08/03/2025
Wakumudzi ndiye
Wodziwa kuphika denje mchilimwe
Wokhathamitsa mmalankhulidwe ake
Weee bambo kuli kundinyadila
Atamvala duku mododometsa
Chilindikhambi chadodometsa mleme
Akuulayawa afuna zanoninoni
Mwamuma aligone mwathu n'ndiwo
Bemberezi adziwa yake nyumba
Wakumudzi ndiye
N'pita kwa anga malume
Andipezele kodziwa chidulo
Kokonola pamanja osati zaulesizi
Kakuyimba nyimbo zozuna kuti zuuu
Kakunyivulira mochititsa Kaso
Osati ndwii ngati wadya tsabola
Wakumudzi ndiye
Wodziwa khasu ngati ine mwini
Chala chimodzi sichiswa nsabwe
Ndekha ndalema
Ndikapeza kuti kakumudzika?
Akuulayawa achulukila poti
Bea poitana ine khambi zindichititsa
Koma weee bambo ndiko ndifuna
Wakumudzi ndiye ( by griffin nkhata)