Daily Gospel Life

Daily Gospel Life Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Daily Gospel Life, Arts and entertainment, Vereenigng, Johannesburg.
(1)

17/10/2025

Hie guys koditu kusowaku anatihakila page ana anjoka ena ake.komabe ndikhulupila k*t inu muli bwino pamudzi pano.

Thanks for being a top engager and making it on to my weekly engagement list! 🎉 Samson Emson, Iyana Kawayawaya Chinula N...
04/10/2025

Thanks for being a top engager and making it on to my weekly engagement list! 🎉 Samson Emson, Iyana Kawayawaya Chinula Nkhata, Austin Maloto Phili, Emma Wa Atoms Jere, Gift Muhiphera

01/10/2025

Ayankha Mulungu.

01/10/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Glyn Lesley, Isaac Sean Chisi, Aggrey Felias, Alfred Dc Valamanja, Alice Luciano, Esther Wa Nkhomah, Felida Shaba, Elizabeth James Alli, Patrick Patrick, Judith Katuli, Milica Raphael, Chigomezgo Nyirenda, Rhoda Chisale, Agness Rice, Enocencia Amosi, Thandi Babda

30/09/2025

good morning mukhale ndi tsiku la mwayi ndinso lotetezeka

29/09/2025

kufikila kuonaso kuwala kwanu kwa ulemelelo wa tsiku lina Atate.ichi ngati sichisomo chanu
ndek*t tikuzusokoneza.

28/09/2025

pomwe nzelu zathu zathela ndipomwe Yehovah amayambira.ipezeka ntchito,banja,mpamba wa geni.akukonza chimwemwe chomwe sichizabedwa.

28/09/2025

Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani. Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa k*ti, “Kodi mukudziwa k*ti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”
Iye anayankha k*ti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe. Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”
Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”
Yesu anawafunsa k*ti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? Kodi inu simudziwa k*ti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi? Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa. Pak*ti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe. Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”
Mateyu 15:10-20

good morning 👋💙💚

28/09/2025

Big shout out to my newest top fans! DE Ric, Grecian Mpakiza, Joe Bou, James Wadi, Paulina Gondwe, Vick Beib, Madalo Kasonga, Spotem Gottem, Hendrina Tasauka, Emmanuel Wa Peniel, Norah Chibaya, Zebede Kachondo Low, Ellanive Banda, Gabriel Chipo

27/09/2025

Munthu wina amayendetsa sitima yapa njanji kuchokela dela lina kupita kukasiya anthu dela lina.njanjiyi imadutsa pasukulu ina imeneso mwana wa mkulu oyendetsa sitima uja amaphunzilapo.daily akamadutsa amamuona mwana wake uja akusewela ndi anzake.akatelo bambo uja amaimba hutala kumubayibitsa mwana uja.mwana uja zimamusangalatsa ndipo anzake aja amawauza k*t ndi bambo anga akuyendetsawo.tsiku lina mwana uja anatengana ndi anzake kupita pa njanji paja kumasewela uku akudikila sitima ija.posakhalitsa sitima inatulukila koma ulendo uwu inali pa speed kwambiri kuposa nthawi zonse.izi zinali chonchi chifukwa mu sitima muja munali mzimayi wina amene amadwala ndipo amafunika afike ku chipatala machangu.posakhalitsa bambo uja adadzidzimuka ataona ana aja kma anali atafika kale pafupi kotelo kuimitsa kunali kosatheka.anayesetsa kuimba hutala k*ti ana aja achokepo pa njanji paja koma ana aja anali akukondwelela k*t sitimayo ikubwela ndipo mwachizolowezi imaimba hutala.apapatu nk*ti zinthu zitafika kale povuta chifukwa kukhotetsaso sitima ija miyoyo yambili ikhoza kuonongeka.ana aja anayamba k*thawa atazindikila k*ti sitimayi sikuyima.koma mwana wa bambo oyendetsa sitima uja pamene amathawa anakolana ndinzake ndikugwa pa njanji pompo.apa ndipameneso shoko yanjanji inamugwila mpaka anakakamila pa njanji paja kulephela kudzuka.sitima ija inali itafika pafupi tsopano zonsezi anthu mu sitima muja amaona.ena amadziwa k*t mwana wagwayo ndi wa driver-wa.naye driver zinthu zinamukulila ndipo maganizo ena amati angoikhotetsela k*tchile mwina? k*ti apulumutse mwana wake? Kudzaonaso sitima yanyamula gulu la anthu pakhoza kukhala infa zambiri sitimayi itagwa.pamene maganizo anali akuzungulila k*t apange bwanji sitimaso nayo inali ik*thamanga.posachedwa driver uja anayiyendetsabe sitima ija mpaka kukafika pali mwana wake paja ndipo sitima inadutsa pamwamba pa msana wa mwana uja ndikudula kati ndi kati kufa kwa mwana wake kunali komweko.

Kenako sitima ija adakwanitsa kuyimitsa itatha ka mtunda ndithu kuchoka pomwe pachitikila ngozi paja.anthu ambiri amatuluka mu sitima ija akusangalala k*ti apulumuka pangozi yoopswa kwambiri.chodabwitsa panalibe munthu or modzi omuyamikilako driver uja pa nsembe yomwe wapeleka ya mwana wake populumutsa miyoyo yawo.

Phunziro driver mu nkhaniyi ndi mulungu ndipo mwana wake ndi yesu kristu.mulungu anapeleka mwana wake okondedwa yesu kristu k*ti apulumutse moyo wathu.kodi inuyo mumayamikila zabwino zimene amakuchitilani tsiku ndi tsiku? Nanga ndindani wina akanalolela kupeleka nsembe ngati imeneyi k*t tipezeke lelo ndi moyo? Tikamakhala tizidziwa k*ti sikupambana kwathu ndipo pali chikondi chozama pa ife kwa Mulungu.tizikumbukila kupatula nthawi ndikumuyamika pazabwino zonse amatichitira.

Ndinu wa chikondi chopanda malire atate.moyo wanga udzakukwezani ndikukuyamikani pa nsembe yomwe munapeleka ya mwana wanu yesu kristu kundifela ine k*ti mupulumutse moyo wanga.....

27/09/2025

atsogo inuyo ndi ampingo wanji? mounyadira tautchulani. mwina nkupezapo church mate mpaka kukaimbaso choir ku church kwao.😍🤗

Address

Vereenigng
Johannesburg

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Daily Gospel Life posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Establishment

Send a message to Daily Gospel Life:

Share