Umodzi Media

Umodzi Media Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Umodzi Media, Arts and entertainment, mz, Mzuzu.

🔥 2026 NEW ARTIST OF THE YEAR (MALE) 🔥 1️⃣ Heis Parable 2️⃣ Trinket 3️⃣ Ca$ino 4️⃣ S KhrizzyPICK 1 - VOTE MU COMMENT 👇  ...
14/10/2026

🔥 2026 NEW ARTIST OF THE YEAR (MALE) 🔥

1️⃣ Heis Parable
2️⃣ Trinket
3️⃣ Ca$ino
4️⃣ S Khrizzy

PICK 1 - VOTE MU COMMENT 👇

MTOLANKHANI WA KU UGANDA AKUFUNIKA OPALESHONI YOCHEPETSA THUPI Moses Agaba yemwe ndi mtolankhani waku Uganda wauzidwa nd...
14/10/2026

MTOLANKHANI WA KU UGANDA AKUFUNIKA OPALESHONI YOCHEPETSA THUPI

Moses Agaba yemwe ndi mtolankhani waku Uganda wauzidwa ndi ma dotolo kuti akufunikira surgery kuti ithandizire kuchepetsa chakudya chomwe thupi lake lingatenge ndi cholinga achepeko thupi.

Agaba wa zaka 42 ndipo amalemera 190kg akuti akufunika amchepetse zogayila chakudya kuti azikhuta msanga akadya pang'ono.

Tiyeni timupempherere 🙏

ZILIKOPali malipoti akuti Lilongwe Town Hall akuyikonza kuti mulowe shop ya Sana. Pakadali pano omwe akuyembekezeka kuko...
14/10/2026

ZILIKO

Pali malipoti akuti Lilongwe Town Hall akuyikonza kuti mulowe shop ya Sana.

Pakadali pano omwe akuyembekezeka kukonza holoyi akumangapo mpanda.

Sana ikutsekulanso shop ina pa Lilongwe CCAP mu hall ya mpingowu.

*NKHANI* Akatswiri a za maphunziro komanso makolo agwirizana ndi ganizo la Nduna yowona za maboma ang'ono Ben Phiri lokh...
14/10/2026

*NKHANI*

Akatswiri a za maphunziro komanso makolo agwirizana ndi ganizo la Nduna yowona za maboma ang'ono Ben Phiri lokhazikitsa timu ya mpira wa miyendo ya atsikana m'sukulu zonse m'dziko muno, ponena kuti izi zithandiza kupititsa patsogolo maphunziro.

Ndunayi inayankhula izi m'boma la Thyolo poyamikira m'mene timu ya mpira wa miyendo ya atsikana ya dziko lino ikuchitira.

Pothilirapo ndemanga m'modzi mwa akatswiri omwe amayankhulapo pa nkhani za maphunziro m'dziko muno Daniel Chibwana, anati ganizoli ndi labwino ponena kuti pamene ophunzira akutenga nawo mbari pa nkhani za masewero, zimathandizanso kaganizidwe kawo mkalasi kamba koti ubongo wawo umakhala ukugwira ntchito bwino ndipo anapempha makolo omwe salora ana awo kutenga nawo mbari pa nkhani za masewero powopa kuwononga tsogolo lawo kuti alore ana awo omwe ali ndi kuthekela kochita nawo masewero wa kuti atero.

M'mawu ake, mayi Lucy Mangwiza omwe ndi limodzi mwa kholo ati ndi koyenela kulora ana makamaka atsikana kutenga nawo mbari pa nkhani za masewero pomwe ali ku sukulu ponena kuti zimathandizanso kuwalimbikitsa pomwe akuwona anzawo akuyenda mmayiko osiyanasiyana kukaimilira dziko la Malawi koma wapempha kuti chisakhale chikakamizo koma kukhale kufuna kwa ophunzirawa kutenga nawo mbali kapena ayii.

Kholo linanso mayi Rose Ganiza anati masewerowa ndi ofunikira kwa atsikana wa ponena kuti zichepetsa nthawi yawo yomachita mchitidwe woseyenera ndi anyamata zomwenso zithandize kuchepetsa chiwelengelo cha atsikana omwe amatenga pathupi asanamalize maphunziro.

