03/08/2026
YANKHO
Part 3
Henry Mkwaila... ποΈ
Click and Follow the Page
https://www.facebook.com/hmkwaila22/
Thankhs π
"Man nde Mwati Nancy ali ndima mistake anji "
"Dekhani man mukuoneka ndi phuma tu mene ndakuuzani izimu "
"Wandibalalitsadi koma ukanangondiuza kuti iye uja ali ndima Mistake anji Poti sindikumamuona ndi Amuna Tangotiuzani koma Man"
"Ayitu sikuti Nancy ndamene ndikutanthauza kuti Ali ndi Vuto komano mnati Kugwira mkazi amene uja ngati ukuganiza zimenezo ndi Mistake posatengera kuti ndi Nancy kaya Jane, Ruth, Mercy koma nkhani ndiyoti Zadzibwenzi zinaletsedwa pa School pano ndipo Kungoziwika School yako imatha Nde Kumbukirani Kuti palibe Chachinsi pa dziko pano simungakwanitse Kukhala mwa Awiriwiri anthu osadziwa Nde ineyo ndangokuuza koma Usankha wekha Maphunziro ako ndi Mkazi"
Apa tu Eva anayankhula Ngati Mokhomelera koma ndinamunvetsetsadi kuti zitha Kukhala Zoopsa koma funso ndinali nalobe kwa iye....
"Nde chinapangitsa ndichani kuti Aletse za dzibwenzi ndikudziwa kuti sukulu singamalimbikitse Kuti ophunzira azipanga Dzibwenzi Komabe kufika ponena kuti Opezeka wo Sukulu izatha nde tandiuzeni Man"
"Ndinkhani Yaitali man Koma mzabho bho poti apa sitikuphunzira lero nde tiye tipeze Malo tikhale ndikufotokozere"........
Tinatengana pamene paja ndikukakhala pa ground pazimitengo inayake Apa tu Evance anayamba kufotokoza mene zinakhalira kuti zifike poti Pomachotsa Sukulu anthu Opezeka akupanga chibwezi ........
APA TILI MMASIKU AMBUYO
"MacDonald ndikukufuna ku Office kwanga Palimodzi ndi Aggie nonse mundipeze";
Awa tu anali Mr Kafakoma Mphunzitsi wamkulu pa Sukulu po ndipo Aggie yo ana ophunzira wa form 2 pomwe Mac anali wa form 3, panthawi amawaitana awiri wa mkuti onse atatuluka mma Class awo ndikumacheza Panja ndipo atanva kuitanidwa analondola .......
MacDonald: Sir Tafika tu
Mr Kafakoma: Chabwino ndikufuna kungokufunsani Mafunso Ochepa chabe ndipo mukayankha Chilungamo ziyenda bwino, Kodi pa uwiri wanu pali Ubale Wanji ?
MacDonald: Aah Sir Tonse ndiOphunzira nde ndiubale monga ophunzilira aliyense
Mr Kafakoma: Aggie Utachotsedwa Sukulu Kodi Makolo ako azakondwera nawe ? Nde Yankha Chilungamo kuti mupeze thandizo langa ndikutetezeni
Aggie: Si-Sir ifeyotu, Ineyo ndi Mac yu nd........
MacDonald: Inuyo kutitetezera ifeyo Motani ? Palibe Kali konse pakati pathu Basi
Mr Kafakoma: Osazanong'oneza Bondo Pitani
Pena Chikondi chimagonthetsa makutu ngakhale maso amakhala akhungu, Koma sitikudziwa ngati makani amapinduladi
Masiku anali Mkupita ndipo tsiku lina Mac Anatailira Kutuluka Mu Class yake Ndikukalowa Class ya Aggie ati Chikondi Chakoma nde awiri wa anafika Potailiranso Mpaka Kumagwirana gwirana mclass momuja ndipo ena mwa Obhoweka nazo anathamangira kukatsina khutu Mpunzitsi wamkulu Uja ........
Mr Kafakoma: Oh ooh Mr Romeo zafika apano nde Madam Juliet Lero mundiuza Kuti chani ?
Mac: Koma tu ndife akulu Akulu nde Osamatilonda Chonde
Mr Kafakoma: ndikuuza malo eni eni Omwe sindingakulondedi, Nonsenu Suspend 2 weeks ndisakuoneni Pa sukulu Pano tulukani Panjaaaaa !!!!
Aggie: Mac ndili mantha ine Kunyumba akanditani ineee ?
Mac: Aah Ukawauza ? Nkhani ngati izi izoyenera Kuwauza makolo iweyo Uzikangokhala mene umakhalira masiku onse ndipo mamawa kukacheza Uzikonzeka ngati Ukupita ku sukulu kenako uzikandipeza Kunyumba kufikira Nthawi Yoweruka
Aggie: nde Kwa 2 weeks yonseyi tikhale tikupanga zimenezi ?.........
"Ase kunja Kukuda basi ndipitiriza Kukufotokozera Mawa"
"Mmh man Eva ndikufuna nditadziwa kuti Chinachtika ndichani tu"
"Ohh Come On Yankho tipitirize mawa Kunja Kwada komanso anandituma nde nthawi"
Nthawi tu Nthawi Guys Osamangowerenga ndikusiya ai taziikaniko Comment ndiziziwa mene mukuinvelera Nkhani Kotero zizipereka chilimbikitso tu kotero nkhani zikhala zizayamba kuponyedwa Daily ndikutitu DAILY
π₯π₯π₯π₯π₯
Writer, Musician & Up coming Actor
https://youtube.com/?si=Gtba2CH1FtWHae0N