30/06/2025
ABWENZI A PADZIKO
Moyo ndi ulendo, ulendo osapanganika
Ulendo omwe umakumana ndi zinkhomo
Pena usangalale, penaso ulire
Pena kusowa okugwira padzanja, abwezi kukuthawa
Zikamakuyendera amakuyandikira, zikakuvuta ngati sakudziwa
ABWENZI A PADZIKO
Ukakhala pantchito kukupangira upo, kuwauza abwana zoipa zokhazokha
Ntchito ikakuthera iwo mkumasekerera, ati umafuna ndinge yani?
Ukavala suit amafalitsa avekere, Zobwerekazotu zikuwakhala,
Akakuona akuyendetsa galimoti, auza anzawo avekere galimoti siyawo abwereka
Akakuona ndi lanya yapamwamba, ati lanyayo anatenga pangongole.
Sakondwera moyo wanga ukamayenda bwino
ABWENZI A PADZIKO
Dzulo anakumana ndi mkazi wanga ati kumamufusa mwaine anaona chani
Kaputha buwe ngt ine thupi langa lokalamba anga munthu oweta ng'ombe
Mutu wanga wamakonamakona anga triapizium
Thupi langa lochepa anga tiligu analota mfumu farawo uja
Ati ndikadya nyama ndi soya pieces chinthu chodula m'nyumba mwanga ndi ndi mpeni
Zonsezi kufuna kuti mkazi wanga andisiye
ABWENZI A PADZIKO
Ataona banja langa likuyenda bwino, ayambaso kumunyoza mkazi wanga
Ati mbinayi siyachilengedwe anachita kukabaitsa
Kunenepaku ati mkazi wangayu ma ARVs amuyanja
Kukakhala Kuyeraku, sichina ai koma ..,...................
Akumamunyozaso ati sukulu sanaimbe angakhale pepala la standard 8 alive
Zosezi kufuna kusokoneza banja langa
ABWENZI A PADZIKO
Ataona kuti moyo wanga aulepha, banja langa alilepheraso
Mbiri yanga tsopano ndiyo target yawo
Chuma ndili nachochi ati nathwimira, chigayo changachi ati naphera mdzukulu wanga
Ntchito ndugwirayi ati nalowaso mwachinyengo,
ABWENZI A PADZIKO
Ngakhale mbiri yanga ataipitsa, banja langa kulisokoneza
Ine ndi mulungu wanga tili nganganga, ubale wanthu sungasokonekere
Pakuti ndidziwa kuti bwenzi labwino ndiyekhayo
Singafanane ndabwezi a padziko, omwe amasithasitha mawanga
Koma ine ndidziwa moyo uno tiyenera kudutsa muzokhoma chifukwa
Abwenzi a padziko sakondwera nawo m'dalitso wanga.
ABWENZI A PADZIKO