J. NICE super stories

J. NICE  super stories Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from J. NICE super stories, Arts and entertainment, 0999266106, Lilongwe.

12/07/2023
16/05/2023

Ndiyambe ndikupepesa kuti ndinasowa pakatipa koma ndabwera ndithu ndipo simukhumudwa and chosangalasa ndichakuti pompano ndikhala ndikukupatsirani nkhani yatsopano ndipo mutu wake CRAZY SCANDALS. Ndipo muyikonda kwambiri nkhani imeneyi, mongokudziwitsani major character is FRANK ABUJALIH and some of minor characters but is not mention all names on this post.
Ndimakukondani nonse omwe mumatsatira nkhani zanga ku J. NICE SUPER stories and Ku BENGO NDI ZAYAKUNKHONGO.koma osaiwala kupanga like page imeneyi ya J. NICE SUPER Stories kuti nkhani zathu zisamakuphonyeni. Mwakoma nonse๐Ÿ™๐Ÿ™๐Ÿ™๐Ÿ™

31/01/2023

LOVE IS ALINK part 1

Poyamba pangani like page ya J. Nice super stories kuti muzilandira nkhani zotchakulidwa bwino komanso zophunzitsa.

Amayi dikirani ndikufotokozereni zokhudza Love. Love ndinzanga chabe koma anthu akamationa amangoona ngati tili mchikondi koma kunena chilungamo Love timangocheza chabe. Uku kunali kucheza kwa mayi ndi mwana.

Pamudzi wa chinsikwa padali banja lina lomwe limachita bwino pa nkhani yaza ulimi.Banjali limadziwika ndi dzina lakuti chidothi. Achidothi adali abambo ambanjali ndipo amayi amatchulidwa kuti anasibeko. Banjali linadalitsidwa ndi ana atatu. Atsikana awiri ndi nyamata mmodzi. Ndipo mayina anawa adali motere, oyamba adali Limbani, wachiwiri adali chimwemwe ndipo omaliza adali madalitso.

Limbani adali mnyamata wanzeru komanso olimbikira pa nkhani yazamaphunziro. Iye adali kuwalimbikitsanso anzake omwe amaphuzira nawo sukulu imodzi yomwe imatchulidwa kuti mdzobwe primary school. Sukuluyi idali ndi aziphunzitsi odzipereka pa ntchito yawo ndipo iwo samalora kuti mwana azipanga masewera pasukuluyi. Iwo amaonetsetsa kuti ana akuphunzira mokwana komanso anawo akuchitabwino. Chomcho izi zidapangitsa kuti sukuluyi izitumiza ana ochulu kuma secondary school odziwika bwino mdziko muno.

Limbani atafika standard 8.adasankhidwa kukhala otsogolera ana anzake ( head boy) wapasukuyi chifukwa iye ndiyemwenso amakhala nambala 1 potsogolera mkalasi yawo. Izi zidamupangitsa limbani kukhala ndi chikondi kwa wina aliyense wapasukulupo ngakhalenso akakhala kunyumba amapanga zinthu zokomera makolo komanso azibale ake.

Tsiku lina limbani ataweluka ku sukulu. Adauyatsa ulendo opita kunyumba, alimkati moyenda adamva kuyitana kuchokera kumbuyo kwake ndipo adati, Limbani!! Limbani! Awa adali mawu achitsikana. Limbani atamva mawuwo adayima ndipo atatembenuka kumbuyo adawona kuti adali Loveness yemwemso adali mkalasi limodzi. Ndipo limbani adali odabwitsika powona loveness akusiya msewu wa kwawo kumulondola Limbani. Loveness atafika adati:koma abale zoona mose ndayambira kukuyitanani koma osandiyankha. Mose ndayambira kukuthamangira koma osandiyang'anako kapena mwina ndidakulakwira chinachake? Kapena sindine oyenera kuti ndizicheza nawe? Chonde ndiuzeni mwina ndipepeseletu. Ndipo Limbani adakhala phee! Kusinkhasinkha zoti amuyankhe Loveness popeza adamufusa mafuso ochuluka pakamodzi. Ndipo limbani sadanjenjemere koma kuyankhula kuti adziwe zoti iye adali katakwe pa nkhani ya zoyankha mafunso, ndipo adamuyankha momufusanso ndipo adafunsa kuti kodi Love mafuso onse omwe wandipatsawa ukufuna kundiuza kuti ndiyankhe kapena umangofuna kuti ndidziwe? chifukwa olo utakhala kuti ndiwe professor sizingatheke kuti ayankhe mafunso osewa pakamodzi. Ndipo Loveness adati; Limbani umadziwa kuti ndife anthu osiyana kapena umangoona kuti zilibwino bwino tikamakhala chomchi? Pilizi pilizi ndikungofuna undiuze zomwe wabwelera zinazose pambuyo. Okay, Limbani ndikufuna kuti ukhale nzanga chifukwa sindidakuoneko ukucheza ndi atsikana ku sukulu kuja chomcho ndaona kuti iwe ndi ine tiyambe kuchezerana wina ndi nzake choncho tiyambe kuyenderana koma sindikudziwa kuti wazikonda zimenezi? Mmmmmm anyway koma ndiwe nzanga kale kungoti zikhoza kumakhala zovuta kwanbiri kuti anzathu azitiona tikuyenda chomchi amayamba kuganiza zambiri pamene ife tikadali ana, limbani ayankha motero. Loveness adati, Okay chabwino ndakumva. Apa nde basitu tionana mawa ku sukulu. Adatsanzikana motero Limbani ndi Loveness.

