Sir Cossah D

Sir Cossah D You are here for laughingšŸ˜‚, Sir Cossah d is afroDancehall/content creator Entertainment ,,,blackchild straight away from Tengani ghetto empire, Nsanje?

timadziwa kuti munthu wamulungu sangangoyang'ana,, Zomwe wapanga Bushiri Ambuye apitilize kumudalitsašŸ™Zikuchitika pompan...
16/06/2026

timadziwa kuti munthu wamulungu sangangoyang'ana,, Zomwe wapanga Bushiri Ambuye apitilize kumudalitsašŸ™

Zikuchitika pompano Prophet Shepherd Bushiri walengeza madzulo uno kuti akupanga madongosolo a ma bus okwana 10 kuti akatenge amalawi omwe akuthamangitsidwa ku South Africa mwachipongwe,

Pali akazi ena akati akukonde wekha nkumadabwa kuti munthuyi alidi serious koma,, Baby daddy. šŸ„ŗā¤ļø
16/06/2026

Pali akazi ena akati akukonde wekha nkumadabwa kuti munthuyi alidi serious koma,, Baby daddy. šŸ„ŗā¤ļø

Sir kodi amuna ena ndi osalira kwambiri eti!!andithamangisa kubanja eti ndinapanga post Pic ndili ndi X wanga komanso si...
16/06/2026

Sir kodi amuna ena ndi osalira kwambiri eti!!

andithamangisa kubanja eti ndinapanga post Pic ndili ndi X wanga komanso sinakambepo zachikondi, anali ndi Birthday ndie tili pachibwenzi timakonda ma out kwambiri ndipo timakonda kupita Malo ngati kubala kumajambula tikumwa zokumwa zabwino!!

ndie dzulo ndapanga post Yoti_Happy birthday Old dearly pano mwakula lekani kumadya kwambiri muma out, koma kale lathu timanjoya kwambiri koma chomwe chinkandibhowa ndi chimodzi ukaledzela iweyo umandipengesa kwambiri usiku onse umafuna kuti uzigona pamwamba panga, koma apapa Kaya ukupitilizabe zako zopepela zija!!

eti mpaka wakwiya nazo eti mpaka kundimenya ati ndine hule ndipo sakufuna kukhala nane banja, kodi apapa Pali nkhani yolakwika kodi, munthu oti anakwatila nane ndinakwatidwa munthu mpaka ungakwiye ndizapa Facebook zoona, koma anyamata enawa?

16/06/2026

zafika poti anyamata awawa akazangofika ndi moyo kuno ku Malawi azaswa mbama wina wake,,

chifukwa anthu awa ndie akuvutika osati masewela Pena Boma ya Malawi muzikhala serious awa ndi Amalawi ngati ena omwe mumawathamangila kuwathandiza akagweledwa vuto, azimayi akubeleka pa mbalambanda ndikuzizilaku ndie Ena ali ndi ana ang'ono, ndie chonde kubomako?

ichi ndie timati chikondi cheni cheni, moti azimayi ena aku Malawi kuno simungapange zomwe wapanga mmayi uyu wa dziko la...
16/06/2026

ichi ndie timati chikondi cheni cheni, moti azimayi ena aku Malawi kuno simungapange zomwe wapanga mmayi uyu wa dziko la South Africa azimayi aku Malawi sachedwa kuituluka unva ndifele chikondi ine!!

Mayi wina wa ku South Africa wasankha kukhala limodzi ndi chibwenzi chake cha ku Malawi ku Sherwood ngakhale akukumana ndi mavuto. Mayiyu akuti mwamuna wa ku South Africa anamusiya ali ndi ana atatu komanso mavuto a moyo, koma bambo wa ku Malawi ndi amene anamuthandiza, kusamalira ana ake komanso kumulimbikitsa pa nthawi yovuta.

Chifukwa cha chikondi ndi kukhulupirika komwe wamuwonetsa, mayiyu akuti sangamusiye pa nthawi yomwe akukumana ndi mavuto. Iye wanenanso kuti akukonzekera kusamukira ku Malawi kuti apitirize moyo wawo limodzi.

Nkhaniyi yadzetsa maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya chikondi, kukhulupirika, komanso ubale wa anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Anthu ambiri akudzifunsa ngati kukhulupirika kwa munthu n’kofunika kuposa dziko limene amachokera.

KUNGOTI A MALAWI PENAPAKE NDI ANTHU ODABWISA KWAMBIRI SIZIKUMVETSETSEKA OR NDI PANG’ONO.Boma lathu lidakayamba layimitsa...
16/06/2026

KUNGOTI A MALAWI PENAPAKE NDI ANTHU ODABWISA KWAMBIRI SIZIKUMVETSETSEKA OR NDI PANG’ONO.

Boma lathu lidakayamba layimitsa kaye Kuti Anthu Ku theba asamapite kukagwira ntchito kwa chaka chino.

Zinthu pa theba pano sizili bwino koma daily anthu akulowa be.

