02/02/2026
Thanks a Ras
Ras,
Nthawi zambiri ma artists tikapita m'ma studio ambiri zimapezeka kuti tapanga record nyimbo yonse then 2 minutes later ma vocals akumveka ngati awamixer kale.
Basitu amakhala kuti ma producer angoyika preset ya ma plug-in oti anayuza kale pa artist winawake and zinawamvekela bwino nthawi imeneyo m'ma speaker awowo basi ati nyimbo yangotsala kuyipanga master ngati kuti amathanso mastering akunenayo.
Ma plugin ake oti angowapanga download pa ma website awulere. Ndi izi zikumapezeka nyimbo za ma artist zikufanana heavy ku Malawi.
Ndi ma producer ochepa ku Malawi omwe amafatsa ndi kuyika ma plug-in ogwirizana ndi voice ya artist yemwe wapanga record nthawi imeneyo and DJ Sley is one of them.
Pano ndi awa agundika akuti ma session aziyambila K1,000,000. To be honest, creativity, customer care and music quality yama producer ambiri ili very bad and only few producers in Malawi are worth this fee.
Nyimbo zake ziti? Izizi zoti timangotumiza beat yapa Youtube kuti mupange yofanana? Khalani serious; K1Million si ndalama yamasewera ku Malawi.
Ma studio ambiri ku Malawi ali ku chipinda za mu nyumba za makolo ama producer and salipira misonkho ku MRA kapena ma Business Premises License ku district/city council.
Basi tizingowasonkhela ma producer ndalama zomwela mowa, kugula ma airforce afake, nkupeza ma bebi m'makwalalamu basi; ambiri equipment anasiya kugula kalekale, angodalira ka soundcard ka Focusrite basi.
At this point, I encourage every artist to buy their own recording equipment. It will save you so much money.