Salic Mv

Salic Mv POET & MUSICIAN
+265888172112
0999931621

30/12/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Kris Tine, Walusungu Ziba

30/12/2025

usadzayerekeze kukwatira mitala mwanawe๐Ÿ˜ณ๐Ÿ˜…๐Ÿ˜…

Pomwe tikudikira album ya Florence Lucy Msukwa & Salic Mv. Kabukhu aka kali mu process ya publication, book cover alread...
14/05/2025

Pomwe tikudikira album ya Florence Lucy Msukwa & Salic Mv. Kabukhu aka kali mu process ya publication, book cover already done, with 10 pages , muli ndakatulo za chizungu and Chichewa, get ready, this is history making๐Ÿ”ฅ๐Ÿ‡ฒ๐Ÿ‡ผ๐Ÿ™

14/05/2025

With Mikozi โ€“ I just earned their Eni mudzi badge!

23/04/2025

Ndakatulo ija yatulukatu ๐Ÿ˜‚๐Ÿ™Œ, PrPretty Nana's creativesNdi SaSalic Mvumulilira Chauta๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚link in comment section ๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡

MONI ! MONI ! Tiyeni tiwerenge nthanoyi modekha mpaka kumapeto โœ๏ธWolemba โœ๏ธSalic MvPADANGOKHALA!! Ndikhulupilira nonse m...
17/04/2025

MONI ! MONI ! Tiyeni tiwerenge nthanoyi modekha mpaka kumapeto โœ๏ธ

Wolemba โœ๏ธSalic Mv
PADANGOKHALA!! Ndikhulupilira nonse mwati "Tilitonse๐Ÿ˜๐Ÿ˜๐Ÿค

Panali banja lina lomwe linkasowekera mphatso yamwana ndipo ili linali vuto lalikulu m'banjamu. Tsiku lina atakhala pansi nalingalira choyenera kuchita anaganiza zopita kwa owombeza ula (sing'anga wa zitsamba)

Ulendo wopita kwa ng'angayo udatheka ndipo anakampezadi watsengayo. Ndieno sing'angayo atamva za vuto lawolo anawauza kuti abwerele kunyumba nakabwerenso tsiku lina koma akabweletse zifuyo zitatu.

Anthu aja anabweleradi kunyumba kwawo ndipo tsiku louzidwalo anatenga galu, mphaka, ndi tambala. Atafika kwa ng'angayo adapereka ziwetozo ndipo ng'angayo idakazitsekera mu kanyumba komata nanenelera ndi mankhwala. Kenako anawauza kuti pakadutsa maora atatu apite natsekure mukanyumbako ndipo chomwe achipezecho nchomwe iwo angakatengemo. Nthawi itakwana anakatsekuladi nakapezamo ana okongola atatu, wamkazi ndi amuna awiri, ndipo anatenga anawo nakawalera kufikira aliyense anapeza banja.
Tsiku lina anaganiza zowayendera anawo aliyense payekha ndipo
anayamba kupita Kwa wamkaziyo . Akutsanzika kuti azipita mwamuna wa mwanayo anadandaulira makolowo kuti vuto la mkazacheyo linali loti akamapita kogona iye akumathamangitsa makoswe kuti awachite ndiwo.

Anapitaso Kwa mwana wina wamwamuna nakamvaso kuti mkazi wakeyo akamuikira chakudya mmbale akumagwetsera pansi namadya zotoleza. Anapitaso Kwa mwana wachitatu nakamvaso kuti mwamunayo akumakagona kuzibwenzi kumusiya mkaziyo pakhomopo. Izi zinawapatsa maganizo makolowo kuti anawo nkuthekha anangotenga matupi aumunthu wokha koma mitima inali ya ziweto zija.

