Vindicator De poet

Vindicator De poet AUTHOR AND POETπŸ••
(2026 Direction is better than speed) 😭πŸ˜₯πŸ™


For business: Whatsapp/call 0996143445)
(5)

Kumva zoti Junior Buleya wachitidwa chiwembu zakhala zondikhuza kwambiriπŸ’”πŸ’”πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­Junior Buleya adali mchimwene wawo wa aphu...
13/08/2026

Kumva zoti Junior Buleya wachitidwa chiwembu zakhala zondikhuza kwambiriπŸ’”πŸ’”πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­

Junior Buleya adali mchimwene wawo wa aphunzitsi a Buleya omwe m'mbuyomu adandiphunzisapo std 8.

Mzimu wa Junior uwuse mumtendere. πŸ’”πŸ’”πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­πŸ˜­

Sad newsπŸ’”πŸ’”πŸ’”Brian Banda😭😭😭😭😭
08/08/2026

Sad newsπŸ’”πŸ’”πŸ’”

Brian Banda😭😭😭😭😭

07/08/2026

Ngati mukufuna part time around phalombe, call/whatsapp: 0996143445, Educating your child while maintaining excellence. Born to be teachersπŸ™πŸ™πŸ™

30/07/2026

Somewhere satana wazigalukira yekha, I know that, may he continue to divide πŸ˜‚πŸ˜‚πŸ˜‚πŸ˜ŠπŸ˜ŠπŸ™πŸ™

29/07/2026

Utha kumawona ngati mkwatulo sudafike osadziwa kuti ku Malawi ndi ku gahena kaleπŸ‡²πŸ‡ΌπŸ˜…πŸ˜…πŸ˜…πŸƒπŸƒπŸƒ

27/07/2026

Wadya yekha Chips mu bus then akundifusa pano ndi pat ?
ndangoti Ku GahenaπŸ˜‘πŸ’”πŸ˜Ή

27/07/2026

GOVERNMENT TO RECRUIT 6,000 POLICE OFFICERS THIS YEAR

The Malawi Government has announced plans to recruit 6,000 police officers as part of efforts to strengthen the Malawi Police Service and improve security across the country.

Minister of Homeland Security Peter Mukhito said the recruitment exercise has already been authorized and is expected to increase police presence in communities while helping address growing security challenges nationwide.

Source: The National News paper, dated, Monday, 27 July 2026, Page 3

26/07/2026

AKAMALIZA KUNENA ZOIPA ZANGA BY Vindicator De poet

Akakunong'onezani izo ndidamulakwira,
Pena mwina ndidamuponda phazi,
Nthawi ya kusadziwa Yehovah polekerera.
Akakubwatikani ndi bodza la mnanu
Akafasa kundijeda ndi mijedo ya ndi
Akandisosola ndi miseche.
Dzina langali akalidesa ndi phulusa
Mawu angawa akawasokoneza pomata ndi phula,
Zomwe ndidachita akazikhotesa,
Onga mbatata ya ufa.
Zabwino ndidawachitira akazibisa,
Ndi malaya awo aakulu bwino.
Nakusegulirani khomo la m'nyozo,
Wondidesa ndi kundinyowesa ndi mvula,
Ati zawo zikhale za mchere,
Zanga zikhale za muwawani.
Akamaliza muwanong'oneze,
Asadye wa khwangwala mteza,
Akuuzeninso za mbali yawo,
Poti mulandu samva mbali imodzi,
Mungadzatengepo temberero.
Poti ulenje umasimba wako,
Apempheni akuuzeni zoipa zawo,
Atatha kunditseka ngati wothawidwa,
Ndi ndege pa Airport.
Atamaliza kundisala,
Ngati wodwala khate,
Akatha kunena zoipa zanga.

25/07/2026

GOOD NEWS ❀️

Ophunzira nonse a form 2-4 omwe muli around Namanjerema primary school m'boma la Phalombe ndi nthawi yabwino tsopano kuti mugwiritse ntchito holiday yanu molondola, lembetsani part time yomwe iyambe pa first Monday ya mwezi wa August.

Subjects : All

Registration fee : k1000

Part time fee : k10000/month

For more information call : 0996143445

'Zikakanika kwinako, ife timakonza'

25/07/2026

28 Districts of Malawi by Vindicator De poet

A phalo adagwera mmadzi a mbe
Mmenemo adali kuti achira dzulo
Anthu atawatengera ku Zomba
Komwe dotolo ochoka ku neno
Adasindikiza za kuthyoka kwawo kuti Thyolo
Mu mtsinje adagwerawo.
Koma dzana lake
Tidali titawalangiza kuti,
Asamalimbane ndi ma bra a kumtaya
Angazathere ku chikhwawa
Komwe mula sakapezekako nje
Tidawauzanso asadasamire dzanja,
Kuti ndalama asamangoti mwa
Kumwazamwanza
Koma amayesa tikuwachitira nsanje
Osadziwa ife timkaziwa za pa dowa pano.
Adayesa tikuwauza njira zokhotakhota
Poti tidali alendo akunkhotakota.
Lero wawathawa mkazi wapita ku Lilongwe
Ena ponena angoti hee! Ba walaka izo
Amutcholesa osakhwima mango
Wangoima chi
Kusowa kuti alowera kuti?
Mwina angopita ku dedza
Vuto salima
Awona ngati kadza okha
Dziko likoma ndi wovala zilimbe
Kapena akayese ku nkhatabay
Koma moyo ofuna kukhala karonga
Akamuthamangisira ku kasungu
Mwina uku akadziwa Mulungu
Asadapite ku mchinji
Komwe akamuthamangisa
Ndi mtchisi weniweni
Mwina akayese ku Rumphi
Koma vuto ndi wazimzimba
Akanva Atumbuka akumuuza
Inu achi mutipa mutikomenge lutaninge
Mwina mukayese ku ntchewu.
Pothawa kumeneko Ndimkona aziponyera m'madzimu.
Mavutowa tiponyane patsogolo
Kuti tipewe kuchotsa moyo
Mmenemo ndi momwe adafera a PHALO.

Address

Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Vindicator De poet posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share

Category