21/05/2026
Mnyamata wazaka 18 dzina lake Narendra Kumar wa ku India anathamangira kuchipatala atayamba kuchepa kwambiri thupi.
Madokotala anadabwa kwambiri atamuyeza ndipo anapeza kuti mkati mwa thupi lake munali mapasa otchedwa parasitic twin, omwe anali ndi mano komanso tsitsi.
Mapasawo anasiya kukula ali akadali m’mimba mwa mayi awo ndipo anakhalabe mkati mwa thupi la Narendra kwa zaka zonse 18.