13/03/2026
Bambo wina yemwe sakudziwika wapezeka atafa komanso thupi lake litawonongeka mu mtsinje wa Bua m'boma la Ntchisi.
Wachiwiri wa wofalitsa nkhani za apolisi m'bomali, a Tadala Makiyi, wati thupi la bamboyu lapezeka likuyandama mu mtsinjewu lachinayi sabata ino.
"A Manuel Mwenje, a mmudzi wa Matekenya mfumu yaying'ono Kabvulala, anathamangira ku polisi ya Malomo ataona thupili," atero a Makiyi.
Iwo ati zotsatira zachipatala, zatsimikiza kuti bamboyu anamwalira kaamba kobanika chifukwa chomira.
Pakadali pano apolisi m'bomali, akusakasaka achibale a malemuwa.
Wolemba: Abdul Kalonga