Achinangolo entertainment

Achinangolo entertainment 👌💯TALENT PROMOTER 🚀💫 ENTERTAIN 💯🙋‍♀️ REMINDER💬🔔EDUCATOR📒OPEN TALKS TO EVERYONE ✏ INDEPENDENT BRAND✅🎧 Smart master

Akuluakulu oyang'ana za mpira m'boma la Dedza lero anali pa Kanyenda, kukhazikisa Kanyenda zoni. kumeneko mwa Zina kunal...
19/06/2026

Akuluakulu oyang'ana za mpira m'boma la Dedza lero anali pa Kanyenda, kukhazikisa Kanyenda zoni. kumeneko mwa Zina kunali kusankha adindo monga Chairman, GS, Treasure komanso ma committee members okwana 6

Awa ndi anthu amene aziyendesa chilichonse chokhuzana ndi mpira ku zone imeneyi, izi zikuthanthauza kuti from KASUMBU to NAKAONA omwe aziyang'anila mpira ndi iwo

Mwa Zina osankhidwawa apasidwa mwayi oti azitha kufikira ma bwana omwe ali ndi chidwi chofuna kutukula ma sewelo kudera limeneli, iwo awuzidwanso kuti pachilichonse chomwe chitika akuyenela kumasamala malamulo a mpira

iwo ati akufunitsitsa kuti team yomwe izichita bwino kuzone izikhala ndi mwayi okakumana ndi ina kuchokera ku zone ina, ndipo ikapitilira izita kukamananso ndi ina mpaka kukafika kumtunda.

Kuwonjezera apo achenjeza ma team onse amene azinyanyala ndikuluka mground kuti azikhala kuti aluza or zitakhala kuti amatsogola ndi zigoli 10. mmalo mwake ati ngati team ili ndi dandawulo izipeleka madando ake kwa omwe akuyang'anira game ndipo masewelo azipitilira. zambili zili mu audio yomwe tiyituluse posachedwapa STAY TURNED

19/06/2026

NDEMBO YAKANA CHIGAMULA CHA A GROUND AMADZUMBI.

Mpira utathera pa njira pakati pa NZOOLA nd NDEMBO akuluakulu a league ndikuwunikira anapeza kuti team yomwe yawina ndi NDEMBO ndipo inayikidwa pa mndanda wa ma team 4 omaliza

koma semifinals imeneyi yakhala isakuseweledwa pa zifukwa zina mpaka panafika poti ma team 4 agawane ndalama

Kwinaku NZOOLA itakatenga chiletso kwa a group amadzumbi, ndiye dzulo a madzumbi anayyitanisa mbali zonse zokhuzidwa kuti akamvele momwe zinayendera. ndipo pamapeto pake anagamula kuti Game iseweledwenso

Koma malingana ndi captain wa Ndembo wati team yake yavomeleza kugonja ndipo sikasewela game yachibwelezayo.

apa tikudikira chigamulo China kwa oyendesa league kuti ati chani
VN BY ALUKI ALANI NDEMBO FC CAPTAIN

19/06/2026

Good morning and JUMMAH MUBARAK

18/06/2026

Zimapweka sizanakupeze Achinangolo khalani osamala kumeneko please. ngati mpata ulipo sunthani it's not end of everything

16/06/2026

Kwa inu anzathu amene kuchoka ku malawi kulowa nziko la South Africa mukafika kuno choyambilira kupanga ndi ma papela okuyenelezani

Ambili tikupita kumudzi chifukwa tinayamba ndikupanga focus za mavuto omwe tinawasiya osaganizira za ma pepala

kodi mungapeze bwanji pepala pamudzi pano?
Pepala limakhala lopweka kupanga mu nthawi imene wangolowa kumene mdziko muno passport yako ikadali ndi ma tsiku. iyi ndi nthawi imene imakhala yabwino chifukwa umayenda mofewa, koma vuto ndi loti timakhala tilibe ndalama

Ukangolowa ndi passport muno umapasidwa ma tsiku ena amkhala 30 days matsiku awa ata kukupezesani Weiver imene mtengo wake ndi R1600 ndipo kumeneko amakupasa slip tsiku lomwelo yomwe imakuthandiza paliponse pomadikira kuti waiver ituluke

Tikakamba za tax number iyi ndiye ndi ulele umatha kupanga or pa online wekha Bola ukhale kuti umamva chizungu kupewa kuzibalalitsa kapena kupita ku ma office a SARS uku umafunika ukhale ndi Bank statement imene imakuyimirila ngati proof of residence. kapena kukatenga proof of residence kupolice station mwa ulele

Kuphuzira sikumatha by

15/06/2026

Tikumva uthenga wa malilo Asidi akulu awu achina Afalu pa Dedza boma

Anachitidwa chipongwe dzana pamene amachokera ku business, ndipo anatengeledwa ku chipatala koma lero atisiya
INNALILLAH WA INNA ILAYH RAJIUNA

Sambano achangwa business syelesi ikuti ikuti uli🙆‍♀️
15/06/2026

Sambano achangwa business syelesi ikuti ikuti uli🙆‍♀️

15/06/2026

Ku cape town ma bus onyamuka mwezi uno sakupezeka onse adzadza ma bus omwe akupezeka ndi onyamuka pa 14 July

koma Pali ka gulu kena ka anthu omwe akusonkhelana ma R2200 kuti ayitanise bus kuchoka Johannesburg kuti izawatenge azipita ku ma malawi.

please kumene muliko ndibwino kumafufuza mayendedwe sizanafike pakhosi, ngati muli mu shop ndipbwino kudziwa zomwe zikuchitika kunja sithu zitha kusintha enytime ma Ethiopia ali ndi njira zawo please be safe Achinangolo

15/06/2026

Inde business ili ma strategies komanso timing komano anzathu ama bus ndi ma transporters mukanakhala ndi Umuthu please. simungakweze mitengo mu nyengo ino yomwe amalawi ambili sakugwira ntchito

Mitengo ikanakhala ya Last week ija anthu ambili si bwezi akudikila ma bus a boma komano chifukwa choti mwaona kuti ambili akhuzidwa ndi mavuto mwayamba ku kweza mitengo come on guys anthu sakupangila kukodwa izi wallah.

Ana oposela 300 ndi omwe akupanga ma phuzilo awo pa KANYENDA MADRASSOR Kutsatila kumangidwa kwa zipinda za tsopano zophu...
14/06/2026

Ana oposela 300 ndi omwe akupanga ma phuzilo awo pa KANYENDA MADRASSOR

Kutsatila kumangidwa kwa zipinda za tsopano zophuzirila, zapeleka chidwi komanso chilimbikiso kwa makolo ambili pomwe zikuwonesa kuti Ana ayamba kukhala serious nd ma phuzirowa

Akulu akulu a Committee yoyendesa ma program pa mzikitipa ati ndi udindo wa kholo lililonse kuwonesetsa kuti mwana wake akupita ku madrassor komanso makolo apemphedwa kuti akuyenera kuwagulira Ana awo zitabu kuyambila a part 1 mpaka 4 kuti alinse azikhala ndi mwayi okawelenga akaweluka ku madrassor

Ana mmudzimu sakuloledwa kupita ku ma show kapena kuyenda yenda ngati nthawi ya class yakwana ndipo Bambo CHEKOLA kapena kuti ODI UMALI ndi gulu lawo ndi omwe akuthandizila kukangila Ana ku maphuzilowa ndipo akumayenda ndi chikwapu mmanja kusaka Ana mnakomo ndi mma show views

Together we can build KANYENDA
-development
-youth-Organization

Address

Dedza

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Achinangolo entertainment posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share