Tsiku lina chimwemwe adali ndi Madalitso ku dondo (kunkhalango) Ina yomwe idayandikana ndiku mudzi wawo. Iwo adali akusakasaka nkhuni zophikira ali mkati mosakasa atsikanawa adayamba kukambirana motere :
Chimwemwe :mada umadziwa
kuti makolo athu
amatikonda?
Madalitso :Eya ndimadziwa
Koma ndimadabwa
nthawi zambiri kuti
Bwanji amakonda
Kumuikira kumbuyo
Limbani?
Chimwemwe :amamukonda
Chifukwa mammuna
alipo yekha pakhomo
paja.
Madalitso :owo chabwino basi
Ndadziwa.
Chimwemwe : eeeeetu
achemwali anga.
Kungoti
pali zinthu zina
zikufunika kuti
limbani uja azimukond
a ndicholinga choti
atsogole ndi
maphunziro ake
ndicholinga choti
iyeyo akadzamaliza
maphunziro ake
ndikuyamba bizimizi
kapena ntchito
azidzatilipilira Sukulu
Fizi poti makolowa
amadalira ulimi nde
mkutheka kuti pamene
tizikati tikufika ku
Sekondare makolo
adzakhala asakukolora
ngati zomwe timakolor
a panozi
Mwina atathanso
mphamvu choncho Izi
zidzamukakamiza
Limbani kuti
azidzatilipilira sukulu.
Madalitso :mmmm okay koma
nde makolo athu
adaganiza mwanzerut
u mpaka Limbani
kumadzatisamalira
ngati momwe amayi
ndi adadi amatisamalir
a. eeeeee koma nde
bola adzateroditu
mwina mkudzaonako
Tawuni ya Lilongwe.
Chimwemwe :eya ndipo
Usakayike Limbani
ndiwakhama ndi
sukulu ndipo ifeyo
tikhala ana
ofewa chifukwa
chamchimwene uja
moti tizingowayikiza
mmapemphero kuti
ziziwayendera
Kusukulu.
Madalitso : eya koma ndikuona
Kuti nthawi yathatu iyi
bwanji tiyambepo
kumanga mitolo kuti
makolo akamabwera
akapezeko nsima
chifukwa akhala
atatopa.
Chimwemwe : waganiza bwino
tiyeko tikayang'ane
Luzi kapena mitsitsi
apo yoti timangire
nkhunizi.
Madalitso :OK chabwino.

Ataliza zonse zomwe amachita zija adanyamuka ulendo wakumudzi mwanthawi zonse amati akafika kunyumba atsikana aja amathandizana ntchito zonse zapakhomo.

Nthawi yamayeso itayandikira Loveness ndi Limbani ubale wawo udali waukulu kwambiri ngakhale kuti ana asulukulu anzawo amawanena kuti adali mchikondi chosaneneka koma iwo samazitengera ngakhalenso kuti aphinzitsi amawakayikira kuti pakati pawo china chake chikuchitika koma iwo adali kukana kuti palibe mgwirizano oyipa pakati pawo. Ndipo nkhaniyi idawapezanso makolo ake Limbani komanso a Loveness. Izi zidapangitsa bambo ake alimbani kukhala mkwiyo oopsa Kwambiri ndipo ataweluka limbani adamuyitana
ndikuyamba kumufunsa amvekere.

Tikumanenso mu part 2.poyamba pangani like J nice super stories kuti nkhani zathu zisamakuphonyeni. Mwakoma nonse๐Ÿ’“โค

Address

0999266106
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when J. NICE super stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share