Bola likudzatuta Anthu othawa ziwawa Ku theba kuno ndi ma bus 10,
Pomwe daily almost ma bus 4 kapena 6 akutuluka mmalawi ndi kumabwera Ku theba.

Zimenezo sizikupanga sense or Ndi pang’ono...

Anthu omwe akubwera theba wa, adzangofikila mmavuto ndi kumafunanso thandizo la boma,
Bwanji nanga bomalo osachita po kanthu before it's too late...

Anthu ku theba kuno akuvutika.
Ma guys ku malawi ko dziwani zimenezo...

PLZ imitsani Ma program anu obwera theba wo kaye...

Theba wawola uyu..
Apolice ayamba kuyenda door to door,
Zinthu zaima nawonso ma landlord akukana Ndalama Ya rent akuopa kugumulidwa Ma nyumba awo.
Mabwana nawo akuopa kulipira chindaputsa Cha 100 thousand Rand.

Ndiye wina kumabwera be....
Kaya...

ati apa kuzinva udolo kwambiri kumati amalawi ambiri akabwela ku south Africa amawoneka bwino koma akapita ku Malawi uma...
16/06/2026

ati apa kuzinva udolo kwambiri kumati amalawi ambiri akabwela ku south Africa amawoneka bwino koma akapita ku Malawi umangowoneka ngati osanduka,, uyuyu anthu akumpasa matama kwambiri kuteleku nkati mwamtima mwakemo mukungoyenda Malawi basi!!

amalawi salimbana ndi munthu sono chomatipangila post yomatigemula ndichani?

uyu ndi waluso oti or atakhala ndi Malawi wabwino athakukhala monthu owopsa kwambiri,,ndi Producer, Amaimba, amathanso k...
16/06/2026

uyu ndi waluso oti or atakhala ndi Malawi wabwino athakukhala monthu owopsa kwambiri,,

ndi Producer, Amaimba, amathanso kulumikiza zitsulo zakale kubwela Galimoto yabwino kudzera munzeru zake, amathanso kumanga Nyumba ndi kuika denga, or ndewu amatha kumenya bwino bwino koma vuto tina chulukidwa ndi Satanic yomwe ikusokoneza anthu abwino komanso amaimbidwe abwino tisamawadziwe kuno ku Malawi!!

uyu ndi Dj Lome limited made, omwe ambiri tinkayembekezela kuti Kumwalira kwa Malemu Katelele Ching'oma akanatha kukhala Mlowa m'Malo ndi nkuluyi Chifukwa amatha kupanga compose music pena osamanveka ngati Nsena ndi oimba ambiri akhala akumuyendela yendelapo ngati Skeffa Chimoto, George Kafodya, Phungu Josephy Nkasa koma still more sananvekepobe ngati oimba waku Malawi!

so izi ndalemba kupangila kwa anthu anzeru zopusa omwe amazinva kupanga manage oimba koma ali makape, kunsanje kulibe artist angatchuke chifukwa cha mphanvu ya management pokha pokha akhele female artist mwina,

ndie Pali ka munthu kena kake kopanda dzina komwe kakufuna kupanga dzina ndi artist mu mbiri yake tikuyidziwa ndipo akhala akuvutika kwambiri kumapempha sponsor mpaka lero anapanga kumbari yake ndie wina angobwela kufuna kumusokonezanso, Asena Kaya chimakhala chani kukhomelerana chonchi!

tiyeni timufunile zabwino nkuluyi kuti naye ku mbari yake akhale dolo ku Lowershire please?

16/06/2026

kwa yekhawo amatha kuimba nkhani ndi iyiyi iyi ndinyimbo yolimbikisa aliyense akuzikaikila mavuto sikutha kwa moyo?

koma Amalawi inuyo anakonza!!ena ayamba kuyankhula akuti mesa awa ndi aja ankafuna kuimila u purezidenti, ndie bwanji an...
16/06/2026

koma Amalawi inuyo anakonza!!

ena ayamba kuyankhula akuti mesa awa ndi aja ankafuna kuimila u purezidenti, ndie bwanji angoti ziii, mu nthawi ya amalawi ambiri akupeza mavuto ku south Africa, sakukhosomola nkomwe pamene Purezidenti wachipani cha UDF Atupele Muluzi wakhudzika ndi kuthandiza AMalawi Dr. Michael Usi tiziti sakunva kanthu!

ndie munthawi ya ndale azizabwela ngati dolo kwambiri uyu tizankoza tokha tikangofika ku malawiko, ndipo anthu sakudziwa kuti mavoti ambiri amachokela ku south Africa, komanso a Boma ndi lomweri anthu oti munakhalapo m'boma ndipo mumati muzabweleranso anthu amene mukuyembekezela kuti azakuvoteleninso ndi ati,apa muli zii anthu oipa inu kodi Atupele ndie kuti ndi yekhayo omwe amakonda AMalawi mwama Purezidenti onse opanga nawo za Ndale kuno ku Malawi!

Amalawi akuwona okha apapa?

Address

Tengani
4670

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Sir Cossah D posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category