24/09/2026
Nthano
Bambo wina anakagula galimoto atafikanayo panyumba anatsika ndikukalowa nyumba
mwana wa zaka 7 anathamanga kukayizungulila galimotoyija
Mwanayo anali ndi cholembela mmanja akusekelela
Anayima ndikuyilemba galimotoija mau oti
ILOVE YOU DAD
Bambo anamuonela pawindo lamunyumba mwanauja akulemba
Bambo anakwiya kwambili ukulemba ngalimoto yanyuwani
Ndikutenga chitsulo kumutenga mwana uja ndikukamutsamilitsa zalazakezija pamwala ndikuzimenya zala zija ndichitsulo chija
Mwana analilamosweka mtima
Mai atava malilidwe amwana anathamanga kudzaona zalaza mwana
Zaonongekelatu
Mai anathamanganaye kuchipatala
Achipatala anamuthandiza pomumanga bandechi
Nawagoneka kuti adzimuonela pafupi
Patatha tsiku limodzi Bambo anapita kuchipatala kuti akamuone mwanawao
Mwana amafunsa funso ( Dad ineyo zala zangazi ndichila liti ? )Anangoti posachedwa
Mmawa watsiku lachiwili anawafunsonso funso lomwelija
( Dad ineyo zala zangazi ndichila liti ? Anangomu uzaso kuti posachedwa uchila )
Patatha tsiku lachitatu adokotala anabwela nadzaonazala zamwana
Anaonakuti zinaonongeka kwambili sizichila chofunika ndikuzidula Basi
Mwana anamudula zala
Atabwela abambo wake kudzamuona anawafunsa funso limene linalinso kulankhula komaliza ndimwana uja
Mwana amafunsa kuti
(
Adad zala zangazino zimela liti ? )
Bambo anayamba kulila natuluka panja misonzi ili mmaso anaganixa kuti apite akawone pomwe mwana uja ankalemba anapeza palembedwa mau oti
( ILOVE YOU. DAD
Mowawidwa ntima anatenga ma kiyi angalimoto ndikulowa ngalimoto nayendetsa kupita kutali atafika pa njila pantengo wina amatulutsa zingwe nazikolekela kudzimangilila Bamboyo nafa pomwepo
Thano yathu ikutiphuzitsa chiyani mmoyo mathu
Nanga mwana Uyu akuti phuzitsa nji ifeyo
Mulungu atithandize kukhala oleza mtima ngakhale takumana ndi nyengo zowawitsa mmoyo mwathu
Tisakhale ofulumiza kukwiya tisanave kapena kuona polakwikapo
Mulungu akadalitseni.