PHUNZIRO
Munthu atha kusintha maonekedwe ndi mavalidwe komano mpovutirapo kuti munthu asinthe mtima komaso khalidwe. Ndieno tisanawakonde abwenzi Tiyeni tiwafufuze kae kuti mbiri yamoyo wawo ndiyotani kuchitira pamawa zingazadzetse mavuto ena.
ZIKOMO ๐Ÿ™๐Ÿ™๐Ÿ™

MONI,! MONI ! Tiyeni tiwerenge nthanoyi modekha mpakana kumapeto, ndipo osaiwala kupanga like nthanoyi โœ๏ธ๐Ÿ™๐Ÿ™Wolemba โœ๏ธ Sa...
17/04/2025

MONI,! MONI ! Tiyeni tiwerenge nthanoyi modekha mpakana kumapeto, ndipo osaiwala kupanga like nthanoyi โœ๏ธ๐Ÿ™๐Ÿ™

Wolemba โœ๏ธ Salic Mv
PADANGOKHALA! Ndikhulupilira nonse mwanena kuti TILITONSE ๐Ÿ˜๐Ÿ˜

Mkulu wina ulova utamutikita anakonza ulendo wopita dziko lakunja kukasaka maganyu. Ndipo atakafika mwamwayi ntchito anayipeza ntchito kwa mzungu wina wolumala manja namagwira ntchitoyo mokhulupilika. Bwiana wachizunguyo anamkondetsetsa munthuyo mpaka zinafika paja pomamupatsa makiyi a sefa ya ndalama kuti azitha kutengamo mwaufulu ndalama yogulira zakudya zamnyumbamo.

Poti munthu ndi munthu umathabe kuyendeledwa ndi kachiwanda kena kofuna kuba maganizo odzachotsa ndalama nkuthawa anayamba kumubwelera. Naye mzunguyo anaganizabe zoti tsiku lina adzamudzidzimutse ndi chozizwa mkuluyo ngati mphatso yomuthokozera . Ndieno bwanayo anakonza ulendo wopita kwao kudziko Lina kuti akadyere tchuthi chawo.

Anamuitana mkuluyo namuuza zaulendowo ndipo anamulonjeza kuti akabwerako adzampatsa mphatso yamtengo wapatali Bola asamalire bwino nyumbayo. Ndieno atapita bwanayo kwao mkuluyo analingalira zotsekura sefa la ndalamalo nkuthawa kubwelera kwao. Atafufuza komwe kunali ma kiyi sanawapeze ndipo anangothyola sefayo nachotsa chuma chochuluka nkusiyamo kandalama kochepa. Anakasungitsa Kwa mzake yemwe ankamudalira chumacho. Mwatsoka kwamzake kuja kunabweraso mbala naba ndalama zonse nkumukhapa mzakeyo namsiya ndi mabala. Ndieno anakumbukirabe za mphatso anamulonjeza bwana ija ndipo anaganiza zowadikirira kuti mwina nkudzapezabe pozitonthozera.

Patatha masabata awiri mzungu uja anamuimbira lamya mkuluyo kuti sabwelera msanga kunyumbako pazifukwa zina. Anamuuzaso kuti mphatso anamulonjeza ija apite kuchipinda, atsekure mu kachitini atenge makiyi a sefa, kenako atsekure sefayo nkutenga ndalama yonse yamkatimo kukhala yake. Nkhaniyi inavuta maka poganizira zoti ndalama ija inali itachotsedwamo kale nakaibetsa Kwa mzake.

PHUNZIRO
Mulungu anapatsa kale mphatso zina komano mmalo modekha kudik

17/04/2025

With Tamia ja โ€“ I'm on a streak! I've been a top fan for 3 months in a row. ๐ŸŽ‰

30/03/2025

PLAN YA LEZA officially out ๐Ÿ”ฅ๐Ÿ˜‚ link in comment section ๐Ÿ‘‡๐Ÿ‘‡

On Saturday, I will release my gospel poem PLAN YA LEZA, Pamene tikukumbukira mazunzo a Yesu khristu pamtanda๐Ÿ™
26/03/2025

On Saturday, I will release my gospel poem PLAN YA LEZA, Pamene tikukumbukira mazunzo a Yesu khristu pamtanda๐Ÿ™

Address

Mzuzu

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Salic Mv posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category