*NKHANI* Prophet Shepherd Bushiri watamanda mulungu kamba ka chigamulo cha khothi lalikulu, chomwe chathetsa mlandu wone...
14/10/2026

*NKHANI*

Prophet Shepherd Bushiri watamanda mulungu kamba ka chigamulo cha khothi lalikulu, chomwe chathetsa mlandu wonena kuti iye komanso Prophetess Mary Bushiri, awatumize ku South Africa.

A Bushiri alemba uthenga pa izi.

Iwo ati ndi zodandaulitsa kuti pali malipoti osonyeza kuti akuluakulu ena apolisi omwe adakhudzidwa ndi kumangidwa kwawo ku South Africa, adawamanga ndipo ena adawachotsa ntchito.

Malingana ndi a Bushiri, izi ndi zodzetsa mafunso pa ntchito za chilungamo.

Dzulo khothi latulutsa chigamulo chomaliza pa nkhaniyi.

Mwazina, khothi lati sikoyenelanso kutumiza a Bushiri ndi mkazi wawo ku South Africa, potengela malipoti akuti anthu ena omwe adadandaula pa milandu yomwe amawaganizira kuti adapalamula, adanena kuti adachita kupatsidwa ndalama kuti adandaule.

vip eli njuchi & casino video now
14/10/2026

vip eli njuchi & casino video now

Eli Njuchi presents the official Video to Vip, featuring Ca$ino & E...

dzimayi vs tsikana muli mbali iti?zonse ndi zeze
14/10/2026

dzimayi vs tsikana muli mbali iti?

zonse ndi zeze

🔥 BREAKING: BUSHIRI NDI MFULU - KHOTI LATHETSA MILANDU YONSE YA EXTRADITIONKhoti lalikulu ku Lilongwe lathetsa nkhani zo...
14/10/2026

🔥 BREAKING: BUSHIRI NDI MFULU - KHOTI LATHETSA MILANDU YONSE YA EXTRADITION

Khoti lalikulu ku Lilongwe lathetsa nkhani zonse za Bushiri za extradition potengera kulephera kwa mboni zaku South Africa. Mwachidule, wathuwa ndi mfulu pano alibenso mlandu.

Mwazina:
1. Mboni zaku South Africa palibe olo imodzi inapezeka kuti ilowe mu court. Atsikana onse aja kukhala ngati anali zigoba za a police kuti azimuchotsa ndalama mtumiki wa Mulungu.

2. Evidence yawo imakhala yoti wakuti anati mwakuti ndipo anamva kwa wakuti yemwe akutinso wakutiyo ankati mwakuti. Kungochuluka ma mwakuti ndi wakuti popanda cheni cheni chogwirika - khoti lati ndi hearsay.

3. Ambiri ogwira ntchito ku police amene amalenga milandu ya Bushiri kuti azimudyera ndalama anachotsedwa ntchito pa nkhani za corruption ku milandu ina ku South Africa komko.

Tikunena pano, Bushiri atha kuyimira u MP atafuna. Ndi freeman. Apapa akuyenera kupangitsa crusade ku South Africa konko title yake: "Mundimva manyi aphwanga ndipo mudziwanso.

ADMIN WAKU MZUZU
b287

🤖 ROBOTI YAGWIDWA KU GERMANYApolisi ku Cologne, Germany, agwira roboti yofiira ndi golide ya 120cm popeza idagwira matak...
14/10/2026

🤖 ROBOTI YAGWIDWA KU GERMANY

Apolisi ku Cologne, Germany, agwira roboti yofiira ndi golide ya 120cm popeza idagwira matako a mtsikana wazaka 16 komanso kuchita mayendedwe osonyeza zachiwerewere kwa iye.

Achinyamata awiri azaka 16 ndi 19 akufufuzidwa pa nkhaniyi. Apolisi atenganso mafoni awo kuti afufuze ngati roboti inalamulidwa ndi munthu kuti ichite zimenezi. Inapezeka mu boot ya galimoto pafupi ndi malo ogulitsira chakudya.

Mneneri wa apolisi Christoph Bermel wati: "Iyi ndi nkhani yatsopano kwa ife.

Gwero: AP News | Oct 13, 2026

Address

Mz
Mzuzu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Umodzi Media posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share