15/06/2026
Mtsogoleri wa chipembedzo cha makolo cha M'bona, mfumu yayikulu Ngabu, ya m'boma la Nsanje, wati M'bona ali ndi kuthekera koletsa kapena kuchepetsa mphamvu ya nyengo ya El Nino yomwe ikhoza kukhudza dziko lino ngati aMalawi angathire nsembe kwa iye ndi chikhulupiliro.
Mfumuyi yati; "anthu atagwirana manja kupita ku Khulubvi kukathira nsembe ngati chikhulupiliro tili nachodi, kupempha M'bona mwini wake amene amadziwa zonse kudzera kwa Mulungu, vuto la ng'amba likhoza osadzakhalapo kapena losapyola muyeso.
Iyo yauza Zodiak Online lero kuti; "tikaona kuti nyengo yafika povuta timagula kachaso wathu ndi zina ndi zina kupita ku Khulubvi kukagwadwa ndikupempha M'bona kuti atithandize ndipo amatithandizadi," yatero mfumu yayikulu Ngabu.
Mkulu wa nthambi yoona za nyengo, Dr. Lucy Mtilatila, anauza Zodiak Online posachedwapa kuti pali kuthekera kwakukulu kuti dziko lino likumana ndi nyengo ya El Nino mu nyengo ya dzinja ya chaka chino.
Uku ndi kutentha kwa madzi ku nyanja ya mchere ya Pacific komwe akuti kumadzetsa vuto la kuchepa kwa mvula maka m'madera a m'chigawo chakumwera.