa ntchito chingwe cha charger cha iPhone (cable) ngati kuti ndi chubu cha kuchipatala, n’kutumiza zithunzi kwa anthu osiyana siyana kuti amukhulupirire mkumutumizila ndalama.
Kotero anabera azibale ake ndalama pafupifupi £345,000, ndipo khoti linamumanga ndikumugamula kuti akakhale kundende Kwa zaka 5 ponamizila kudwala ndikubela ndalama azibale ake ndi amzake
😳 Anthu chinyengo anafika nacho patali